Mutu

1Yuda, kapolo wa Yesu Khristu, ndi m’bale wake wa Yakobo, kwa oitanidwawo okondedwa mwa Mulungu1 Atate ndi osungidwa mwa Yesu Khristu: 2Chisomo kwa inu, ndi mtendere, ndi chikondi zichulukire.

3Okondedwa, pogwiritsa khama lonse kukulemberani za chipulumutso chathu cha ife tonse, ndafuIumizidwa kukulemberani pokudandaulirani [inu] mulimbikire mwakhama pa chikhulupiliro choperekedwa kamodzi kwa oyera mtima. 4Pakuti anthu ena anayenda mseri, iwo amene adalembedweratu kale, [anthu] osapembedza, otembenuza chisomo cha Mulungu2 wathu kukhala chisokonezo, ndi kukana Mbuye wathu yekhayo ndi Ambuye Yesu Khristu.

5Koma ine ndikumbukira inu, amene poyamba munadziwa zinthu zonse, kuti Ambuye, pamene anapulumutsa anthu kuchoka mdziko la Aigupto, kachiwiri anaononga iwo amene sanakhulupilire. 6Ndiponso angelo amene sanathe kusunga chikhalidwe chawo choyamba, koma anasiya malo awo okhala, anawasunga m’maunyolo amuyaya pansi pa mdima wa ndiwe yani, kufikira chiweruzo cha tsiku lalikulu; 7monga Sodomu ndi Gomora, ndi mizinda yowazungulira, nachita chigololo cha chisika, chimodzimodzi ndi iwo, ndi kutsata zilakolako zina, akhala pamenepo ngati chitsanzo, kudutsa m’chilango cha moto wamuyaya. 8Komabe momwemo olota amenewanso adetsa thupi, napeputsa umbuye, ndi kulankhula monyozetsa anthu olemekezeka. 9Koma Mikayeli mkulu wa angelo, pamene anakangana ndi mdierekezi potsutsana za thupi la Mose, sanayesere kubweretsa chiweruzo chonyozetsa pa iye, koma anati, Ambuye akudzudzule. 10Koma awa, zinthu zimene sazidziwa, alankhula monyozetsa; komatu monga ngati zinyama zopanda nzeru, azindikira chabe mwa chikhalidwe, mu zinthu zimenezi iwo eni amaonongeka nazo. 11Tsoka kwa iwo! Chifukwa ayenda mnjira ya Kaini, nadzipereka okha mkulakwitsa kwa Balamu pofuna mphoto, naonongeka m’kupanduka kwa Kore. 12Awa ndiwo mawanga m’mapwando anu a chikondi, kudya pamodzi [ndi inu] mopanda mantha, kudziweta okha; mitambo yopanda madzi, yotengeka ndi mphepo; mitengo ya nyengo ya dzinja, yopanda chipatso, yakufa kawiri, yozuka mizu; 13mafunde aukali pa nyanja, kutulutsa thovu la manyazi awo; nyenyezi zoyendayenda, zimene mdima wa ndiwe yani wasungidwira iwo kwamuyaya. 14Ndipo Enoke, wachisanu ndi chiwiri kuchokera pa Adamu, ananeneraponso ku zimenezi, nati, Taonani, Ambuye wabwera pakati pa magulu ochuluka a angelo oyera, 15kudzapereka chiweruzo kwa onse; ndi kuwatsutsa osapembedza onse ntchito zawo zonse za chisapembedzo, zimene anazichita kosapembedza, ndi zinthu zonse zovuta zimene ochimwa osapembedza analankhula motsutsana naye. 16Awa ndiwo ong’ung’uza, odandaula, oyenda mwa zilakolako zawo; ndipo kamwa lawo limalankhula mau otumphukira, oyamikira munthu cholinga apeze cholowa. 17Koma inu, okondedwa, kumbukirani mau olankhulidwa poyamba paja ndi atumwi a Ambuye wathu Yesu Khristu, 18kuti anati kwa inu, Pa nthawi yotsiriza kudzakhala onyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni za kusapembedza. 19Amenewa ndiwo anazipatula [okha], anthu achilengedwe, osakhala naye Mzimu. 20Koma inu, okondedwa, kudzimangilira nokha pa chikhulupiliro chanu choyeretsetsa, kupemphera mwa Mzimu Woyera, 21kuzisunga nokha m’chikondi cha Mulungu3, kudikilira chifundo cha Ambuye wathu Yesu Khristu kufikira moyo wosatha. 22Ndipo ena muchite nawo chifundo, pofuna kusintha zinthu, 23koma ena apulumutseni ndi mantha, kuwakwatula [iwo] kuchoka ku moto; podana ndi chovala chokhala ndi mawanga a kuthupi.

24Koma iye amene ali nako kuthekera kukusungani popanda kukhumudwa, ndi kukukhazikani [inu] kukondwera kopanda banga pamaso pa ulemelero wake, 25kwa Mulungu4 yekhayo Mpulumutsi wathu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu, kukhale ulemelero, ukulu, mphamvu, ndi ulamuliro, kuyambira zisanayambe nthawi zonse, ndi tsopano, ndi kufikira nthawi zonse. Amen.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu