Mutu 4

1Ine ndichitira umboni pamaso pa Mulungu1 ndi Khristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa, ndi pakuonekera kwake komanso ufumu wake, 2lalikira mau;chita nawo pa nthawi yake [ndi] posakhala nthawi yake, tsutsa, dzudzula, limbikitsa, ndi kupilira konse ndi chiphunzitso. 3Pakuti nthawi idzafika imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa; koma molingana ndi zilaolako zawo azaziunjikira okha aphunzitsi, pokhala nalo khutu loyabwa; 4ndipo iwo adzachotsa khutu lawo ku choonadi, ndipo adzapatukira kutsata nthano chabe. 5Koma iwe, khala tcheru mu zinthu zonse, imva zowawa, gwira ntchito ya mlaliki, kwaniritsa mlingo onse wa utumiki wako. 6Pakuti ndaperekedwa kale ngati nsembe, ndipo nthawi yakumasulidwa kwanga yafika. 7Ine ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro. 8Kuyambira pano korona wa chilungamo wayikidwa pa ine, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzapereka kwa ine m’tsiku limenelo; koma osati kwa ine ndekha, komanso kwa onse amene akonda maonekedwe ake. 9Chita khama kuti ubwere kwa ine mwachangu; 10pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi, ndipo wapita ku Tesalonika; Kresike ku Galatiya, Tito ku Dalimatiya. 11Luka yekha ali ndi ine. Umtenge Maliko, ndipo ubwere naye pamodzi ndi iwe, pakuti iyeyo ndi wofunikira kwa ine pa utumiki. 12Koma Tukiko ndamtuma ku Efeso. 13Chofunda chimene ndinachisiya m’Trowa ku Karpo, uchitenge pamene ukubwera, ndi mabuku, makamaka zikopa zolembapo. 14Alesandro wosula zitsulo anandichitira zinthu zambiri zoipa. Ambuye adzam’bwezera iye molingana ndi ntchito zake. 15Ameneyu iwenso usamale naye, pakuti anatsutsana ndi mau athu. 16Kudzikanira kwanga koyamba palibe munthu amene anayima nane, koma onse anandithawa ine. 17Koma Ambuye anayima nane, ndipo anandipatsa mphamvu, kuti mwa ine kulalikira kuchitike kwathunthu, ndipo onse a mitundu akamve; ndipo ndinalanditsidwa mkamwa mwa mkango. 18Ambuye adzandilanditsa ine ku ntchito iliyonse yoipa, ndipo adzandisunga ine mu ufumu wake wakumwamba; kwa ameneyo kukhale ulemelero kwa nthawi za nthawi. Amen.

19Umlonjere Priska and Akula, ndi banja la Onesifolo. 20Erasto anatsalira m’Korinto, koma Trofimo ndinamusiya m’mbuyo m’Melito ali wodwala. 21Chita khama kubwera isanafike nyengo yozizira. Eubulo akukulonjera, ndi Pude, ndi Lino, ndi Klaudiya ndi abale onse. 22 Ambuye Yesu Khristu akhale ndi mzimu wako. Chisomo chikhale ndi iwe.

1Elohimu