Mutu 12

1Pamenepo ndikudandaulirani abale, mwa zifundo za Mulungu1, mupereke matupi anu nsembe ya moyo, yoyera, yovomerezeka kwa Mulungu2, [imene ili] kutumikira kwanu kwa nzeru.2Ndipo musafanizidwe ndi dziko ili lapansi, koma musandulike pokonzanso malingaliro anu, kuti mukazindikire chifuniro chabwino ndi chovomerezeka ndi changwiro cha Mulungu3.3Pakuti ine ndinena, kudzera mu chisomo chimene chapatsidwa kwa ine, chopita kwa aliyense amene ali pakati panu, kuti musalingalire mopyola zimene mukuyenera kuganiza; koma ganizirani kotero monga anthu a nzeru, monga Mulungu4 achitira ndi mlingo wa chikhulupiliro.4Pakuti, monga tili nazo ziwalo zambiri, koma ziwalozo sizili nayo ntchito yofanana;5kotero ife, [pokhala] ambiri, ndife thupi limodzi mwa Khristu, ndipo chiwalo chilichonse chalumikizika ku chinzake.6Koma pokhala nazo mphatso zosiyanasiyana, molingana ndi chisomo chimene chapatsidwa kwa ife, kaya [ukhale] uneneri, [tiyeni tinenere] molingana ndi chikhulupiliro choperekedwa;7kapena utumiki, [tiyeni tidzipereke tokha] mu utumiki; kapena iye amene amaphunzitsa, adzipereke mu kuphunzitsa;8kapena iye amene amalimbikitsa, adzipereke mu kulimbikitsa; iye wopereka, apereke modzichepetsa; iye wotsogolera, atsogolere mosamalitsa; iye amene amaonetsera chifundo, awonetsere mokondwera.9Chikondi chikhale chopanda chinyengo; dana nacho choipa; kakamira chabwino:10monga mwa chikondi cha pa abale, lemekezanani wina ndi mzake: monga kuchitirana ulemu, potsogolerana kuchita ichi pa wina ndi mzake:11monga mokondwera mwachangu, osakhala aulesi; mu mzimu wa changu; potumikira Ambuye.12Kulingana ndi chiyembekezo, kukondwera: kulingana ndi msautso, chipiliro: kulingana ndi pemphero, kulimbikabe:13kugawira zosoweka za abale; kuzipereka ku kuchereza alendo.14Dalitsani iwo akuzunza inu; adalitseni, ndipo musawatembelere.15Sangalalani nawo amene akusangalala, lirani ndi iwo amene akulira.16Lemekezanani wina ndi mzake, osakhumba zinthu zapamwamba, koma phatikanani ndi anthu wamba: musakhale a nzeru pa inu nokha:17musabwenzere choipa ku choipa: perekani zinthu za chilungamo kwa anthu onse:18ngati nkutheka, monga mwa kuthekera kwanu, khalani mu mtendere ndi anthu onse;19osabwenzerana choipa pa inu nokha, okondedwa, patukani ku mkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera ndi kwanga, ndidzabwenzera, atero Ambuye.20Pamenepo ngati mdani wako akumva njala, mdyetse; ngati akumva ludzu, mpatse madzi akumwa; pakuti pochita izi, mumuunjikira makala a moto pamutu pake.212Musagonjetsedwe ndi choipa, koma gonjetsani choipa ndi chabwino.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu