Mutu 20

1Ndipo ndinaona mngelo akutsika kuchoka kumwamba, wakukhala nacho chifungulo cha kuphompho m’dzanja lake. 2Ndipo iye anagwira chinjoka, njoka yokalamba amene ali mdierekezi ndi Satana, ndipo anam’manga iye kwa zaka chikwi, 3ndipo anamponya kuphompho, natsekako nayika chizindikiro pa iye, kuti asanyengenso mitundu kufikira zaka chikwi zikwane; zitapita zimenezi akamasulidwe kwa kanthawi.

4Ndipo ndinaona mipando yachifumu; ndi iwo akukhalapo, ndipo chiweruzo chinaperekedwa kwa iwo; ndipo mizimu ya iwo amene anadulidwa mitu chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu1; ndi iwo amene sanalambire chirombocho kapena chifanizo chake, ndipo sanalandire chizindikiro pamphumi pawo ndi padzanja; ndipo iwo anakhala moyo nalamulira ndi Khristu kwa zaka chikwi: 5otsalira akufawo sanakhale moyo kufikira zaka chikwi zitamalizika. Chimenechi [ndicho] chiukitso choyamba. 6Wodala ndi woyera amene adzakhala ndi gawo mu chiukitso choyambacho: pakuti pa amenewa imfa yachiwiri ilibe mphamvu; komatu adzakhala ansembe a Mulungu2 ndi a Khristu, ndipo adzalamulira ndi iye kwa zaka chikwi.

7Ndipo zikazatha zaka chikwi, Satana adzamasulidwa ku ndende yake, 8ndipo adzapita kusokeretsa mitundu imene [ili] ku ngodya zinayi za dziko lapansi, Gogo ndi Magogo, kuwasonkhanitsa pamodzi ku nkhondo, amene chiwerengero chawo [ndicho] mchenga wa panyanja. 9Ndipo iwo anakwera nafalikira padziko lapansi, ndi kuzungulira msasa wa oyera mtima ndi mzinda wokondedwa: ndipo moto unatsika [kuchokera kwa Mulungu3] kuchokera kumwamba ndi kuwanyeketsa. 10Ndipo mdierekezi amene anawanyenga iwo anaponyedwa mnyanja yamoto ndi sulfure, kumene [kuli] chirombo ndi mneneri wonyenga; ndipo azazunzidwa usana ndi usiku ku nthawi za nthawi.

11Ndipo ndinaona mpando wachifumu woyera, ndi iye wakukhalapo, amene nkhope ya dziko lapansi ndi kumwamba zinamuthawa, ndipo malo sanapezeke kwa iwo. 12Ndipo ndinaona akufa, akulu ndi ang’ono, akuyima pa mpando wachifumu, ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, limene lili la moyo. Ndipo akufa anaweruzidwa mu zinthu zolembedwa m’mabukumo molingana ndi ntchito zawo. 13Ndipo nyanja inapereka akufa awo amene [anali] m’menemo, ndipo imfa ndi hade zinapereka akufa awo amene [anali] m’menemo; ndipo anaweruzidwa molingana ndi ntchito zawo: 14ndipo imfa ndi hade zinaponyedwa m’nyanja ya moto. Imeneyi ndiyo imfa yachiwiri, [ngakhale] nyanja ya moto. 15 Ndipo ngati wina sanapezeke atalembedwa m’buku la moyo, anaponyedwa m’nyanja ya moto.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu