Mutu 19

1Ndipo zinangochitika, pamene Yesu anamaliza kulankhula mau amenewa, Iye anachokako ku Galileya, ndipo anabwera ku magombe a Yudeya kutsidya kwa Yordano; 2ndipo makamu ochuluka anamtsata Iye, ndipo Iye anawachiritsa kumeneko.

3Ndipo Afalisi anadza kwa Iye namuyesa, nanena, Kodi ndi kololedwa munthu kuchotsa mkazi wake pa chifukwa chilichonse? 4Koma Iye pakuyankha anati [kwa iwo], Kodi simunawerenge kuti iye amene anawapanga [iwo], kuchokera pachiyambi anawapanga iwo mwamuna ndi mkazi, 5ndipo anati, Pachifukwa chimenechi mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, ndipo adzaphatikana kwa mkazi wake, ndipo awiriwa adzakhala thupi limodzi? 6kotero kuti iwo salinso awiri, koma thupi limodzi. Pamenepo chimene Mulungu1 anachiphatika pamodzi, munthu aliyense asachilekanitse. 7Iwo anati kwa Iye, Nanga ndi chifukwa chiyani Mose analamulira kupereka kalata wa chilekaniro ndi kumuchotsa [iye]? 8Iye anati kwa iwo, Mose, pakuona kuuma kwa mitima yanu, anakulolani inu kuchotsa akazi anu; komatu kuchokera pachiyambi sizinali chomwechi. 9Koma ndinena kwa inu, kuti aliyense wakuchotsa mkazi wake, osati pa chifukwa cha chigololo, ndipo nakwatira wina, ameneyo wachita chigololo; ndipo iye amene akwatira wochotsedwayo wachitanso chigololo. 10Ophunzira ake anati kwa Iye, ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wake uli wotere, sibwino kukwatira. 11Ndipo Iye anati kwa iwo, Sionse amene akhoza kulandira mau amenewa, komatu kwa iwo amene apatsidwa; 12pakuti alipo osabereka amene anabadwa choncho kuchokera m’mimba mwa amayi [awo]; ndipo aliponso osabereka amene anachita kufulidwa ndi anthu; ndiponso alipo osabereka amene anazifula okha chifukwa cha ufumu wakumwamba. Iye amene akhoza kuwalandira [awa], mlekeni awalandire [awa].

13Pamenepo anabwera nawo kwa Iye ana ang’ono kuti Iye awasanjike manja ndi kuwapempherera; komatu ophunzira anawadzudzula iwo. 14Koma Yesu anati, Alekeni ana ang’ono, ndipo musawakanize iwo kubwera kwa Ine; pakuti ufumu wa kumwamba uli wa otere: 15ndipo atasanjika manja ake pa iwo, Iye anachoka kumeneko.

16Ndipo taonani, wina anabwera nanena kwa Iye, Mphunzitsi, kodi ndichite chiyani chabwino kuti ndikhale nawo moyo wosatha? 17Ndipo anati kwa iye, Chifukwa chiyani ufunsa zokhudza kuchita chabwino? Alipo m’modzi yekha amene ali wabwino. Komatu iwe ufuna kukalowa m’moyo, sunga malamulo. 18Anati kwa iye, Otani? Ndipo Yesu anati, Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachitire umboni wabodza, 19Lemekeza Atate wako ndi amako, komanso Uzikonda mzako monga uzikonda iwe mwini. 20Mnyamata uja anati kwa Iye, Onsewa ndakhala ndikuwasunga ine; ndisowanso chiyani? 21Yesu anati kwa iye, ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo ndipo upereke kwa osauka, ndipo udzakhala nacho chuma kumwamba; ndipo ubwere, nunditsate Ine. 22Koma mnyamata uja pakumva mauwa, anachoka ali ndi chisoni, pakuti anali ndi chuma chambiri. 23Ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, Indetu ndinena kwa inu, Munthu wolemera adzalowa movutika mu ufumu wakumwamba; 24ndinenanso kwa inu, Nkwapafupi kwa ngamila kulowa pa diso la singano kusiyana ndi munthu wolemera kulowa mu ufumu wa Mulungu2. 25Ndipo pamene ophunzira anamva [ichi] anali ozizwa kwambiri, nanena, Nanga ndi ndani amene angapulumutsidwe? 26Koma Yesu, pakuwaona [iwo], anati kwa iwo, Ndi anthu zimenezi ndi zosatheka; koma ndi Mulungu3 zonse ndi zotheka.

27Pamenepo Petro pakuyankha anati kwa Iye, Taonani, ife tasiya zinthu zonse ndipo takutsatirani inu; kodi ndi chiyani chimene chidzachitika kwa ife? 28Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Kuti inu amene mwanditsata Ine, m’kukozedwanso pamene Mwana wa munthu adzakhala pa mpando wa ulemelero wake, inunso mudzakhala nawo pa mipando ya chifumu khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a mtundu wa Israyeli. 29Ndipo aliyense amene wasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amayi, kapena mkazi, kapena ana, kapena malo, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezera zochuluka, ndipo akalowa moyo wosatha. 30Komatu ambiri oyambilira adzakhala akumapeto, ndipo akumapeto oyambilira.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu