Mutu 3
1Taonani chikondi chimene Atate watipatsa, kuti ife titchedwe ana a Mulungu1. Pachifukwa chimenechi dziko lapansi silitidziwa ife, chifukwa silinamdziwe iye. 2Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu2, ndipo chimene tidzakhala sichinaoneke; tikudziwa kuti ngati chidzaonetsedwa tidzakhala ngati iye, pakuti tidzamuona iye monga ali. 3Ndipo aliyense amene ali ndi chiyembekezo chimenechi adziyeretsa yekha, monga iye ali woyera.
4Aliyense wakuchita tchimo achitanso kusaweruzika; ndipo tchimo ndiko kusaweruzikako. 5Ndipo inu mudziwa kuti iye waonetsedwa kuti atichotsere machimo athu; ndipo mwa iye mulibe tchimo. 6Aliyense wakukhala mwa iye, samachimwa: aliyense amene amachimwa, sanamuone iye kapena samudziwa iye.
7Ana inu, munthu aliyense asakusokeretseni; iye amene achita chilungamo ali wolungama, monga iye ali wolungama. 8Iye wakuchita tchimo ali wa mdierekezi; pakuti kuyambira pachiyambi mdierekezi amachimwa. Kufikira mapeto Mwana wa Mulungu3 waonetsedwa, kuti akathetse ntchito za mdierekezi. 9Aliyense wobadwa mwa Mulungu4 samachimwa, chifukwa mbewu yake ikhalira mwa iye, ndipo sangachimwe, chifukwa iye wabadwa mwa Mulungu5. 10M’menemu awonekera ana a Mulungu6 ndi ana a mdierekezi. Aliyense amene sachita chilungamo sali wa Mulungu7, komanso amene sakonda m’bale wake. 11Pakuti umenewu ndi uthenga umene mwaumva kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mzake: 12osati monga Kaini wa woipayo, ndipo anapha m’bale wake; ndipo anamupha pachifukwa chanji? Chifukwa ntchito zake zinali zoipa, komanso za m’bale wake zinali zolungama.
13Musadabwe, abale, ngati dziko lapansi likudani. 14Ife tikudziwa kuti tatuluka mu imfa tapita ku moyo, chifukwa tiwakonda abale. Iye amene sakonda m’bale wake akhala mu imfa. 15Aliyense wakudana ndi m’bale wake ali wakupha, ndipo inu mukudziwa kuti wakupha alibe moyo wamuyaya wokhala mkati mwake.
16Umo ife tadziwira chikondi, chifukwa iye anataya moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ife tiyenera kupereka moyo [wathu] chifukwa cha abale. 17Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona m’bale wake ali ndi chosowa, natsekera chifundo chake kwa iye, kodi chikhazikika bwanji chikondi cha Mulungu8 mwa iye?
18Ana inu, tiyeni tisakonde ndi mau chabe, kapena ndi lilime, koma mu ntchito ndi m’choonadi. 19Ndipo pamenepo tizadziwa kuti tili a choonadi, ndipo tidzakhazikitsa mitima yathu pamaso pake — 20kuti ngati mtima wathu ukatitsutsa ife, Mulungu9 ndi wamkulu kuposera mtima wathu ndipo amadziwa zinthu zonse. 21Okondedwa, ngati mtima wathu sutitsutsa, tili nako kulimbika mtima pa Mulungu10, 22ndipo kalikonse kamene ife tingapemphe tidzalandira kuchokera kwa iye, chifukwa timasunga malamulo ake, ndi kuchita zinthu zimene zili zokondweretsa pamaso pake. 23Ndipo limeneli ndi lamulo lake, kuti timakhulupilira padzina la Mwana wake Yesu Khristu, ndi kuti tikondane wina ndi mzake, monga iye anatipatsa ife lamulo. 24Ndipo amene amasunga malamulo ake akhala mwa iye, ndi iye mwa munthuyo. Ndipo pamenepo tidziwa kuti iye akhala mwa ife, mwa Mzimu amene anatipatsa.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu