Mutu 12

1Ndipo chizindikiro chachikulu chinaonekera m’mwamba: mkazi wovala dzuwa, ndi mwezi ku mapazi kwake, ndipo pamutu pake korona wa nyenyezi khumi ndi ziwiri; 2ndipo pokhala ndi mwana iye analira, [pokhala] mu ululu, ndi ululu wa pobereka.

3Ndipo chizindikiro china chinaoneka m’mwamba: ndipo taonani, chinjoka chachikulu chofiira, chokhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi, ndipo pamutu pake nduwira zisanu ndi ziwiri; 4ndipo mchira wake uguza gawo lachitatu la nyenyezi za kumwamba; ndipo anaziponya padziko lapansi. Ndipo chinjokacho chinayimilira pamaso pa mkaziyo amene amafuna kubereka, cholinga kuti pamene akubereka amlikwire mwana wake. 5Ndipo iye anabereka mwana wa mwamuna, amene adzaweta mafuko onse ndi ndodo ya chitsulo; ndipo mwana wake anakwatulidwa kwa Mulungu1 ndi ku mpando wake wachifumu. 6Ndipo mkaziyo anathawira m’chipululu, kumene kuli malo ake wokonzedwa ndi Mulungu2, kuti akamusamale iye kumeneko kwa masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri kudza mphambu makumi asanu ndi limodzi.

7Ndipo kunali nkhondo kumwamba: Mikayeli ndi angelo ake kulimbana ndi chinjoka chija. Ndipo chinjokacho chinamenya nkhondo, pamodzi ndi angelo ake; 8ndipo icho sichinapambane, kapenanso malo kupezeka kwa iye m’mwamba. 9Ndipo chinjoka chachikulucho chinaponyedwa pansi, chinjoka chokalamba, iye amene amatchedwa Mdierekezi ndi Satana, iye amene ananyenga dziko lonse lapansi, anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.

10Ndipo ndinamva mau akulu m’mwamba akunena, Tsopano chafika chipulumutso ndi mphamvu ndi ufumu wa Mulungu3 wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake; pakuti woneneza wa abale athu waponyedwa kunja, amene anawaneneza iwo pamaso pa Mulungu4 usana ndi usiku: 11ndipo iwo anamgonjetsa iye chifukwa cha mwazi wa Mwanawankhosa, ndi chifukwa cha mau a umboni wao, ndipo sanaukonde moyo wao ngakhale kufikira imfa. 12Chomwecho khalani ndi chimwemwe chodzala, miyamba inu, ndi inu akukhalira momwemo. Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo mkwiyo waukulu, podziwa kuti watsala ndi kanthawi kochepa.

13Ndipo pamene chinjokacho chinaona kuti chaponyedwa m’dziko lapansi, chinamzuza mkazi uja amene anabereka [mwana] wa mwamuna. 14Ndipo kunapatsidwa kwa mkaziyo mapiko awiri a nkhwazi yaikulu, kuti auluke kupita ku chipululu kumalo kwake, kumene atasamalidwe kwa kanthawi, ndi nthawi, ndi theka ya nthawi, kuchoka pamaso pa chinjokacho. 15Ndipo chinjokacho chinalavulira kumbuyo kwa mkaziyo madzi ngati mtsinje, kuti akampangitse iye ngati munthu wokokoloka ndi mtsinje. 16Ndipo dziko lapansi linamthandizira mkaziyo, ndipo dziko lapansi linatsegula pakamwa pake ndi kumeza mtsinjewo umene chinjoka chija chinalavula kuchoka mkamwa mwake. 17Ndipo chinjokacho chinali ndi ukali ndi mkaziyo, ndipo chinapita kukachita nkhondo ndi otsala a mbeu yake, amene anasunga malamulo a Mulungu5, ndipo ali ndi umboni wa Yesu.

18Ndipo ndinayima pa mchenga wa panyanja;

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu