Mutu 11
1Ndipo panali pamene Yesu anamaliza kuwalamulira ophunzira ake khumi ndi awiri, anachoka kumeneko kukaphunzitsa ndi kulalikira m’mizinda mwao.
2Koma Yohane, pakumva m’ndende ntchito za Khristu, anatumiza ophunzira ake, 3ndipo ananena ndi Iye, Kodi ndinu wakudzayo? Kapena tiyembekezere wina? 4Ndipo Yesu pakuyankha ananena kwa iwo, Pitani, kamuuzeni Yohane zimene mwamva ndi kuona. 5[Anthu] akhungu akupenya ndipo olumala akuyenda; akhate akuyeretsedwa, ndipo osamva akumva; ndipo akufa akudzutsidwa, ndipo osauka uthenga wabwino ukulalikidwa kwa iwo: 6ndipo wodala amene sadzakhumudwa mwa Ine.
7Koma pamene iwo amachoka, Yesu anayamba kulankhula kwa makamu zokhudza Yohane, Kodi mutatuluka kupita ku chipululu munakaonako chiyani? Bango likugwedezedwa ndi mphepo? 8Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala chovala chofewa kodi? Taonani, iwo amene amavala chovala chofewa amapezeka m’nyumba za mafumu. 9Koma inu munatuluka kukaona chiyani? Mneneri kodi? Indetu, ndinena kwa inu, ndipo woposa mneneri: 10ameneyu ndi yemwe kunalembedwa za Iye, Taonani, Ine nditumiza mthenga pamaso panu, amene adzakonza njira yanu pamaso panu. 11Indetu ndinena kwa inu, palibe amene anauka kuchoka mwa mkazi wamkulu kuposa Yohane m’batizi. Komatu amene ali wamng’ono mu ufumu wa kumwamba ali wamkulu kuposa iye. 12Koma kuchokera mu nthawi ya Yohane kufikira tsopano, ufumu wa kumwamba umatengedwa mokakamiza, ndipo wokakamirawo adzaukwatula. 13Pakuti aneneri onse komanso chilamulo ananenera za Yohane. 14Ndipo ngati mukalandira, ameneyu ndi Eliya, amene anati ali mkudza. 15Iye amene ali nawo makutu akumva, amve. 16Koma ndidzafanizira chiyani m’badwo uwu? Uli ngati ana akukhala m’misika, akuitana amzawo, 17nanena, tinakuimbirani inu zitoliro, ndipo simunavine: takulilirani maliro inu, ndipo inu simunalire. 18Pakuti Yohane sanabwere kumwa kapena kudya, ndipo ananena ali ndi chiwanda. 19Mwana wa munthu wabwera kudya ndi kumwa, ndipo iwo anena, Taonani, munthu [amene] akudya ndi kumwa vinyo, bwenzi la okhometsa misonkho, ndi ochimwa: — ndipo nzeru yalungamitsidwa ndi ana ake.
20Pamenepo Iye anayamba kudzudzula mizinda imene ntchito za mphamvu yake zakhala zikuchitika, pakuti iwo sanalape. 21Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe Betsaida! Pakuti ntchito za mphamvu zimene zinachitika kwa iwe, zikanachitika m’Turo ndi m’Sidoni, akadalapa kalekale mu ziguduli ndi m’phulusa. 22Koma ndinena kwa inu, kuti udzachepa mlandu wa Turo ndi Sidoni patsiku la chiweruzo kusiyana ndi mlandu wanu. 23Ndipo iwe, Kapernao, amene unakwezedwa kumwamba, udzatsitsidwa ngakhale kufika ku dziko la akufa. Pakuti ngati ntchito za mphamvu zimene zachitika mwa iwe, zikadachitika mwa Sodomu, zikadakhalabe kufikira lerolino. 24Komatu ndinena kwa inu, kuti udzachepa mlandu wa dziko la Sodomu patsiku la chiweruzo kusiyana ndi mlandu wanu.
25Pa nthawi imeneyo, Yesu pakuyankha anati, Ndikuyamikani inu, Atate, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti mwazibisira zinthu izi kwa anzeru ndi ozindikira ndipo mwaziululira kwa makanda. 26Indetu, Atate, pakuti zimenezi zakhala zokusangalatsani pamaso panu. 27Zinthu zonse zinaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga, ndipo palibe amene adziwa Mwana koma Atate, kapenanso alipo wina amene adziwa Atate, koma Mwana, komanso amene chamkomera Mwana kuti amuululire [iye]. 28Bwerani kwa Ine, nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupatsani inu mpumulo. 29Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; pakuti ndili ofatsa ndi odzichepetsa mu mtima; ndipo mudzapeza mpumulo ku miyoyo yanu; 30pakuti goli langa ndi losavuta, ndipo katundu wanga ndi wopepuka.