Mutu 17
1Ndipo pamene anayenda kudutsa Amfipoli ndi Apoloniya, iwo anafika ku Tesalonika, kumene kunali sunagoge wa Ayuda. 2Ndipo monga mwa chozolowezi cha Paulo iye anapita pakati pawo, ndipo kwa masabata atatu analankhula nawo kuchokera m’malemba, 3natsegula ndi kutsimikizira kuti Khristu anazunzika ndi kuuka kuchoka kwa akufa, ndipo kuti ameneyu ali Khristu, Yesu amene ine ndinalalikira kwa inu. 4Ndipo ena mwa iwo anakhulupilira, ndipo anaziphatika okha kwa Paulo ndi Sila, ndi kwa Ahelene amene anapembedza, khamu lalikulu, ndi akazi akulu osati owerengeka. 5Koma Ayuda pamene anadukidwa ndi nsanje, ndipo anazisonkhanitsira [iwo okha] amuna ena oipa osowa chochita, ndipo pamene anasonkhanitsa khamulo pamodzi, anasonkhedzera mzindawo ku chisokonezo; ndipo anakhamukira kunyumba kwa Yasoni nafuna kuti awatulutsire iwo kunja kwa anthu; 6ndipo pamene sanawapeze iwo, anamkokera Yasoni pamodzi ndi abale ena pamaso pa akulu a mzindawo, nafuula, Anthu awa anasanduliza dziko lapansi ku chisokonezo, afikanso kuno, 7amene Yasoni anawalandira; ndipo onsewa akuchita zosemphana ndi malamulo a Kaisara, ponena kuti, pali mfumu ina, Yesu. 8Ndipo iwowa anasautsa makamu ndi akulu a mzindawo pamene anamva zinthu izi. 9Ndipo pamene analandira chikole kwa Yasoni ndi ena onse, anawamasula iwo. 10Koma nthawi yomweyo abalewo anawachotsa, pakati pa usiku, Paulo ndi Sila kupita ku Bereya; amene, pofika, anapita nalowa m’sunagoge wa Ayuda. 11Ndipotu awa anali mfulu kuposa iwo aku Tesalonika, polandira mau ndi mtima wokonzeka, tsiku ndi tsiku kusanthula mau ngati zinthu zinalidi choncho. 12Pamenepo ambiri mwa iwo anakhulupilira, ndi akazi otchuka a Chihelene komanso amuna osati owerengeka. 13Koma pamene Ayuda ochokera ku Tesalonika anadziwa kuti mau a Mulungu1 analalikidwanso m’Bereya ndi Paulo, iwo anafikanso kumeneko, nautsa makamu. 14Ndipo pamenepo nthawi yomweyo abale anamtumiza Paulo kupita mbali ya kunyanja; koma Sila ndi Timoteyo anakhalabe komweko. 15Koma iwo amene anamperekeza Paulo anafika naye mpaka ku Atene, pamene Paulo amawadikira iwo, mzimu wake unavutika kwambiri poona kuti mzindawo unaperekedwa ku mafano.
16Koma ku Atene, pamene Paulo amawadikira iwo, moyo wake unali wopweteka poona kuti mzindawo uneperekedwa ku mafano.1 17Pomwepo iye anakambirana m’sunagoge ndi Ayuda, ndi iwo amene anali opembedza, ndi m’misika kukambirana tsiku ndi tsiku ndi iwo amene amakumana nawo. 18Komanso ena mwa aku Epikureya ndi Stoiki anthu a nzeru anatsutsana naye. Ndipo ena anati, Kodi wopusa uyu akuti chani? Ndipo ena anati, Uyu akuoneka ngati wolalikira ziwanda zachilendo, chifukwa analalikira [kwa iwo] uthenga wabwino wa Yesu ndi kuuka kwake. 19Ndipo pamene iwo anamgwira [iye] anam’bweretsa ku Areopagi, nanena, Kodi tingadziwe nawo za chiphunzitso ichi chatsopano chimene iwe ukuphunzitsa? 20Pakuti iwe watibweretsera zinthu za chilendo m’makutu mwathu. Pamenepo ife tikufuna utiuze kuti zinthu zimenezi zikutanthauza chiyani. 21Tsopano a Atene onse ndi alendo okhalamo anapereka nthawi yawo kulankhula ndi kumva uthenga. 22Ndipo Paulo pamene anayimilira pakati pa Aeorapagi anati, Atene inu, munjira zonse ndikuona inu mwaperekedwa ku kupembedza chiwanda; 23pakuti, podutsa ndi kuona zinthu zimene muzipembedza, ndapezanso guwa limene linalembedwa, Kwa Mulungu2 wosadziwika. Pamenepo amene mumpembedza koma osamudziwa [Iye], Ameneyu ndabwera kudzamulalikira kwa inu. 24Mulungu3 amene analenga dziko lapansi ndi zinthu zonse zopezeka m’menemo, Iye, pokhala Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, samakhala m’kachisi womangidwa ndi manja, 25kapena kutumikiridwa ndi manja a anthu monga wosowa kanthu, Iye mwini amapereka moyo onse ndi mpweya ndi zinthu zonse; 26ndipo anapanga mtundu ulionse wa anthu padziko lapansi kukhala mwazi umodzi, atapangiratu nyengo zawo ndi malire a pokhala pawo, 27kuti amfunefune Mulungu4; ngatidi iwo adzamfuna Iye ndi kumupeza, ngakhale kuti Iye sali kutali ndi wina aliyense wa ife: 28pakuti mwa Iye timakhala ndi kuyenda ndi kupezeka; monganso umo ena mwa olakatula ndakatulo pakati panu ananena, Pakuti ifenso ndife mbadwa zake. 29Pamenepo pokhala mbadwa za Mulungu5, sitikuyenera kuganiza kuti chimene chili cha umulungu chioneke ngati golide kapena siliva, kapena mwala, wosema bwino ndi luso komanso malingaliro a munthu. 30Pamenepo Mulungu6, polekerera mu nthawi ya kusadziwa, tsopano akulamulira anthu paliponse kuti onse alape, 31chifukwa wakhazikitsa tsiku limene Iye adzaweruza okhala padziko lapansi m’chilungamo mwa munthu amene Iye anamusankha, popereka umboni [wa ichi] kwa onse anamuukitsa Iye pakati pa akufa. 32Ndipo pamene iwo anamva za kuuka kwa akufa, ena anamseka, ndipo ena anati, Tidzakumvanso nthawi ina zokhudza zimenezi. 33Pomwepo Paulo anachoka pakati pawo. 34Koma anthu ena anaziphatika okha kwa iye nakhulupilira; ena mwa iwonso anali Dionisiyo m’Areopagi, ndi ena amene anali nawo.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu