Mutu 17

1Ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, sizingatheke kuti zoipa zisabwere, koma tsoka [kwa iye] amene abwera nazo! 2Zikanakhala zopindulitsa [kwambiri] kwa iye ngati mwala wa mphero ukanamangidwa m’khosi mwake ndi kuponyedwa m’nyanja, kusiyana kuti akhale chokhumudwitsa kwa kamodzi ka tiana iti. 3Ziyang’anireni nokha: ngati m’bale wanu achimwa, mdzudzuleni iye; ndipo ngati alapa, mkhululukireni. 4Ndipo akakuchimwirani inu kasanu ndi kawiri patsiku, ndipo kasanu ndi kawiri abwerera kwa inu, nanena, Ndalapa, mkhululukireni iye.

5Ndipo atumwi anati kwa Ambuye, Tipatseni ife chikhulupiliro chochuluka. 6Koma Ambuye anati, Mukanakhala ndi chikhulupiliro ngati [mbeu] ya mpiru, mukananena kwa mtengo uwu, uzidzule wekha, ndipo ukazidzale m’nyanja, ndipo ukanakumverani inu. 7Koma ndani wa inu amene, pokhala naye kapolo wolima kapena woyang’anira ziweto, pamene abwera kuchokera kumunda, anena naye, Bwera ukhale ndi kudya nane pa gome? 8Komatu sadzanena kwa iye, undikonzere zimene ndizadya, ndipo uzimangire wekha ndi kunditumikira kuti ndikadye ndi kumwa; ndipo pambuyo pake kuti iwe ukadye ndi kumwa? 9Kodi iye adzayamikira kapoloyo chifukwa wapanga zolamulidwazo? Ine sindingaweruze. 10Chotero inunso, pamene mudzachita zinthu zonse zolamulidwa kwa inu, munene kuti, Ndife akapolo osapindulitsa; tachita zinthu zimene tinayenera kuti tichite.

11Ndipo kunachitika kuti pamene Iye amapita ku Yerusalemu, kuti anadutsa pakatikati pa Samariya ndi Galileya. 12Ndipo analowa m’mudzi wina, anthu akhate khumi anakumana ndi Iye, amene anayima patali. 13Ndipo anakweza maso awo nanena, Yesu, Mbuye, tichitireni ife chifundo. 14Ndipo powaona [iwo] anati kwa iwo, Pitani, kadzionetsereni nokha kwa ansembe. Ndipo kunachitika kuti pamene iwo amapita anakonzedwa. 15Ndipo m’modzi wa iwo, powona kuti wachiritsidwa, anabwerera, nalemekeza Mulungu1 ndi mau okweza, 16ndipo anagwetsa nkhope [yake] pamapazi pake namuthokoza: ndipo iye anali m’Samariya. 17Ndipo Yesu poyankha anati, Kodi sanali khumi amene anakonzedwa? Koma asanu ndi anayiwo [ali kuti]? 18Sanapezeke wobwerera kudzalemekeza Mulungu2 kupatula mlendo uyu. 19Ndipo Yesu anati kwa iye, Dzuka nupite kwanu: chikhulupiliro chako chakupulumutsa iwe.

20Ndipo atafunsidwa ndi Afarisi kuti, Kodi ufumu wa Mulungu3 udzabwera liti? Iye anawayankha iwo nati, Ufumu wa Mulungu4 sumabwera ndi maonekedwe; 21kapena iwo azati, Taonani uli kuno, kapenanso uli uko; pakuti taonani, ufumu wa Mulungu5 uli pakati panu. 22Ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, Masiku akubwera, pamene muzalakalaka kuona limodzi la masiku a Mwana wa munthu, ndipo simudzaliona. 23Ndipo adzati kwa inu, Taonani uli kuno, kapena uli uko; musapiteko, kapena kuwatsatira [iwo]. 24Pakuti monga mphenzi ing’anima imene imang’anima kuchokera [mbali ina] pansi pa thambo kupita [mbali ina] pansi pa thambo, chomwechonso zizakhala choncho ndi Mwana wa munthu pa tsiku lake. 25Komatu poyamba akuyenera kumva zowawa zambiri ndi kukanidwa ndi m’badwo uno. 26Ndipo monga zinachitika m’masiku a Nowa, zomwezonso zizachitika m’masiku a Mwana wa munthu: 27anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa, ndipo namondwe anabwera ndi kuwaononga [iwo onse]; 28ndipo monga zinachitikira m’masiku a Loti: anadya, anamwa, anagula, anadzala, anamanga; 29koma patsiku limene Loti anatuluka kuchoka mu Sodomu, kunagwa moto ndi sufure kuchokera kumwamba, ndipo unawaononga onsewo: 30zitachitika moteremu, kudzachitika kuti Mwana wa munthu adzavumbulutsidwa. 31Tsikulo, iye amene adzakhala pamwamba panyumba, ndi katundu wake m’nyumba, ameneyo asatsike kukatenga katundu wake; ndipo amene ali kumunda, ameneyonso asabwerere kunyumba. 32Kumbukirani mkazi wa Loti. 33Amene adzafuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, ndipo amene adzautaya adzaupulumutsa. 34Ine ndinena kwa inu, Usiku umenewo kudzakhala [anthu] awiri pa kama m’modzi; wina adzatengedwa ndipo wina adzasiyidwa. 35[Akazi] awiri adzakhala akupera pamodzi; m’modzi adzatengedwa ndipo wina adzatsala. 36 [Amuna awiri adzakhala kumunda; wina adzatengedwa ndipo wina adzatsala.] 37NNdipo iwo poyankha anati kwa Iye, Kuti, Ambuye? Ndipo Iye anati kwa iwo, Kumene kuli mtembo, kumeneko miimba imasonkhana pamodzi.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu