Mutu 12

1Nthawi imeneyo Yesu anapita pa sabata pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ake anali ndi njala, ndipo anayamba kubudula ngala ndi kumadya. 2Koma Afarisi, pakuona [ichi], ananena kwa iye, Taonani, ophunzira anu akuchita choletsedwa kuchita tsiku la sabata. 3Koma iye anati kwa iwo, Kodi simunawerenge zimene Davide anachita pamene anamva njala, pamodzi ndi iwo amene anali naye? 4M’mene analowera mnyumba ya °Mulungu, ndipo anadya mikate yoonetsa, zimene zinali zosaloledwa kwa iye kudya, komanso amene anali naye, komatu ansembe okha? 5Kapena simunawerenge m’chilamulo kuti tsiku la sabata ansembe m’kachisi amaipitsa tsiku la sabata, ndipo anapezeka osachiwa? 6Koma ndinena kwa inu, kuti wakuposa kachisi ali pompano. 7Koma mukanazindikira chinthu ichi: Ine ndifuna chifundo osati nsembe ayi, simukadawaweruza iwo amene ali osalakwa. 8Pakuti Mwana wa munthu ndiye Mbuye wa sabata.

9Ndipo, pakuchoka Iye pamenepo, analowa m’sunagoge mwao. 10Ndipo taonani, panali munthu amene dzanja lake linali lopuwala. Ndipo iwo anamfunsa Iye, nanena, Kodi ndi koyenera kuchiritsa tsiku la sabata? Cholinga amafuna kumpezera chifukwa chakumtsutsa Iye. 11Koma iye ananena kwa iwo, Munthu ndani pakati panu amene akhala nayo nkhosa imodzi, ndipo ngati igwera m’dzenje tsiku la sabata, kodi sadzaitulutsa ndi kuinyamula [iyo] tsiku la sabata? 12Kodi munthu sakuposa nkhosa! Chotero kuti ndi kololedwa kuchita zabwino tsiku la sabata. 13Pamenepo Iye analankhula kwa munthu uja, tambasula dzanja lako. Ndipo anatambasula [ilo], ndipo linabwerera m’chimake ngati limzake.

14Koma Afarisi, atatuluka kunja, nafuna upangiri wotsutsana naye, m’mene angamuonongere Iye. 15Koma Yesu pakudziwa [ichi], anachoka Iye pamenepo, ndipo khamu lochuluka linamutsatira Iye; ndipo anawachiritsa iwo onse: 16ndipo anawaudzitsa iwo kuti asauze munthu aliyense za Iye: 17kuti chikakwaniritsidwe chimene chinalankhulidwa kudzera mwa Yesaya mneneri, kunena kuti, 18Taonani mtumiki wanga, amene ndamusakha, wokondedwa wanga, amene mwa Iye moyo wanga wapeza kukondwera kwake. Ine ndidzaika mzimu wanga pa Iye, ndipo adzaonetsa chiweruzo ku mafuko. 19Iye sadzalimbana kapena kulira, kapena wina aliyense kumva mau ake m’makwalala; 20bango lophwanyika sadzalithyola iye, ndi nyali yoyaka sadzaizimitsa, kufikira Iye atabweretsa chiweruzo kuti chikagonjetse; 21ndipo pa dzina lake mafuko adzayembekezera.

22Pamenepo anabweretsa kwa Iye wodzala ndi chiwanda, wakhungu ndi wosalankhula, ndipo anamuchiritsa iye, kotero kuti [munthu] wosalankhulayo analankhula ndi kupenya. 23Ndipo khamu lonse linali lodabwa ndipo linati, kodi [munthu] uyu si Mwana wa Davide? 24Koma Afarisi, pakumva [ichi], anati, [Munthu] uyu samatulutsa ziwanda, komatu mwa Beelzebule, mkulu wa ziwanda. 25Koma Iye, pakudziwa malingaliro awo, anati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanikana pawokha umapasuka, ndipo mzinda uliwonse ndi nyumba yogawanikana payokha siimakhala ayi. 26Ndipo ngati Satana amatulutsa Satana, iye wagawanika pa iye yekha; ndipo udzakhala bwanji ufumu wake? 27Ndipo ngati Ine ndimatulutsa ziwanda mwa Beelzebule, nanga ana anu, amatulutsa [izo] mwa ndani? Pachifukwa chimenechi iwo adzakhala okuweruzani. 28Koma ngati Ine mwa Mzimu wa Mulungu1 ndimatulutsa ziwanda, pamenepo ndiye kuti ufumu wa Mulungu2 wafika pa inu. 29Kapena munthu adzalowa bwanji m’nyumba ya [munthu] wamphamvu ndi kulanda katundu wake, pokhapokha ngati ayamba kumanga [munthu] wamphamvuyo? Ndipo pamenepo iye adzalanda katundu wake. 30Iye amene sali ndi Ine atsutsana ndi Ine, ndipo iye amene sasonkhanitsa ndi Ine amwaza. 31Pachifukwa chimenechi Ine ndinena ndi inu, Tchimo lililonse ndi zonena zilizonse zopweteka zidzakhululukidwa kwa anthu. 32Ndipo amene adzalankhula mau otsutsana ndi Mwana wa munthu, adzakhululukidwa kwa Iye; koma aliyense wakunenera motsutsana ndi Mzimu Woyera, sadzakhululukidwa kwa Iye, kaya ndi m’badwo uno kapena [umene] uli mkudza.

33Mungathe kupanga mtengo kukhala wabwino, ndipo zipatso zake zimakhalanso zabwino; kapena kuononga mtengo, ndipo zipatso zakenso zimakhala zoonongeka. Pakuti ndi zipatso zake mtengo umadziwika. 34Obadwa anjoka inu! Mungathe bwanji kulankhula zinthu zabwino, pomwe inu muli oipa? Pakuti m’kuchuluka kwa mtima pakamwa palankhula. 35Munthu wabwino kuchoka mu chuma chake chabwino amatulutsa zinthu zabwino; ndipo munthu woipa kuchoka mu chuma chake choipa amatulutsa zinthu zoipa. 36Ndipo ndinena kwa inu, mau onse opanda pake amene anthu adzalankhula, adzawerengedwa mlandu patsiku la chiweruzo: 37pakuti ndi mau anu mudzalungamitsidwa, ndipo ndi mau anu mudzatsutsidwa.

38Pamenepo anamuyankha Iye ena mwa alembi ndi Afarisi, nanena, Mphunzitsi, ife tikufunitsitsa tione chizindikiro kuchokera kwa inu. 39Koma Iye, pakuyankha, anati kwa iwo, M’badwo woipa ndi wachigololo umafuna chizindikiro, ndipo chizindikiro sichidzaperekedwa kwa iwo kupatula chizindikiro cha Yona mneneri. 40Pakuti ngakhale Yona anakhala m’mimba mwa nsomba masiku atatu ndi usiku utatu, momwemonso Mwana wa munthu adzakhala mu mtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku utatu. 41Anthu aku Nineve adzaimilira pa chiweruzo pamodzi ndi m’badwo umenewu, ndipo adzautsutsa: pakuti analapa pa kulalikira kwa Yona; ndipo taonani, woposa Yona [ali] pano. 42Mfumu yaikazi ya kumwera idzauka patsiku la chiweruzo pamodzi ndi mbadwo uwu, ndipo adzautsutsa; pakuti iye anachokera kumalekezero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomo. Ndipo taonani, woposa Solomo [ali] pano.

43Komatu pamene mzimu wonyansa watuluka mwa munthu, umapita kumalo owuma, kufuna mpumulo, ndipo samawupeza [uwo]. 44Kenako umanena, ndibwerera kunyumba kwanga kumene ndinatuluka; ndipo pakufika, upeza [iyo] yopanda wokhalamo, yosesedwa, ndi yokonzedwa. 45Kenako iye amapita ndi kukatenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoipa kuposa iye mwini, ndipo pakulowa, iwo amakhalira m’menemo; ndipo mathero a munthuyu amakhala oipa kuposera poyamba. Chomwecho zidzakhala ndi m’badwo uwunso.

46Koma pamene Iye anali kulankhula kwa makamu, taonani, amayi ake ndi abale ake anaimirira kunja, nafuna kulankhula kwa Iye. 47Pamenepo m’modzi anati kwa Iye, Taonani, amayi anu ndi abale anu ali kuimilira kunja, afuna kulankhula kwa Inu. 48Koma Iye pakuyankha anati kwa iye, amayi anga ndi ndani, ndipo abale anga ndi ndani? 49Ndipo, pakutansa dzanja lake kwa ophunzira ake, Iye anati, Taonani amayi anga ndi abale anga; 50pakuti aliyense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga amene ali kumwamba, ameneyo ndiye m’bale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amayi wanga.

1Elohimu2Elohimu