Mutu 1
1Chiyambi cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu1; 2monga kunalembedwa mu [Yesaya] mneneriyo, Taonani, Ine ndikutumizirani wa mthenga pamaso panu, amene adzakonza njira yanu. 3Mau a wofuula m’chipululu, Konzani njira ya Ambuye, pangani njira zake kukhala zoongoka.
4Anadza Yohane kubatiza m’chipululu, ndi kulalikira ubatizo wa kulapa pa kukhululukidwa kwa machimo. 5Ndipo anatuluka kwa iye onse aku madera a Yudeya, komanso iwo onse aku Yerusalemu, ndipo anabatizidwa ndi iye mu mtsinje wa Yordano, kuvomereza machimo awo. 6Ndipo Yohane amavala ubweya wa ngamila, ndi lamba wa chikopa m’chiuno mwake, ndipo amadya dzombe ndi uchi wa kuthengo. 7Ndipo iye analalikira, nanena, Akubwera pambuyo panga Iye amene ali wamphamvu kuposa ine, zingwe za nkhwayira zake sindili woyenera kugwada ndi kuzimasula. 8Ine ndakubatizanidi ndi madzi, koma Iye adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera.
9Ndipo kunachitika masiku amenewo [kuti] Yesu anabwera kuchokera ku Nazarete waku Galileya, ndipo anabatizidwa ndi Yohane ku Yordano. 10Ndipo nthawi yomweyo pokwera kuchokera m’madzi, iye anaona kumwamba kutatseguka pakati, ndipo Mzimu, monga nkhunda anatsikira pa Iye. 11Ndipo anadza mau kuchokera ku miyamba: Iwe ndi Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndapeza kukondwera kwanga.
12Ndipo pomwepo Mzimu anamtulutsa Iye napita m’chipululu. 13Ndipo Iye anali m’chipululu masiku makumi anayi akuyesedwa ndi Satana, ndipo anali pamodzi ndi zilombo za kuthengo; ndipo angelo anamtumikira Iye.
14Komatu pamene Yohane anaperekedwa, Yesu anabwera m’Galileya kulalikira uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu2, 15ndipo nanena, Nthawi yakwaniritsidwa ndipo ufumu wa Mulungu3 wayandikira; lapani ndi kukhulupilira uthenga wabwino.
16Ndipo pakuyenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya, Iye anaona Simoni, ndi Andreya, m’bale wake wa [Simoni], akuponya khoka m’nyanja, pakuti iwo anali asodzi. 17Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nditsateni Ine, ndipo ndidzakupangani inu kukhala asodzi a anthu; 18ndipo nthawi yomweyo pakusiya makhoka awo anamtsatira Iye. 19Ndipo pakuyenda pamenepo pang’ono, Iye anaona Yakobo [mwana] wa Zebedayo, ndi Yohane m’bale wake, ndipo iwowa [anali] m’ngalawa kusoka makhoka awo; 20ndipo nthawi yomweyo Iye anawaitana iwo; ndipo pakusiya atate awo m’ngalawamo pamodzi ndi antchito olembedwa, iwo anamtsatira Iye.
21Ndipo iwo anapita m’Kapernao. Ndipo nthawi yomweyo patsiku la sabata Iye analowa m’sunagoge ndipo anaphunzitsa. 22Ndipo iwo anali ozizwa ndi chiphunzitso chake, pakuti Iye anawaphunzitsa iwo monga wokhala ndi ulamuliro, ndipo osati ngati alembiwo. 23Ndipo analimo m’sunagoge mwao munthu [wogwidwa] ndi mzimu woipa, ndipo iye anafuula 24nanena, Eh! Kodi ife tikuchitireni chiyani inu, Yesu, m’Nazarayo? Kodi mwabwera kudzationonga ife? Inetu ndikudziwani inu, woyera wa Mulungu4. 25Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Khala bata ndipo tuluka mwa iye. 26Ndipo mzimu woipa, utamng’amba iye, ndi kulira ndi mau okuwa, unatuluka mwa iye. 27Ndipo onse anali odabwa, kotero kuti anafunsana pamodzi pakati pawo nanena, Ichi ndi chiyani? Chiphunzitso chatsopano chanji ichi? Pakuti ndi ulamuliro Iye alamulira ngakhale mizimu yoipa, ndipo imumvera Iye. 28Ndipo kudziwika kwake kunafikira nthawi yomweyo dera lonse la Galileya ndi madera ozungulira.
29Ndipo pomwepo pakutuluka m’sunagoge, iwo anabwera naye Yakobo ndi Yohane mnyumba ya Simoni ndi Andreya. 30Ndipo mpongozi wa mkazi wa Simoni anali gone wodwala malungo. Ndipo nthawi yomweyo iwo analankhula ndi Iye zokhudza mpongozi wa Simoniyo. 31Ndipo Yesu anapita kwa [iye] namdzutsa, ndipo atamugwira pa dzanja, nthawi yomweyo malungo anamuleka iye, ndipo iye anawatumikira iwo. 32Komatu pakufika madzulo, pamene dzuwa linalowa, iwo anabwera nawo kwa Iye iwo onse amene anali kuvutika, ndi iwo ogwidwa ndi ziwanda; 33Ndipo mzinda wonse unasonkhana pamodzi pa khomo. 34Ndipo Iye anachiritsa ambiri ovutika ndi nthenda zosiyanasiyana; ndipo anatulutsa ziwanda zambiri, ndipo sanazilole ziwandazo kuti zilankhule chifukwa izo zinamdziwa Iye.
35Ndipo m’bandakucha kusanache, Iye anatuluka napita ku malo a chipululu, ndipo kumeneko anapemphera. 36Ndipo Simoni ndi iwo amene anali naye pamodzi anamtsatira Iye: 37ndipo pamene anamupeza, iwo anati kwa Iye, Anthu onse akufunani Inu. 38Ndipo Iye anati kwa iwo, tiyeni tipite kumalo kwina kumidzi yoyandikana nafe, kuti Ine kumeneko ndikalalikirenso, pakuti chimenechi ndi cholinga chimene ndinabwerera Ine. 39Ndipo Iye anali kulalikira m’masunagoge awo m’Galileya yense, ndi kutulutsa ziwanda.
40Ndipo anadza naye kwa Iye wodwala khate, nampempha Iye, ndi kugwada pa maondo kwa Iye, ndi kunena kwa Iye, Ngati Inu mufuna mukhoza kundiyeretsa ine. 41Koma Yesu, pogwidwa ndi chifundo, potambasula dzanja lake, anamkhudza iye, ndipo anati kwa iye, Ndifuna, tayeretsedwa iwe. 42Ndipo pamene Iye amalankhula nthawi yomweyo khate linachoka mwa iye, ndipo iye anali woyeretsedwa. 43Ndipo pamene anamuuzitsa iye, nthawi yomweyo anamtumiza kwawo, 44ndipo anati kwa iye, Uwonetsetse kuti usauze munthu china chilichonse, koma upite, ukadziwonetsere wekha kwa wansembe, ndipo ukapereke cha mayeretsedwe ako chimene Mose anakhazikitsa, chikakhale umboni kwa iwo. 45Koma iye, pamene anapita, anayamba kuchilalika [ichi] kwambiri, ndipo anabukitsa nkhaniyi paliponse, kotero kuti Iye sakanathanso kulowa mowonetsera mu mzindawo, koma anakhala malo a chipululu, ndipo iwo anadza kwa Iye kuchokera mbali zonse.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu