Mutu 16

1Ndipo ndinamva mau akulu ochokera ku kachisi, akunena kwa angelo asanu ndi awiri aja, Pita ndipo ukakhutulire mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu1 padziko lapansi.

2Ndipo woyamba anapita nakhutulira mbale yake padziko lapansi; ndipo panadza chilonda choipa ndi chopweteka pa anthu amene anali ndi chizindikiro cha chirombo chija, ndi iwo amene analambira chifanizo chake.

3Ndipo wachiwiri anakhutulira mbale yake panyanja; ndipo inakhala ya mwazi, monga wa munthu wakufa; ndipo chamoyo chilichonse chinafa m’nyanja.

4Ndipo wachitatu anakhutulira mbale yake pa mitsinje, ndi [pa] akasupe a madzi; ndipo anasandulika mwazi. 5Ndipo ndinamva mngelo wa madzi akunena, Ndinu wolungama, amene muli ndipo munali, woyera, kuti munaweruza kotero; 6pakuti iwo akhutulira mwazi wa oyera mtima ndi aneneri, ndipo inu munawapatsa iwo mwazi kuti amwe; ayenera iwo. 7Ndipo ndinamva guwa likunena, Inde, Ambuye Mulungu2 Wamphamvuzonse, oona ndi olungama maweruzo anu.

8Ndipo wachinayi anakhutulira mbale yake padzuwa; ndipo analipatsa ilo kuti litenthe anthu ndi moto. 9Ndipo anthu anatenthedwa ndi kutentha kwakukulu, ndipo anachitira mwano dzina la Mulungu3, amene anali ndi ulamuliro pa milili yonseyi, ndipo sanalape kumpatsa iye ulemelero.

10Ndipo wachisanu anakhutulira mbale yake pa mpandowachifumu wa chirombocho; ndipo ufumu wake unadetsedwa; ndipo iwo anatafuna malilime awo mwa ululu, 11ndipo anachitira mwano Mulungu4 wakumwamba chifukwa cha ululu wao ndi zilonda zawo, ndipo sanalape chifukwa cha ntchito zawo.

12Ndipo wachisanu ndi chimodzi anakhutulira mbale yake pa mtsinje waukulu wa Firate; ndipo madzi ake anaphwera, kuti njira za mafumu kuchokera pakutuluka kwa dzuwa zikakonzedwe. 13Ndipo ndinaona mukutuluka kuchoka mkamwa mwa chinjoka, ndi kuchoka mkamwa mwa chirombo, ndi kutuluka mkamwa mwa mneneri wonyenga, mizimu yoipa itatu, monga achule; 14pakuti inali mizimu ya ziwanda, kuchita zizindikiro; imene imatuluka kupita kwa mafumu adziko lonse lapansi kuwasonkhanitsa iwo pamodzi kuchita nkhondo patsiku lalikulu limenelo la Mulungu5 Wamphamvuzonse. 15(Taonani, ndibwera ngati wakuba. Wodala [ali] iye wakuyang’anira ndi kusunga zovala zake, kuti asayende wa maliseche, ndi kuti iwo [asathe] kuona manyazi ake.) 16Ndipo anawasonkhanitsa pamodzi kumalo otchedwa m’Chiheberi, Armagedoni.

17Ndipo wachisanu ndi chiwiri anakhutulira mbale yake mlengalenga; ndipo panatuluka mau akulu kuchokera m’kachisi wakumwamba, kuchokera pa mpandowachifumu, akunena, Chachitika. 18Ndipo panali mphenzi, ndi mau, ndi mabingu; ndipo panali chivomezi chachikulu, chimene sichinachitikepo chiyambire munthu kukhala padziko lapansi, chivomezi chachikulu zedi. 19Ndipo mzinda waukulu [unagawika] m’magawo atatu; ndipo mizinda ya mafuko inagwa: ndipo Babulo wamkuluyo anakumbukirika pamaso pa Mulungu6 kumpatsa chikho cha vinyo wa ukali ndi mkwiyo wake. 20Ndipo chisumbu chilichonse chinathawa, ndipo mapiri sanapezeke; 21 Ndipo matalala akulu, monga kulemera kwa talenti, anatsika kuchoka kumwamba kutsikira pa anthu; ndipo anthu ananenera mwano Mulungu7 chifukwa cha mlili wa matalala, pakuti mlili wake unali waukulu koposa.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu