Mutu 24
1Ndipo Yesu anachoka ndi kutuluka m’kachisi, ndipo ophunzira ake anabwera kwa [Iye] namulozera nyumba ya kachisi. 2Ndipo Iye poyankha anati kwa iwo, Kodi simukuona zinthu zonse izi? Zoonadi ndinena kwa inu, Palibe mwala ndi umodzi umene sudzagwetsedwa. 3Ndipo pamene anakhala pansi pamwamba pa phiri la Azitona ophunzira anabwera kwa Iye payekha, nanena, Tatiuzeni ife, kodi zinthu zimenezi zizachitika liti, ndipo chizindikiro cha kubwera kwanu ndi chimaliziro cha nthawi ino ndi chiti? 4Ndipo Yesu pakuyankha anati kwa iwo, Onetsetsani kuti aliyense asasocheretse inu. 5Pakuti ambiri adzabwera m’dzina langa, nadzanena, Ine ndine Khristu, ndipo adzasokeretsa anthu ambiri. 6Komatu mudzamva za nkhondo ndi mphekesera za nkhondo. Onetsetsani kuti musasokonezeke; pakuti [zinthu zonse izi] zikuyenera kuchitika, komatu chimaliziro sichinafike. 7Pakuti mtundu wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi milili, ndi zivomezi malo osiyanasiyana. 8Koma zinthu zonsezi [ndizo] chiyambi cha zowawa. 9Pamenepo adzakuperekani inu ku msautso, ndipo adzakuphani inu; ndipo mitundu yonse ya anthu idzadana ndi inu chifukwa cha dzina langa. 10Ndipo pamenepo anthu ambiri adzakhumudwa, ndipo adzaperekana wina ndi mzake, ndi kudana wina ndi mzake; 11ndipo aneneri onyenga ambiri adzauka ndipo adzasocheretsa anthu ambiri; 12ndipo chifukwa chakuti kusaweruzika kudzachuluka, chikondi cha anthu ambiri chizazizira; 13komatu wakupirira kufika kumapeto, iyeyu adzapulumuka. 14Ndipo uthenga wabwino uwu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, kuchitira umboni mitundu yonse, ndipo pamenepo chimaliziro chidzafika.
15Pamene mudzaona chonyansa cha kupululutsa, chimene chinanenedwa m’buku la Danieli mneneri, chitaima [amene ali] malo woyera, (iye amene amadziwa kuwerenga azindikire,) 16pamenepo iwo amene ali ku Yudeya athawire ku mapiri; 17iye amene ali pamwamba pa nyumba asatsike kukatenga zinthu m’nyumba mwake; 18ndipo iye amene ali kumunda asabwerere kukatenga chovala chake. 19Koma tsoka kwa iwo akukhala ndi ana, ndi iwo amene akuyamwitsa m’masiku amenewo. 20Komatu mupemphere kuti kuthawa kwanu kusadzakhale m’nyengo yozizira kapena pa sabata: 21pakuti pamenepo padzakhala mazunzo akulu, amene sanaonekepo kuyambira pachiyambi kufikira pano, ndipo sipadzakhalanso otere; 22ndipo ngati masiku amenewo sakanafupikitsidwa, thupi lina lililonse silikanapulumutsidwa; koma chifukwa cha osankhidwa masiku amenewo adzafupikitsidwa. 23Pamenepo ngati wina aliyense adzanena kwa inu, Taonani, Khristu ali kuno, kapena uko, musakhulupirire [izi]. 24Pakuti adzauka odzitcha Khristu abodza, ndi eneneri onyenga, ndipo adzapereka zizindikiro zikuluzikulu ndi zozizwa, cholinga akasokeretse, ngati nkotheka, iwonso amene ali osankhika. 25Taonani, Ine ndakuuziranitu. 26Ngati pamenepo iwo adzanena kwa inu, Taonani, ali m’chipululu, musapite inu kumeneko; taonani, [iye ali] m’zipinda za mkati, musakhulupirire [izi]. 27Monga umo mphenzi ithwanima kuchoka ku m’mawa ndi kuwalira ku madzulo, chomwechonso kubwera kwa Mwana wa munthu. 28[Pakuti] kumene kuli mtembo, nkhwazi zimasonkhana komweko.
29Komatu akadzangotha mazunzo a masiku amenewo dzuwa lidzadetsedwa, ndipo mwezi sudzapereka kuwala kwake, ndipo nyenyezi zidzagwa kuchoka kumwamba, ndipo mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka. 30Ndipo pamenepo padzaoneka chizindikiro cha Mwana wa munthu m’mwamba; ndipo mitundu yonse ya anthu padziko lapansi idzabuma, ndipo adzaona Mwana wa munthu akubwera m’mitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. 31Ndipo adzatumiza angelo ake ndi mfuu waukulu wa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi osankhika ake ku mphepo zinayi, kuyambira [kwa m’modzi] wa kumayambiliro [a] thambo kufikira [kwa wina] wakumapeto kwa iwo.
32Komatu phunzirani ku fanizo la mtengo wa mkuyu: Pamene nthambi yake ili ya nthete niphuka masamba, mumadziwa kuti dzinja layandikira. 33Chimodzimodzinso inu, pamene muona zinthu zonsezi, dziwani kuti ili pafupi, inde pakhomo. 34Zoonadi ndinena kwa inu, M’badwo uwu sudzachoka kufikira zinthu zonsezi zidzachitike. 35Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mau anga sadzachoka ayi. 36Koma za tsiku ilo ndi nthawi yake palibe amene amadziwa, ngakhale angelo akumwamba, komatu Atate [wanga] yekha. 37Koma monga analili masiku a Nowa, chomwechonso zizatero kubwera kwa Mwana wa munthu. 38Pakuti iwo anali m’masiku amene chisanafike chigumula, anadya ndi kumwa, anakwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa, 39ndipo iwo sanadziwe kufikira chigumula chinabwera ndi kuwatenga iwo onse; chomwechonso zizatero kubwera kwa Mwana wa munthu. 40Pamenepo awiri adzakhala m’munda, m’modzi adzatengedwa ndipo wina kusiyidwa; 41[akazi] awiri adzakhala akupera pa mphero, wina adzatengedwa ndipo wina adzasiyidwa. 42Khalani tcheru pamenepo, pakuti simudziwa nthawi imene Ambuye wanu adzabwera. 43Komatu dziwani ichi, kuti ngati mwini nyumba akadadziwa nthawi ya kudikira pamene mbala ikubwera, akadakhala tcheru kuti nyumba yake isabooledwe. 44Chomwecho inunso, khalani okonzeka, pakuti mu nthawi imene simukuganizira Mwana wa munthu adzabwera. 45Kodi ndi ndani pamenepo kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene mbuye wake amkhazika kukhala woyang’anira a m’nyumba mwake, kuwapatsa zakudya munyengo yake? 46Wodala ali kapoloyo amene mbuye wake pobwera adzampeza akuchita chotero. 47Zoonadi ndinena kwa inu, kuti adzamuika iye akhale woyang’anira zinthu zake zonse. 48Koma ngati kapolo woipa anena mu mtima mwake, Mbuye wanga akuchedwa kubwera, 49ndipo nayamba kumenya akapolo amzake, ndi kudya ndi kumwa pamodzi ndi oledzera; 50mbuye wa kapolo ameneyu adzabwera tsiku limene iye sakuliyembekezera, ndi nthawi imene iye sanaidziwe, 51ndipo adzamdula iye pawiri ndi kumsankhira pokhala pamodzi ndi onyenga: kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.