Mutu 10
1Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu akutsika kuchokera kumwamba, atavala mtambo, ndi utawaleza pamutu pake, ndipo nkhope yake ngati dzuwa, ndi mapazi ake ngati mizati ya moto, 2ndipo m’dzanja lake ananyamula kabuku kotsekula. Ndipo anaponda mwendo wake wamanja pa nyanja, ndipo wamanzere pa mtunda, 3ndipo anafuula ndi mau akulu monga mkango wobuma. Ndipo pamene analira, mabingu asanu ndi awiri anatulutsa mau awo. 4Ndipo pamene mabingu asanu ndi awiri analankhula, ndimafuna kuti ndizilemba: ndipo ndinamva mau kuchokera kumwamba nanena, Sindikiza chizindikiro pa zinthu zimene mabingu asanu ndi awiri alankhula, ndipo usazilembe.
5Ndipo mngelo amene ndinamuona atayima pa nyanja ndi pa mtunda anakweza dzanja lake lamanja kumwamba, 6ndipo analumbira mwa iye amene akhala ku nthawi za nthawi, amene analenga kumwamba ndi zinthu zimene zili kumeneko, ndi dziko lapansi ndi zinthu zimene zili m’menemo, ndi nyanja ndi zinthu zimene zilli m’menemo, kuti pasakhalenso kuchedwa; 7koma mu nthawi ya mau a mngelo wachisanu ndi chiwiri, pamene adzafuna kuomba lipenga, chinsinsi cha Mulungu1 chidzatsirizidwanso, monga iye anadziwitsira uthenga wabwino kwa akapolo ake aneneri.
8Ndipo mau amene ndinamva kuchokera kumwamba analinso kulankhula ndi ine, ndi kunena, Pita, ukatenge kabuku kamene kali kotsegula m’dzanja la mngelo amene wayimilira panyanja ndi pa mtunda. 9Ndipo ndinapita kwa mngelo, ndinamuuza andipatse kabukuko. Ndipo iye anati kwa ine, Tenga ndipo udye: ndipo kadzapangitsa mimba yako kumva kuwawa, koma mkamwa mwako kadzakhala kozuna monga uchi. 10Ndipo ndinatenga kabukuko m’dzanja la mngelo, ndipo ndinakadya; ndipo mkamwa mwanga kanali ngati uchi, kuzuna; ndipo pamene ndinakadya mimba yanga inamva kuwawa. 11 Ndipo ananena kwa ine, Unenerenso monga kwa anthu ndi mafuko ndi manenedwe ndi mafumu ochuluka.
1Elohimu