Mutu 6
1Kodi pamenepo tidzanena chiyani? Tipitirize kuchimwa kuti chisomo chichulukebe? 2Musaganize choncho. Ife amene tinafa ku uchimo, tikakhalabe bwanji m’menemo? 3Kodi simudziwa kuti ife, monga tinabatizidwa mwa Khristu Yesu, tinabatizidwa mu imfa yake? 4Pamenepo tayikidwa naye m’manda pamodzi mwa ubatizo wa mu imfa, cholinga kuti, ngakhale kuti Khristu anaukitsidwa pakati pa akufa mwa ulemelero wa Atate, chotero ifenso tiyende m’moyo watsopano. 5Pakuti ngati ife tikhala odziwika ndi [Iye] mwa chifanizo cha imfa yake, koteronso kudzakhala pa kuuka kwake; 6podziwa ichi, kuti munthu wathu wakale anapachikidwa ndi [Iye], kuti thupi la uchimo likhale lopanda mphamvu, kuti tisatumikirenso tchimo. 7Pakuti iye amene anafa analungamitsidwa ku uchimo. 8Tsopano ngati ife tinafa ndi Khristu, tikhulupilira kuti tidzakhalanso nawo moyo ndi Iye, 9podziwa kuti Khristu ataukitsidwa pakati pa akufa sanafenso: imfa ilibenso mphamvu pa Iye. 10Pakuti m’menemo Iye anafa, kufa ku tchimo kamodzi kokha; komatu m’menemo akhala ndi moyo, akhala wa kwa Mulungu1. 11Chomwechonso inu, muziyese akufa ku tchimo ndi amoyo kwa Mulungu2 mwa Khristu Yesu. 12Musalore pamenepo tchimo lilamulire thupi lanu la imfa kumvera chilakolako chake. 13Kapena kupereka ziwalo zanu kukhala zida za kusalungama kwa tchimo, koma mudzipereke nokha kwa Mulungu3 amoyo pakati pa akufa, ndi matupi anu kukhala zida za kulungama kwa Mulungu4. 14Pakuti tchimo silidzakhalanso ndi mphamvu pa inu, pakuti inu simuli pansi pa lamulo koma pansi pa chisomo.
15Nanga chiyani pamenepo? Tidzichimwa chifukwa tili pansi pa chisomo? Musaganize choncho. 16Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mwadzipereka kapolo wakumvera, mukhala kapolo kwa iye amene mumumverayo, mwina wa uchimo waku imfa, kapena kumvera ku kulungama? 17Koma zikomo kwa Mulungu5, kuti inu munali akapolo a tchimo, koma mwamvera kuchokera ku mtima mtundu wa chiphunzitso chimene inu munalangizidwa nacho. 18Tsopano, mutapeza mtendere wanu kuchoka ku tchimo, mwakhala akapolo a kulungama. 19Ine ndikulankhula mwa umunthu zokhudza kufooka kwa thupi lanu. Pakuti ngakhale monga kuti munapereka matupi anu mu ukapolo wa chinyaso ndi kusamvera, chomwecho tsopano perekani matupi anu mu ukapolo wa kulungama m’chiyero. 20Pakuti pamene inu munali akapolo a tchimo munali omasuka ku kulungama. 21Kodi muli nacho chipatso chanji pamenepo mu zinthu zimene mukuchita nazo manyazi tsopano? Pakuti mapeto ake a izi [ndi] imfa. 22Koma tsopano, popeza ufulu wanu kuchoka ku tchimo, ndi kukhala akapolo kwa Mulungu6, muli nacho chipatso chanu m’chiyero, ndipo mathero ake ndi moyo wosatha. 23Pakuti mphoto yake ya tchimo [ndi] imfa; koma machitachita a kukonderedwa kwa Mulungu7, ndiwo moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu