Mutu 2

1Ndipo analowanso m’kapernao masiku [angapo], ndipo kunadziwika kuti Iye anali m’nyumba; 2ndipo nthawi yomweyo anthu ambiri anasonkhana pamodzi, kotero kuti panalibenso malo ngakhale pakhomo; ndipo Iye analankhula mau kwa iwo. 3Ndipo anadza kwa Iye [amuna] nabweretsa wa manjenje wonyamulidwa ndi anthu anayi; 4ndipo pakulephera kufika pafupi ndi Iye chifukwa cha khamulo, iwo anasasula denga la nyumbayo pamene Iye anayima, ndipo atalibowola [ilo] anatsitsira pansi mphasa imene anagonekapo wa manjenjeyo. 5Koma Yesu, pakuona chikhulupiliro chao, anati kwa wa manjenjeyo, Mwanawe, machimo ako akhululukidwa [iwe]. 6Komatu ena mwa alembi anali kukhala pamenepo, ndi kulingalira m’mitima mwao, 7Chifukwa chiyani [munthu] uyu alankhula chonchi? Iyeyu akuchitira mwano Mlengi. Ndani wina amene akhoza kukhululukira machimo koposa Mulungu1 yekha? 8Ndipo nthawi yomweyo Yesu, podziwa mu mzimu mwake kuti akulingalira izi pakati pawo, anati kwa iwo, Chifukwa chiyani mukulingalira izi m’mitima mwanu? 9Chapafupi ndi chiti, kunena kwa wamanjenjeyu, Machimo [ako] akhululukidwa [iwe]; kapena kunena, Dzuka, ndipo tenga mphasa yako nuyende? 10Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali nayo mphamvu padziko lapansi ya kukhululukira machimo, Iye anati kwa wamanjenjeyo, 11Kwa iwe ndinena, tenga mphasa yako ndi kupita kunyumba kwako. 12Ndipo anauka nthawi yomweyo, ndipo pamene anatenga mphasa yake anatuluka pamaso pa [iwo] onse, kotero kuti onse anali ozizwa, ndipo analemekeza Mulungu2, nanena, Ife sitinaoneko zotere.

13Ndipo Iye anatulukanso kupita kunyanja, ndipo khamu lonse linabwera kwa Iye, ndipo Iye anawaphunzitsa iwo. 14Ndipo podutsapo, Iye anaona Levi [mwana] wa Alifeyu atakhala pa nyumba yolandilira msonkho, ndipo anati kwa Iye, nditsatire Ine. Ndipo iye anadzuka namtsatira Iye. 15Ndipo zinachitika kuti Iye anakhala pagome m’nyumba mwake, kotero kuti okhometsa msonkho ambiri ndi ochimwa anakhala pagome pamodzi ndi Yesu komanso ophunzira ake; popeza anali ambiri, ndipo iwo anamtsatira Iye. 16Ndipo alembi ndi Afarisi, pakumuona Iye ali mkudya pamodzi ndi ochimwa komanso okhometsa msonkho, anati kwa ophunzira ake, Chifukwa chiyani [zili chonchi] kuti Iye akudya ndi kumwa pamodzi ndi okhometsa msonkho komanso ochimwa? 17Ndipo Yesu pakumva [ichi] anati kwa iwo, Iwo amene ali amphamvu samafuna sing’anga, komatu iwo amene ali odwala. Inetu sindinabwere kudzaitana [anthu] olungama, komatu ochimwa.

18Ndipo ophunzira a Yohane ndi Afarisi anali kusala kudya; ndipo iwo anafika nati kwa Iye, Chifukwa chiyani ophunzira a Yohane komanso [ophunzira] a Afarisi asala kudya, koma ophunzira anu sakusala kudya? 19Ndipo Yesu anati kwa iwo, Kodi anyamata a nyumba ya ukwati akhoza kusala kudya pamene mkwati ali nawo? Pokhapokha pamene mkwati ali pamodzi ndi iwo sangasale kudya. 20Koma masiku adzafika pamene mkwati adzachotsedwa pakati pawo, ndipo pamenepo iwo adzasala kudya tsiku limenelo. 21Palibe amene amasoka chigamba chatsopano pa chovala chakale: zotsatira zake chigamba chatsopanocho chimazumuka pa [chovala] chakale, ndipo chimang’ambika kuposa kale. 22Ndipo palibe amene amaika vinyo watsopano m’zotengera zachikopa zakale; zotsatira zake vinyoyo amaphulitsa zotengerazo, ndipo vinyoyo amatayika, ndipo zotengerazo zimaonongeka; komatu vinyo watsopano akuyenera kuikidwa m’zotengera zachikopa zatsopano.

23Ndipo zinachitika kuti Iye anali kuyenda pa sabata m’minda ya tirigu; ndipo ophunzira ake anayamba kuyenda ndi kubudula ngala zake. 24Ndipo Afarisi anati kwa Iye, Taonani, chifukwa chiyani pa sabata iwowa akuchita chinthu chosaloledwa? 25Ndipo Iye anati kwa iwo, Kodi simunawerenge zimene Davide anachita pamene anamva njala, iye pamodzi ndi iwo amene anali naye, 26m’mene analowa m’nyumba ya Mulungu3, mu [chipinda cha] Abyatara mkulu wansembe, nadya mkate woonetsera, umene sunali wololedwa kudyedwa pokhapokha wansembe yekha, ndipo iye anapatsanso iwo amene anali naye? 27Ndipo Iye anati kwa iwo, Sabata linapangidwa chifukwa cha munthu, osati munthu kupangidwa chifukwa cha sabata; 28kotero kuti Mwana wa munthu ndiyenso mbuye wa sabata.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu