Mutu 1

1Popeza ambiri anayesa kulongosola zinthu zimene zinakhulupiridwa pakati pathu, 2kuyambira iwo amene pachiyambi anali mboni komanso atumiki a Mau operekedwa kwa ife, 3zaonekanso zabwino kwa ine, kulondalonda mosamalitsa kuchokera pachiyambi ndi zinthu zonse, kulembera kwa iwe mwa ndondomeko, Teofilo wabwino kwambiri, 4kuti ukathe kudziwa zoona zake za zinthu zimene iwe unalangizidwa.

5Kunali mmasiku a Herode, mfumu ya Yudeya, wansembe wina, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya, ndi mkazi wake wa ana akazi a Aroni, ndipo dzina lake Elizabeti. 6Ndipo iwo onse awiri anali olungama pamaso pa Mulungu1, nayenda mmalamulo onse ndi zoikika za Ambuye mwangwiro. 7Ndipo iwo analibe mwana, chifukwa Elizabeti anali wosabereka, ndipo onse awiri anali okalamba. 8Ndipo kunachitika kuti pamene iye amakwaniritsa utumiki wa unsembe pamaso pa Mulungu2 monga mwa ndondomeko ya utumiki wake, 9adamgwera iye mayere, molingana ndi chikhalidwe cha unsembe, kulowa mkachisi wa Ambuye kukafukiza. 10Ndipo khamu lonse la anthu linali kupemphera kunja kwa ola la zofukiza. 11Ndipo mngelo wa Ambuye anawonekera kwa iye, atayima kumanja kwa guwa la zofukiza. 12Ndipo Zakariya anavutika, pakumuona [iye], ndipo mantha anamugwira. 13Koma mngelo anati kwa iye, Usachite mantha, Zakariya, chifukwa pemphero lako lamveka, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakuberekera iwe mwana wa mwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane. 14Ndipo iye adzakhala chimwemwe kwa iwe ndi kusangalala, ndipo ambiri adzakondwera pakubadwa kwake. 15Pakuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena chakumwa chaukali; ndipo adzakhala wodzadzidwa ndi Mzimu Woyera, ngakhale mmimba mwa mayi wake. 16Ndipo ambiri a ana a Israyeli iye adzawatembenuzira kwa Mulungu3 Ambuye wawo. 17Ndipo iye adzatsogozedwa ndi mzimu komanso mphamvu ya Eliya, kutembenuza mitima ya atate kwa ana, ndi osamverawo ku malingaliro a [anthu] olungama, kuwapanga kukhala okonzeka kwa Ambuye, anthu okonzeka. 18Ndipo Zakariya anati kwa mngelo, Ndizadziwa bwanji zimenezi, ndine munthu wokalamba, ndipo mkazi wanga zaka zake ndi zochuluka? 19Ndipo poyankha mngelo anati kwa iye, Ndine Gabrieli, amene ndimaima pamaso pa Mulungu4, ndipo ndatumidwa kulankhula kwa iwe, ndi kubweretsa uthenga wabwinowu kwa iwe; 20ndipo taona, iwe udzakhala chete ndipo sudzakwanitsanso kulankhula, kufikira tsiku limene zinthu izi zidzachitika, chifukwa iwe sunakhulupilire mau anga, amene adzakwaniritsidwa mu nthawi yake. 21Ndipo anthu anali kumudikira Zakariya, ndipo iwo anali odabwa ndi kuchedwa kwake mkachisimo. 22Koma pamene anatuluka sanathenso kulankhula kwa iwo, ndipo iwo anadziwa kuti iye waona masomphenya mkachisimo. Ndipo iye amangopereka zizindikiro kwa iwo, nakhalabe wosalankhula. 23Ndipo zinachitika kuti pamene masiku ake otumikira anali atatha, ananyamuka kupita kunyumba kwake.

24Tsopano atapita masiku amenewa, Elizabeti mkazi wake anayima, ndipo iye anabisa kwa miyezi isanu, nanena, 25Wandichitira chotero Ambuye mmasiku [ano] pamene wandiona [ine] kundichotsera chitonzo changa pakati pa anthu. 26Komatu mwezi wa chisanu ndi chimodzi, mngelo Gabrieli anatumidwa ndi Mulungu5 ku mzinda wa Galileya, umene dzina lake [unali] Nazareti, 27kwa namwali amene anatomeredwa kwa munthu amene dzina lake [linali] Yosefe, wanyumba ya Davide; ndipo dzina la namwaliyo [linali] Mariya. 28Ndipo mngelo anadza kwa iye, nanena, Tikuone, [iwe] munthu wokonderedwa! Ambuye ali ndi iwe: [wodala ndi iwe pakati pa akazi onse]. 29Koma iye, [pakuona] [mngelo], anavutika pa mau akewa, ndipo anaganiza mwa iye yekha kuti malonje amenewa ndi otani. 30Ndipo mngelo anati kwa iye, Usaope, Mariya, pakuti wapeza chisomo ndi Mulungu6; 31ndipo taona, udzayima mmimba mwako ndi kubereka mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu. 32Iye adzakhala wamkulu, ndipo adzatchedwa Mwana wamwamuna wa Wammwambayo; ndipo Ambuye Mulungu7 adzampatsa Iye ufumu wa Davide atate Wake; 33ndipo adzalamulira pa nyumba ya Yakobo ku nthawi zonse, ndipo ufumu wake udzakhala wopanda malekezero. 34Koma Mariya anati kwa mngelo, Kodi zimenezi zidzatheka bwanji pakuti ine sindidziwa mwamuna? 35Ndipo mngelo poyankha anati kwa iye, Mzimu Woyera adzabwera pa iwe, ndipo mphamvu ya Wammwambayo idzakuphimba iwe, pamenepo choyeracho chimene chidzabadwa chidzatchedwa Mwana wa Mulungu8. 36Ndipo taona, Elizabeti, mbale wako, iyenso wayima mu ukalamba wake, ndipo mwezi uno ndi wachisanu ndi chimodzi kwa iye chimenechi chinatchedwa kusabereka: 37pakuti palibe chinthu chomulaka Mulungu9. 38Ndipo Mariya anati, Taonani mdzakazi wa Ambuye; chichitike molingana ndi mau anu. Ndipo mngelo anachoka kwa iye.

39Ndipo Mariya, ponyamuka mmasiku amenewo, anapita kudziko la kumapiri ndi changu, mu mzinda wa Yudeya, 40ndipo analowa mnyumba ya Zakaliya, namlonjera Elizabeti. 41Ndipo kunachitika kuti pamene Elizabeti anamva kulonjeredwa kwa Mariya, mwana anatakataka mmimba mwake; ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, 42ndipo anafuula ndi mau akulu nanena, Uli wodala iwe pakati pa akazi onse, ndipo chodala chipatso cha mmimba mwako. 43Ndipo chichokera kuti ichi kwa ine, kuti mayi wa Ambuye wanga adze kwa ine? 44Pakuti taonani, pamene mau ako a malonje anamveka mmakutu mwanga, mwana anatakataka ndi chimwemwe mmimba mwanga. 45Ndipo ndi wodala iye amene akhulupilira, pakuti kudzakhala kukwaniritsidwa kwa zinthu zolankhulidwa kwa iye kuchokera kwa Ambuye.

46Ndipo Mariya anati, Moyo wanga ulemekeza Ambuye, 47ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu10 Mpulumutsi wanga. 48Pakuti Iye wayanganira umphawi wa mdzakazi wake; pakuti taonani, kuyambira pano mitundu yonse idzanditchula ine wodalitsika. 49Pakuti Wamphamvuyonse wandichitira ine zinthu zazikulu, ndipo dzina lake ndi loyera; 50ndipo chifundo chake [chili] mibadwo mibadwo kwa iwo amene amuopa Iye. 51Iye wachita za mphamvu ndi dzanja lake; wabalalitsa odzitama mu lingaliro la mtima wawo. 52Iye watsitsa olamulira pa mipando yawo, ndipo wakweza aumphawi. 53Iye wakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino, ndipo wachotsa achuma opanda kanthu. 54Iye wathandiza Israyeli mtumiki wake, kuti akakumbukire chifundo, 55 (monga Iye analankhula kwa makolo athu,) kwa Abrahamu ndi mbewu yake ku nthawi zonse. 56Ndipo Mariya anakhala ndi iye ngati miyezi itatu, nabwerera kunyumba kwake.

57Koma nthawi inakwana kwa Elizabeti kuti abereke, ndipo anabereka mwana wa mwamuna. 58Ndipo anansi ake ndi abale ake anamva kuti Ambuye anakulitsa chifundo chake kwa iye, ndipo anakondwera naye pamodzi. 59Ndipo kunachitika kuti tsiku lachisanu ndi chitatu iwo anadza kudzamdula mwanayo, ndipo anamtchula dzina la atate wake, Zakaliya. 60Ndipo mayi wake poyankha anati, Ayi; koma adzatchedwa Yohane. 61Ndipo anati kwa iye, Palibe mwa abale ako amene amatchedwa ndi dzina limeneli. 62Ndipo iwo anapereka chizindikiro kwa atate wake kuti akufuna mwanayo atchulidwe ndani. 63Ndipo atapempha polembapo, analemba kuti, Yohane ndilo dzina lake. Ndipo onse anali odabwa. 64Ndipo pakamwa pake panatseguka nthawi yomweyo, ndi lilime lake, ndipo iye analankhula, adalitsike Mulungu11. 65Ndipo mantha anagwira onse amene anazungulira iwo; ndipo dziko lonse la mapiri la Yudeya imeneyi inali nkhani imene amakambirana. 66Ndipo onse amene anawamva iwo anazisunga mu mtima mwawo, nanena, Kodi mwana ameneyu adzakhala wotani? Ndipo dzanja la Ambuye linali naye.

67Ndipo Zakariya atate wake anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nanenera, nati, 68Alemekezeke Ambuye Mulungu12 wa Israyeli, chifukwa wayendera ndi kupereka chiombolo cha anthu ake, 69ndipo watikwezera ife nyanga ya chipulumutso mnyumba mwa Davide mtumiki wake; 70monga analankhulira ndi kamwa la aneneri ake oyera, amene anakhalako chiyambire cha dziko lapansi; 71chipulumutso kuchoka kwa adani athu ndi kudzanja la iwo onse akudana nafe; 72kukwaniritsa chifundo ndi makolo athu ndi kukumbukira pangano lake loyera, 73lumbiro limene analumbira kwa Abrahamu kholo lathu, 74kutipatsa ife, kuti, titalanditsidwa mdzanja la adani athu, tikamutumikire Iye ndi mantha 75mchiyero ndi mchilungamo pamaso pake masiku athu onse. 76Ndipo iwe, mwanawe, udzatchedwa mneneri wa Wammwamba; pakuti udzapita pamaso pa Ambuye kukonzekeretsa njira zake; 77kupereka chidziwitso cha chipulumutso kwa anthu ake mwa kukhululukidwa kwa machimo awo 78potengera mkatikati mwa chifundo cha Mulungu13 wathu; mmenemo mbandakucha wa mmwamba watiyendera ife, 79kuwalira iwo amene anakhala mu mdima komanso mu mthunzi wa imfa, kutsogolera mapazi athu munjira ya mtendere.

80Ndipo mwana anakula nalimbikitsidwa mu mzimu; ndipo iye anakhala mchipululu kufikira tsiku lowonetsedwa kwa Israyeli.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu12Elohimu 13Elohimu