Mutu 11

1Mukadakhala kuti munapilira nane mu chopusa chochepa; komatu mundilole ine. 2Pakuti ndili nanu nsanje [imene ili] ya 1Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi ndi mwamuna m’modzi, kukuperekani [inu] namwali woyera mtima kwa Khristu. 3Koma ndichita mantha mwanjira iliyonse, monga njoka inanyenga Hava mwa kuchenjera kwake, [kotero] malingaliro anu angaonongeke kusiyana nako kuyera mtima monga kwa Khristu. 4Pakutidi ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitinalalikire, kapena mulandira Mzimu wosiyana, amene simunalandire, kapena uthenga wabwino wina wosiyana, umene simunaulandire, umene muulandira bwino lomwe. 5Pakuti ndizindikira mwanjira ina kuti sindinasalire mu kalikonse mwa iwo amene ali atumwi oposawo. 6Koma ngati ine ndili munthu wamba m’malankhulidwe, komabe wosakhala nacho chidziwitso, koma mu zonse kupanga choonadi kuonekera mu zinthu zonse kwa inu. 7Kodi ndachimwa ine, podzichepetsa ndekha cholinga kuti inu mukakwezedwe, chifukwa ndinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa 2Mulungu? 8Ndinasokoneza mipingo ina, polandira chuma pa utumiki wa kwa inu. 9Ndipo pakukhala nanu ndi kusowa, sindinachite mwa ulesi pofuna kulemetsa aliyense, (pakuti abale amene anabwera kuchokera ku Makedoniya anakwaniritsa zosowa zanga,) ndipo mu kalikonse ndinadziletsa ndekha kukhala chipsinjo kwa inu, ndipo ndidzazisunga ndekha. 10Choonadi cha Khristu chili mwa ine kuti kudzitamandira kumeneku kusaletsedwe monga kwa ine kumbali za Akaya. 11Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti ine sindimakukondani? 3Mulungu akudziwa. 12Komatu chimene ine ndichita, ndidzachichitanso, kuti ndikadule danga la iwo amene akufuna kupezerapo mpata, kuti pakudzitukumula iwo akapezeke monga ife tili. 13Pakuti oterewa ali atumwi onyenga, antchito achinyengo, kuzisanduliza okha kukhala atumwi a Khristu. 14Ndipo sizodabwitsa, pakuti Satana mwini amazisanduliza yekha kukhala mngelo wa kuunika. 15Sichinthu chovuta pamenepo kuti atumiki ake azisandulizenso okha monga atumiki a chilungamo; amene mapeto awo adzakhala monga mwa ntchito zawo.

16Ndinenanso ine, Wina aliyense asaganize kuti ndine wopusa; komatu ngati zili choncho, ndilandireni pamenepo ngati wopusawo, kutinso nane ndikazitamandire pang’ono. 17Chimene ndikulankhula sindikulankhula kolingana kwa Ambuye, koma monga mopusa, mu chilimbiko ichi cha kuzitamandira. 18Popeza ambiri amazitamandira molingana ndi thupi, inenso ndizitamandira. 19Pakuti inu muwavomereza opusa kukhala anthu a nzeru. 20Pakuti inu mumalola ngati munthu akutengerani ku ukapolo, ngati wina akukhadzulani, ngati wina atenga chuma chanu, ngati wina azitamandira yekha, ngati wina akumenyani pa nkhope. 21Ndilankhula ngati mopanda ulemu, ngati kuti ife tafooka; koma pamene wina alimbika mtima, (ndilankhula mopanda nzeru,) Inenso ndi wolimba mtima. 22Kodi ali Ahebri? Inenso. Kodi ali a Israyeli? Inenso. Kodi ali mbeu ya Abrahamu? Inenso. 23Kodi ali atumiki a Khristu? (Ndilankhula monga mosefukira) modutsa mlingo wake motero; m’zivutiko mochulukira kwambiri, m’mikwingwirima moonjeza, mu ndende moonjeza kwambiri, mu imfa kawirikawiri. 24Kwa Ayuda kasanu konse ndinalandira mikwingwirima makumi anayi, kuchotsapo umodzi. 25Katatu konse ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinagendedwa miyala, katatu ndinapulumuka pa ngozi ya bwato, usiku ndi usana ndinadutsa m’mayenje akuya: 26m’maulendo kawirikawiri, m’mitsinje yoopsa, m’chiopsezo cha achiwembu, m’chiopsezo cha mtundu wanga womwe, m’chiopsezo chochokera ku maiko, m’chiopsezo cha mumzinda, m’chiopsezo cha m’chipululu, m’chiopsezo cha panyanja, m’chiopsezo cha pakati pa abale achinyengo; 27m’chivutiko ndi m’cholemetsa, m’madikiro kawirikawiri, m’njala ndi m’ludzu, m’kusala kudya kawirikawiri, m’kuzizira ndi m’maliseche. 28Kupatulapo zinthu zimene zili kunja, mtambo wa zokhumba umene ukundisautsa ine tsiku ndi tsiku, zopsinja za mipingo yonse. 29Ndani amene ali ofooka, ndipo sindine ofooka? Ndani amene wakhumudwa, ndipo ine sindinapse mtima? 30Ngati kuli kofunikira kuzitamandira, ndikazitamandira pa zinthu zimene zikukhudza chifooko changa. 314Mulungu ndi Atate wa Ambuye Yesu akudziwa — iye amene ali wodalitsika kwamuyaya — kuti ine sindikunama. 32M’Damasiko kazembe wa mfumu Areta anasunga mzinda wa Adamasiko ukhale chete, nafuna kundigwira ine; 33ndipo kudzera pazenera mu mtanga ndinatsitsidwa pakhoma, ndipo ndinathawa m’manja mwake.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu