Mutu 5

1Ndipo kunachitika kuti pamene khamu linali kumkanikiza Iye kuti akamve mau a Mulungu1, Iye anayimilira m’mbali mwa nyanja ya Genesarete: 2ndipo Iye anaona ngalawa ziwiri zili m’mbali mwa nyanjayo, koma asodzi, atatuluka m’menemo, anali kutsuka makoka awo. 3Ndipo polowa mu imodzi mwa ngalawazo, imene inali ya Simoni, anamuuza aikankhe pang’ono kuchoka ku mtunda; ndipo Iye anakhala pansi naphunzitsa makamuwo kuchokera m’ngalawa. 4Koma pamene anasiya kulankhula, Iye anati kwa Simoni, Kankhira [kumadzi] akuya ndipo uponye makoka ako kukusodza. 5Ndipo Simoni poyankha anati kwa Iye, Ambuye, takhala usiku onse koma sitinakola kanthu, komatu chifukwa cha mau Anu ndiponya khoka. 6Ndipo atachita ichi, anazinga gulu lalikulu la nsomba. Ndipo khoka lawo linang’ambika. 7Ndipo iwo anawakodola amzawo amene analinso mu ngalawa ina kuti abwere ndi kuwathandiza, ndipo iwo anabwera, nadzadza ngalawa zonse ziwiri, kotero kuti iwo anayamba kumira. 8Koma Simoni Petro, pakuona ichi, anagwa pamapazi a Yesu, nanena, Chokani kwa ine, pakuti ndine munthu wochimwa, Ambuye. 9Pakuti kuzizwa kunamugwira iye, ndi iwonso onse amene anali naye, kukusodza kwa nsomba kumene iwo anachita; 10ndiponso chimodzimodzi ndi Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, amene anali antchito amzake a Simoni. Ndipo Yesu anati kwa Simoni, Usaope; kuyambira pano iweyo udzakhala msodzi wa anthu. 11Ndipo m’mene anakocheza ngalawazo pa gombe, anasiya zonse namtsata Iye.

12Ndipo kunachitika kuti pamene anali mu imodzi mwa mizindayo, kuti taonani, kunali munthu amene anali wodzala ndi khate, ndipo pomuona Yesu, anagwetsa nkhope yake pansi, nampempha Iye, nanena, Ambuye, ngati mufuna, mungathe kundiyeretsa ine. 13Ndipo Iye potambasula dzanja lake anamkhudza, nanena, Ndifuna; khala woyeretsedwa: ndipo nthawi yomweyo khate linachoka pa iye. 14Ndipo Iye anamuuzitsa kuti asaudze munthu wina aliyense; koma pita, kadzionetse wekha kwa ansembe, ndipo ukapereke nsembe ya chiyeretso chako monga analamulira Mose, kukhala umboni kwa iwo. 15Komatu mbiri yokhudza Iye inabuka kwambiri konseko, ndipo makamu ambiri anadza kudzamva, ndi kuchiritsidwa ku nthenda zawo. 16Ndipo Iye anachokapo ndipo anapita ku [malo] a chipululu ndi kukapemphera.

17Ndipo kunachitika kuti tsiku lina, Iye amaphunzitsa, ndipo panali Afarisi ndi akatakwe a za malamulo atakhala pamenepo, amene anabwera kuchokera ku midzi yonse yaku Galileya ndi Yudeya komanso [kunja] kwa Yerusalemu; ndipo mphamvu ya Mulungu inali [pamenepo] kuwachiritsa iwo. 18Ndipo taonani, anthu anabweretsa pa kama munthu wakufa ziwalo; ndipo iwo anafuna kumubweretsa kwa Iye, ndi kumuika [iye] pamaso pake. 19Ndipo pamene sanapeze njira yomubweretsera kwa Iye, chifukwa cha khamulo, anakwera padenga pa nyumba namtsitsira iye kudzera pa bowo padenga la nyumbayo, pamodzi ndi kama wakeyo, namfikitsa pakati pamaso pa Yesu. 20Ndipo powona chikhulupiliro chawo, Iye anati, Munthu iwe, machimo ako akhululukidwa. 21Ndipo Alembi anayamba kulingalira [m’maganizo awo], nanena, Ndani uyu amene akulankhula zomchitira Mulungu mwano? Ndani amene akhoza kukhululukira machimo komatu Mulungu2 yekha? 22Koma Yesu, podziwa malingaliro awo, poyankha anati kwa iwo, chifukwa chiyani mukulingalira m’mitima mwanu? 23chapafupi ndi chiti, kunena, Machimo ako akhululukidwa iwe; kapena kunena, Tauka nuyende? 24Komatu kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali nayo mphamvu kukhululukira machimo, Iye anati kwa wakufa ziwaloyo, Ndinena kwa iwe, Tauka, ndi kusenza kama wako ndi kupita kunyumba kwako. 25Ndipo nthawi yomweyo anaimilira pamaso pa iwo onse, nanyamula chimene iye anagonapo, napita kunyumba kwake, nalemekeza Mulungu3. 26Ndipo kudabwa kunawazinga onse, ndipo iwo analemekeza Mulungu4, ndipo anadzazidwa ndi mantha, nanena, Taona zinthu zodabwitsa lero.

27Ndipo zitatha izi Iye anapita nawona wotolera msonkho, dzina lake Levi, atakhala polandilira misonkho, nati kwa iye, nditsate Ine. 28Ndipo posiya zonse, anaimilira, namtsatira Iye. 29Ndipo Levi anamsamalira Iye kwambiri kunyumba kwake, ndipo panali khamu lalikulu la okhometsa msonkho ndi ena amene anali nawo pagome. 30Ndipo alembi awo ndi afarisi anang’ung’uza kwa ophunzira ake, nanena, Chifukwa chiyani mukudya ndi kumwa pamodzi ndi okhometsa misonkho komanso ochimwa? 31Ndipo Yesu poyankha anati kwa iwo, Amene ali bwino m’thupi safuna sing’anga, koma iwo amene akudwala. 32Ine sindinabwere kudzaitana [anthu] olungama, koma iwo amene ali ochimwa kuti alape. 33Ndipo iwo anati kwa Iye, Chifukwa chiyani ophunzira a Yohane amasala kudya pafupipafupi ndi kupembedzera, chimodzimodzinso ophunzira a Afarisi, koma ophunzira anu amadya ndi kumwa? 34Ndipo Iye anati kwa iwo, Kodi mukhoza kuletsa anyamata a ukwati kusala kudya pamene mkwati ali nawo? 35Komatu masiku adzafika pamenenso mkwati adzachotsedwa pakati pawo; pamenepo iwo adzasala masiku amenewo. 36Ndipo Iye analankhulanso fanizo kwa iwo: Palibe amene amaika chigamba chatsopano pa chovala chakale, mapeto ake adzang’ambitsa chigamba chatsopano ndipo chigamba chatsopanocho sichidzagwirizana ndi chovala chakalecho. 37Ndipo palibe amaika vinyo watsopano m’matumba a zikopa akale, mapeto ake vinyo watsopano amaphulitsa zikopazo, ndipo vinyoyo amatayika, ndi zikopazo zimaonongeka; 38komatu vinyo watsopano aikidwe mu zikopa zatsopano, ndipo zonse zimasungika. 39Ndipo palibe amene wamwa vinyo wakale [nthawi yomweyo] nafunanso kumwa vinyo watsopano, pakuti iye amati, Wakaleyu ali bwino.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu