Mutu-2
1Pamenepo ine ndikulangizani, choyambilira pa zonse, kuti mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko achitike chifukwa cha anthu onse; 2pakuti mafumu ndi onse a ulemu wao, kuti tikathe kutsogolera ndi moyo wa chete ndi wodekha m’kuyamika konse komanso mkulemekeza; 3pakuti chimenechi ndi chabwino ndi chovomerezeka pamaso pa Mulungu 1 Mpulumutsi wathu, 4amene afunitsitsa anthu onse apulumutsidwe ndi kubwera ku chidziwitso cha choonadi. 5Pakuti Mulungu2 ndiye m’modzi, ndipo mkhalapakati wa Mulungu3 ndi anthu ndiye munthu m’modzi, Khristu Yesu, 6amene anadzipereka yekha dipo kwa onse, umboni ukaperekedwe mu nthawi zake; 7umene ine ndinasankhidwa wamthenga ndi mtumwi, (ine ndilankhula choonadi, sindinama,) mphunzitsi wa amitundu m’chikhulupiliro ndi m’choonadi.
8Pamenepo ndifunitsitsa kuti anthu apemphere m’malo onse, kukweza manja oyera, popanda mkwiyo ndi makani. 9Momwemonso kuti akazi m’mavalidwe a ulemu ndi kuvala modzilemekeza okha ndi mosamalitsa, osati ndi tsitsi loluka ndi golide, kapena ngale, kapenanso zovala za mtengo wapatali, 10koma, chimene chimapangitsa akazi kuvomereza za kuopa Mulungu4, mu ntchito zabwino. 11Mkazi aphunzire mwa chete ndi kumvera konse; 12Koma sindilola mkazi kuphunzitsa kapena kulamulira mwamuna, komatu akhale chete; 13pakuti Adamu analengedwa koyamba, kenako Hava: 14ndipo Adamu sananyengedwa; koma mkaziyo, atanyengedwa, analowa m’kuchimwa. 15 Koma iye azasungidwira m’kubereka mwana, ngati akhalabe m’chikhulupiliro ndi chikondi ndi chiyero ndi nzeru.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu