Mutu 13
1Kachitatu aka ndikubwera kwa inu. Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu kanthu kalikonse kakhazikitsidwa. 2Ndinanena kale pachiyambi, ndipo ndinenanso ndisanafike monga tsopano kachiwiri, ndipo tsopano pokhala ine palibe, kwa iwo amene anachimwa pachiyambi, ndi kwa ena onse, kuti ngati ndifikanso sindidzawasiya. 3Popeza mufuna chitsimikizo cha Khristu akulankhula mwa ine, (amene siofooka pa inu, koma ali ndi mphamvu pakati panu, 4pakuti ngatidi anapachikidwa m’chifooko, ndipo akhala ndi moyo mwa mphamvu ya 1Mulungu; pakuti ngatidi tili ofooka mwa Iye, koma tidzakhala ndi Iye mwa mphamvu ya 2Mulungu pa inu,) 5Dziyeseni nokha ngati muli m’chikhulupiliro; dzitsimikizireni nokha: kodi simutha kuzizindikira nokha, kuti Yesu Khristu ali mwa inu, pokhapokhadi ngati muli osatsimikizidwa? 6Tsopano ndiyembekezera kuti mudziwa kuti sitili osatsimikizika. 7Koma tipemphera kwa 3Mulungu kuti musachite kanthu koipa; osati kuti tikapezeke ovomerezeka, koma kuti mukachite chimene chili choyenera, ndipo ife tikhala monga osatsimikizika. 8Pakuti palibe chimene tingapange motsutsana ndi choonadi, koma kuvomereza choonadi. 9Pakuti ife tikondwera pamene tikhala ofooka ndipo inu mukhala amphamvu. Komanso ichi tipempherera, ndicho ungwiro wanu. 10Pachifukwa ichi ndilemba zinthu izi pokhala ine palibepo, kuti popezeka ine ndisagwiritse ntchito moonjeza molingana ndi ulamuliro umene Mulungu anandipatsa kumangilira, ndipo osati kugwetsa.
11Chotsalira abale, kondwerani; muchitidwe ungwiro; mulimbikitsidwe; khalani a mtima umodzi; khalani mu mtendere; ndipo 4Mulungu wa chikondi adzakhala ndi inu. 12Lonjeranani wina ndi mzake ndi chipsopsono chopatulika. 13Oyera mtima onse akukulonjerani. 14Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha 5Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera, zikhale ndi inu nonse.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu