Mutu 2

1Koma ndiweruza ichi mwa ine ndekha, kuti ndisabwerenso kwa inu m’chisoni. 2Pakuti ngati ndikuchititsani inu chisoni, ndani amene azandisangalatsa ine, ngati si uyo amene akumva chisoni mwa ine? 3Ndipo ndakulemberani kalata uyu, kuti pobwera ine ndisadzapeze chisoni kwa iwo amene akuyenera kusangalatsa ine; ndikhulupilira mwa inu nonse kuti chimwemwe changa chikhale cha inu nonse. 4Pakuti kuchoka mu m’sautso waukulu ndi kusweka mtima ndakulemberani inu, ndi misozi yochuluka; osati kuti mukakhale ndi chisoni, koma kuti mukadziwe chikondi chimene ndili nacho kwambiri pa inu. 5Koma ngati wina amva chisoni, wamva chisoni payekha, osati ine ayi, koma mbali ina (kuti ndisakulemetseni [inu] nonsenu. 6Chikwanire kwa wotere chidzudzulo ichi chimene [chapatsidwa] mwa ochuluka; 7kotero kuti mosiyana muonetsere chisomo ndi kulimbikitsa, kuti kapena wotereyu angamezedwe ndi chisoni chachikulu. 8Pamenepo ndikulimbikitsani kuti mumtsimikizire iye za chikondi chanu. 9Pakuti kufikira kumapeto uku ndakulemberaninso, kuti ndidziwe, pokuyikani inu pa mayeso, ngati kuti mu zonse muli omvera. 10Koma kwa iye amene mwamkhululukira kanthu, inenso ndimkhululukira; pakuti inenso, chimene ndakhululukira, ngati ndakhululukira kanthu, ndachita ichi chifukwa cha inu mwa munthu Yesu; 11kuti Satana asapeze mpata wotsutsana nafe, pakuti sitili mbuli pa malingaliro ake.

12Tsopano pamene tinafika ku Trowa polalikira uthenga wabwino wa Khristu, khomo linatsegukiranso ine mwa Ambuye, 13Ndinalibe mpumulo mu mzimu mwanga pamene sindinampeze Tito m’bale wanga; koma powatsanzika iwo, ndinachoka kupita ku Makedoniya. 14Koma alemekezeke 1Mulungu, amene amatitsogolera ife ku chipambano mwa Khristu, ndi kusonyezera fungo labwino la chidziwitso chake kudzera mwa ife pamalo paliponse. 15Pakuti ndife fungo labwino la Khristu mwa 2Mulungu, mwa opulumutsidwa ndi mwa iwo amene anaonongeka: 16kwa wina fungo lochoka ku imfa kupita ku imfa, koma kwa ena fungo lochoka ku moyo kupita ku moyo; ndani amene ali wokwanira mu zinthu zimenezi? 17Pakuti ife, monga ambiriwo, sitichita malonda pa mau a 3Mulungu; koma ndi mtima woona, koma monga mwa 4Mulungu, pamaso pa 5Mulungu, tilalikira Khristu.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu