Mutu 9
1Ndipo pamene Iye amayenda, anaona munthu wakhungu chidabwire. 2Ndipo ophunzira ake anamfunsa Iye, nanena, Rabi, anachimwa ndani, [munthu] uyu kapena makolo ake, kuti abadwe wakhungu? 3Yesu anayankha, Sanachimwe [munthu] uyu kapena makolo ake, koma kuti ntchito za Mulungu1 zionetsedwe mwa iye. 4Ine ndikuyenera kugwira ntchito za Iye amene anandituma udakali msana. Usiku ukubwera, umene munthu sangagwire ntchito. 5Pamene ndili m’dziko lapansi, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi. 6Atalankhula zinthu izi, Iye analavulira pansi napanga thope ndi malovuwo, ndipo anapaka thopelo, ngati mafuta, m’maso mwake. 7Ndipo anati kwa iye, Pita, ukasambe m’thamanda la Siloamu, limene limatanthauza, Wotumidwa. Pamenepo iye anapita ndi kukasamba, ndipo anabwera akupenya. 8Pamenepo anansi, ndi iwo amene anamuona poyamba, kuti anali wopempha, anati, Kodi uyu siuja amakhala ndi kupempha? 9Ena anati, Ndi yemweyu; ena anati, Ayi, koma angofanana: iye anati, Ndine amene. 10Pamenepo iwo anati kwa iye, Kodi maso ako atsegulidwa bwanji? 11Iye anayankha [ndipo anati], Munthu wotchedwa Yesu anakanya thope ndi kupaka m’maso mwanga, ndipo anati kwa ine, Pita ku Siloamu ndipo ukasambe: ndipo nditapita kukasamba, ine ndinapenya. 12Pamenepo iwo anati kwa iye, Ali kuti? Iye anati, Sindikudziwa.
13Iwo anamutengera iye amene anali wakhungu poyambayo kwa Afarisi. 14Tsopano linali la sabata pamene Yesu anakanya thope ndi kutsegula m’maso mwake. 15Pamenepo Afarisi anamufunsanso iye momwe analandilira kuona kwake. Ndipo iye anati kwa iwo, Anayika thope m’maso mwanga, ndinasamba, ndipo ndinapenya. 16Ena mwa Afarisi pamenepo anati, Munthu ameneyu siwa Mulungu2, pakuti sasunga sabata. Ena anati, Zitheka bwanji munthu wochimwa kuchita zizindikiro zotere? Ndipo panali kugawikana pakati pawo. 17Pamenepo iwo anatinso kwa [munthu] wakhungu, Kodi iwe unena chiyani za Iye, kuti watsegula maso ako? Ndipo anati, Iye ndi mneneri. 18Pamenepo Ayuda sanakhulupilire zokhudza iye kuti anali wakhungu ndipo wapenya, kufikira anayitana makolo ake a iye amene analandira kuonayo. 19Ndipo anawafunsa iwo nanena, Uyu ndi mwana wanu, amene mukuti anabadwa wakhungu: kodi zakhala bwanji kuti tsopano apenye? 20Makolo ake anawayankha [iwo] ndipo anati, Ife tikudziwa kuti uyu ndi mwana wathu, ndipo kuti anabadwa wakhungu; 21koma momwe anapenyera sitikudziwa, komanso amene anatsegula naso ake sitikumudziwa. Iyeyu ndi wamkulu: mfunseni; adzilankhulira yekha zokhudza iye mwini. 22Makolo ake analankhula izi chifukwa anaopa Ayuda, pakuti Ayuda anali atagwirizana kale kuti ngati aliyense adzamvomereza Iye [kukhala] Khristu, achotsedwe ku sunagoge. 23Pa chifukwa chimenechi makolo ake anati, Iyeyu ndi wamkulu: mfunseni.
24Pamenepo iwo anamuyitana kachiwiri munthu amene anali wakhunguyo, ndipo anati kwa iye, Lemekeza Mulungu3: ife tikudziwa kuti munthu uyu ndi wochimwa. 25Pamenepo iye anayankha, Ngati ndi wochimwa ine sindikudziwa. Chinthu chimodzi chimene ine ndikudziwa, ndinali wakhungu [poyamba], tsopano ndikupenya. 26Ndipo iwo anatinso kwa iye, Anachita chiyani kwa iwe? Kodi anatsegula bwanji maso ako? 27Iye anawayankha iwo, Ine ndakuuzani kale ndipo simunandimvere: chifukwa chiyani mukufuna kumvanso? Kodi mukufuna kukhala ophunzira ake? 28Iwo anamukalipira iye, nati, Iwe ndi ophunzira wake, koma ifeyo ndi ophunzira a Mose. 29Ife tikudziwa kuti Mulungu4 analankhula kwa Mose; koma monga kwa [munthu] uyu, sitidziwa kumene Iye achokera. 30Munthuyo anayankha nati kwa iwo, Tsopano mu ichi muli chinthu chodabwitsa, kuti inu simudziwa kumene akuchokera, ndipo Iye watsegula maso anga. 31[Koma] ife timadziwa kuti Mulungu5 samamvera ochimwa; koma ngati wina akhala woopa Mulungu6 nachita chifuniro chake, ameneyo Iye amumvera. 32Kuyambira pachiyambi, sizinamvekeko kuti wina anatsegula maso a munthu wakhungu chibadwire. 33Ngati [munthu] uyu sanali wa Mulungu7 sakanatha kuchita kanthu kalikonse. 34Iwo anayankha nati kwa iye, Iwe unabadwa kwathunthu m’machimo, ndipo ufuna utiphunzitse ife? Ndipo iwo anamtulutsa iye kunja.
35Yesu anamva kuti anamtulutsa iye kunja, ndipo atamupeza, anati kwa iye, Kodi iwe ukhulupilira pa Mwana wa Mulungu8? 36Iye anayankha nati, Ndipo ameneyu ndi uti, Ambuye, kuti ndimkhulupilire Iye? 37Ndipo Yesu anati kwa iye, Mwamuona nonse Iye, ndipo amene akulankhula ndi iwe ndi yemweyo. 38Ndipo iye anati, Ndikhulupilira, Ambuye: ndipo anamgwadira Iye.
39Ndipo Yesu anati, Kudzaweruza Ine ndabwera m’dziko lapansili, iwo amene ali akhungu apenye, ndipo iwo amene ali openya akhale akhungu. 40Ndipo [ena] mwa Afarisi amene anali naye pamodzi anamva zinthu izi, ndipo iwo anati kwa Iye, Ifenso ndife akhungu? 41Yesu anati kwa iwo, Mukanakhala akhungu simukanakhala nalo tchimo; koma tsopano mukuti, Tikupenya, tchimo lanu litsalirabe.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu