Mutu 16

1Ndipo iye anapita ku Derbe ndi Lustra: ndipo taonani, wophunzira wina anali pamenepo, dzina lake Timoteo, mwana wa mkazi wina wokhulupilira wa Chiyuda, koma atate wake anali Mhelene, 2amene anali ndi umboni [wabwino] wa abale m’Lustra ndi Ikoniyo. 3Ameneyu Paulo anafuna kupita naye, ndipo anamutenga [iye ndi] kumuchita mdulidwe chifukwa cha Ayuda amene anali ku malo amenewo, pakuti iwo onse anadziwa kuti atate wake anali Mhelene. 4Ndipo pamene iwo amadutsa m’mizinda anawalangiza iwo kusamalira malamulo amene anaperekedwa ndi atumwi komanso akulu amene anali mu Yerusalemu. 5Pamenepo mipingoyo inalimbikitsidwa mu chikhulupiliro, ndipo anachulukira mu chiwerengero tsiku lililonse.

6Ndipo atadutsa mu Frugiya ndi dziko la Galatiya, analetsedwa ndi Mzimu Woyera kulankhula mau mu Asiya, 7atatsikira kufika ku Musiya, iwo anayesera kufuna kupita ku Bituniya, ndipo Mzimu wa Yesu sunawalole iwo; 8ndipo atadutsira ku Musiya anafika ku Trowa. 9Ndipo masomphenya anaonekera kwa Paulo usiku: Kumeneko kunali munthu wina waku Makedoniya, atayimilira ndi kumupempha iye, ndi kuti, Udutsire ku Makedoniya ndipo udzatithandize ife. 10Ndipo pamene anaona masomphenyawa, nthawi yomweyo tinafuna kupita ku Makedoniya, kuganiza kuti Ambuye watiyitanira ife kukalalikira kwa iwo uthenga wabwino. 11Pamenepo tinayenda m’ngalawa kuchoka ku Trowa, tinapita mu njira yolunjika ku Samotrake, ndipo m’mawa mwake ku Neapoli, 12ndipo kuchoka kumeneko ku Filipi, umene unali mzinda woyamba kulamulidwa monga gawo la Makedoniya. Ndipo tinakhala mu mzinda umenewo kwa masiku angapo. 13Ndipo pa tsiku la sabata tinatuluka kunja kwa chipata mphepete mwa mtsinje, kumene monga mwa mwambo kumayenera kuchitikako mapemphero, ndipo ife tinakhala pansi ndi kulankhula nawo akazi amene anasonkhana. 14Ndipo mkazi wina, dzina lake Lidiya, wogulitsa chibakuwa, wa mu mzinda wa Tiyatira, amene amapembedza Mulungu1, anamva; amene mtima wake Ambuye anautsegula kusamalira zinthu zimene zinalankhulidwa ndi Paulo. 15Ndipo pamene iye anabatizidwa ndi nyumba yake, anatidandaulira [ife], nanena, Ngati inu mwandiweruza ine kukhala wokhulupirika kwa Ambuye, lowani mnyumba mwanga ndi kukhala [m’menemo]. Ndipo iye anatiumiriza ife. 16Ndipo kunachitika kuti pamene timapita kukapemphera kuti kapolo wina wa mkazi, amene anali ndi mzimu Wobwebweta, anakumana nafe, amene amabweretsa phindu lochuluka kwa ambuye ake ponenera. 17Iyeyu, pamene anatsatira Paulo ndi ife, anafuula nati, Anthu awa ndi akapolo a Mulungu2 wam’mwambamwamba, amene akukulalikirani inu njira ya chipulumutso. 18Ndipo zimenezi anachita kwa masiku ochuluka. Ndipo Paulo, potopa nazo, anatembenuka, ndipo anati kwa mzimuwo, Ndikukulamulira m’dzina la Yesu Khristu kuti utuluke mwa iye. Ndipo unatuluka ola lomwelo. 19Ndipo ambuye wake, poona kuti chiyembekezo cha phindu lawo chapita, anamgwira Paulo ndi Sila, nawaduduluzira [iwo] mu msika kupita pamaso pa oweruza; 20ndipo pamene anawabweretsa iwo kwa oweruza, anati, Anthu awa akubweretsa vuto mu mzinda mwathu, pokhala Ayuda, 21ndipo akulalikira miyambo imene ili yosaloledwa kwa ife kuyilandira, pokhala ife Aroma. 22Ndipo khamulo linaukanso motsutsana nawo; ndipo oweruzawo, anawang’ambira iwo zovala, nalamulira kuti akwapulidwe [iwo]. 23Ndipo pamene anawapatsa mikwingwirima yambiri anawaponya [iwo] mndende, nalamulira mdindo wa ndende kuti awasamalire iwo; 24ameneyu, pamene analandira lamulo lotere, anawaponya iwo mndende ya pakatikati, ndipo anawamanga mapazi awo m’zigologolo. 25Ndipo pakati pa usiku Paulo ndi Sila, popemphera, amalemekeza Mulungu3 poyimba nyimbo, ndipo akayidi anawamva iwo. 26Ndipo mwadzidzidzi kunachitika chivomezi, kotero kuti maziko a ndende anagwedezeka, ndipo makomo onse a ndende anatseguka, ndipo maunyolo a onse anamasuka. 27Ndipo mdindoyo pouka kutulo take, ndi poona kuti makomo a ndende atseguka, anasolola lupanga lake nafuna kuzipha nalo, poganiza kuti akayidi athawa. 28Koma Paulo anafuula ndi mau okweza, nanena, Usazipweteke wekha, pakuti tonse tilipo muno. 29Ndipo pamene anapempha nyali, analowa mkati, monjenjemera, nagwa pamapazi a Paulo ndi Sila. 30Ndipo pamene anawatulutsa panja anati, Ambuye, ndichite chiyani kuti ndipulumutsidwe? 31Ndipo iwo anati, Khulupilira pa Ambuye Yesu ndipo iwe udzapulumuka, iwe ndi nyumba yako. 32Ndipo iwo analankhula kwa iye mau a Ambuye, ndi zonse zimene zinali mnyumba mwake. 33Ndipo iye anawatenga iwo ola lomwelo la usiku ndi kuwasambitsa [iwo] ku mikwingwirima yawo; ndipo iye anabatizidwa, iye pamodzi ndi apabanja pake. 34Ndipo atawabweretsa iwo mnyumba mwake anawakonzera [iwo] gome la chakudya, nasangalala pamodzi ndi banja lake lonse, atakhulupilira mwa Mulungu4. 35Ndipo pamene kunali masana, oweruza anatuma akapitawo, nanena, Amasuleni amuna aja adzipita. 36Ndipo mdindoyo anatumiza uthenga kwa Paulo: Oweruza atumiza uthenga kuti mukhoza kumapita. Pamenepo tsopano nyamukani mu mtendere. 37Koma Paulo anati kwa iwo, Mutatikwapula ife pagulu musanamve mlandu wathu, ife amene tili Aroma, anatiponya ife mndende, ndiye pano akutitulutsa mwa mseri? Zoona, ayi ndithu, komatu auzeni abwere okha adzatitulutse. 38Ndipo akapitawo anatumiza mau amenewa kwa oweruza. Ndipo iwo anachita mantha pakumva kuti anali Aroma. 39Ndipo iwo anabwera kudzawadandaulira iwo, ndipo pamene anawatulutsa, anawapempha kuti atuluke mu mzindawo. 40Ndipo pamene anatuluka mndendemo, iwo anapita ku Lidiya; ndipo pamene anawaona abale, anawalimbikitsa nanyamuka.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu