Mutu 8

1Koma Yesu anapita ku phiri la Azitona.

2Ndipo mamawa Iye anapitanso m’kachisi, ndipo anthu onse anabwera kwa Iye; ndipo anakhala pansi nawaphunzitsa iwo. 3Ndipo alembi ndi Afarisi anabweretsa [kwa Iye] wogwidwa m’chigololo, ndipo anamuyika iye pakati, 4iwo anati kwa Iye, Mphunzitsi, mkazi uyu wagwidwa mkatikati, mwa chigololo. 5Tsopano Mose anatilamulira ife kuwagenda miyala oterewa; nanga inu pamanepa, munena kuti chiyani? 6Koma ichi analankhula kumuyesa Iye, kuti amupezere [kanthu] komutsutsa nako. Koma Yesu, atawerama, analemba pansi ndi chala chake. 7Koma pamene anapitiliza kumufunsa, anaweramuka nati kwa iwo, Amene alibe tchimo pakati panu aponye mwala woyamba kwa iye. 8Ndipo ataweramanso pansi analemba pansi. 9Koma iwo, atamva [chimenechi], anatulukamo m’modzim’modzi kuyambira akulu kufikira ochepa; ndipo Yesu anatsalapo yekha ndi mkaziyo ali kuyimilira pamenepo. 10Ndipo Yesu, pakuweramuka ndi kuona kuti panalibepo anthu kupatula mkazi uja, anati kwa iye, Mkaziwe, ali kuti aja amakutsutsawa? Kodi palibe amene wakutsutsa iwe? 11Ndipo iye anati, Palibe, Ambuye. Ndipo Yesu anati kwa iye, Inenso sindikutsutsa: pita, ndipo usakachimwenso. 12Pameneponso Yesu analankhula kwa iwo, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wakutsatira Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuunika kwa moyo. 13Pamenepo Afarisi anati kwa Iye, Mukuchitira umboni okhudza inu nokha; umboni wanu suli owona. 14Yesu anayankha nati kwa iwo, Ngakhale ndichitire umboni okhudza Ine mwini, umboni wanga ndi owona, chifukwa Ine ndidziwa kumene ndikuchokera komanso kumene ndikupita. 15Inu mumaweruza molingana ndi thupi, Ine sindiweruza munthu aliyense. 16Ndipo ngatinso Ine ndikaweruza, chiweruzo changa ndi choona, chifukwa sindili ndekha, koma Ine ndili ndi Atate amene anandituma. 17Ndipo m’chilamulonso chanu munalembedwa kuti umboni wa anthu awiri ndi owona: 18Ine ndi amene ndichitira umboni okhudza Ine mwini, ndipo Atate amene anandituma Ine achitira umboni okhudza Ine. 19Pamenepo iwo anati kwa Iye, Kodi Atate wanu ali kuti? Yesu anayankha, Inu simudziwa Ine kapena Atate wanga. Mukadadziwa Ine, mukadadziwanso Atate wanga. 20Mau amenewa analankhula mosungira chuma, akuphunzitsa m’kachisi; ndipo palibe amene anamgwira, pakuti ola lake linali lisanafike.

21Pameneponso Iye anati kwa iwo, Ndipita, ndipo mudzandifunafuna, ndipo mudzafa m’machimo anu; kumene ndikupita simungafikeko. 22Pamenepo Ayuda anati, Kodi azadzipha yekha, kuti akunena, Kumene ndipita simungafikeko? 23Ndipo Iye anati kwa iwo, ndinu a pansi pano; Ine ndine wakumwamba. Inu ndinu a dziko ili lapansi; Ine siwadziko lapansili. 24Kotero Ine ndinena kwa inu, kuti mudzafa m’machimo anu; pakuti ngati simukhulupilira kuti ndine [Iye], mudzafa m’machimo anu. 25Kotero iwo anati kwa Iye, Inu ndinu ndani? [Ndipo] Yesu anati kwa iwo, Chimene ndinalankhulanso kwa inu. 26Ndili nazo zinthu zambiri zonena ndi kuweruza zokhudza inu, koma Iye amene wandituma Ine ali woona, ndipo Ine, zimene ndamva kuchokera kwa Iye, zinthu zimenezo ndilankhula ku dziko lapansi. 27Iwo sanadziwe kuti Iye amakamba kwa iwo za Atate. 28Chomwecho Yesu anati kwa iwo, Pamene mudzamkweza Mwana wa munthu, pamenepo muzadziwa kuti ndine [Iye], ndipo [kuti] sindipanga kanthu pa Ine ndekha, koma monga Atate anandiphunzitsira ndilankhula zinthu zimenezi. 29Ndipo Iye amene anandituma ali nane; sanandisiye Ine ndekha, chifukwa ndimachita nthawi zonse zinthu zosangalatsa Iye. 30Pamene Iye analankhula zinthu zimenezi ambiri anakhulupilira pa Iye.

31Pamenepo Yesu anati kwa Ayuda amene anakhulupilira Iye, Ngati mukhalabe m’mau anga, ndinu ophunzira anga enieni; 32ndipo muzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani. 33Iwo anamuyankha Iye, Ife ndi mbeu ya Abrahamu, ndipo sitinakhalepo pansi pa ukapolo wa aliyense; nanga bwanji Inu munena, Mudzakhala mfulu? 34Yesu anawayankha iwo, Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, Aliyense wakuchita tchimo ali kapolo wa tchimo. 35Tsopano kapolo sakhala mnyumba nthawi zonse: mwana ndiye amakhala nthawi zonse. 36Pamenepo ngati Mwana adzakumasulani, mudzamasulidwadi. 37Ine ndikudziwa kuti ndinu mbeu ya Abrahamu; koma mufuna kundipha Ine, chifukwa mau anga sanalowe mwa inu. 38Ine ndilankhula zimene ndaona ndi Atate, ndipo inu pamenepo zimene mwaona ndi atate wanu. 39Iwo anayankha nati kwa Iye, Abrahamu ndi atate wathu. Yesu anati kwa iwo, Mukanakhala ana a Abrahamu, mukanachita ntchito za Abrahamu; 40koma pano mufuna kundipha, munthu amene walankhula chilungamo kwa inu, chimene ndachimva kuchokera kwa Mulungu1: chimenechi Abrahamu sanachite. 41Inu muchita ntchito ya atate wanu. [Kotero] iwo anati kwa Iye, Ife sitinabadwe mwa chigololo; ife tili naye atate m’modzi, Mulungu2. 42Yesu anati kwa iwo, Ngati Mulungu3 akanakhala atate wanu mukanandikonda Ine, pakuti Ine ndinachokera kwa Mulungu4 ndipo ndinachokera [kwa Iye]; pakuti sindinabwere mwa ndekha, koma Iye wandituma Ine. 43Chifukwa chiyani simukutha kudziwa malankhulidwe anga? Chifukwa simungathe kumva mau anga. 44Inu ndinu a mdierekezi, monga atate [wanu], ndipo mukhumba kuchita zonyansa za atate wanu. Iye anali wakupha kuyambira pachiyambi, ndipo sanayimeko pa choonadi, chifukwa mulibe choonadi mwa iye. Pamene alankhula bodza, amalankhula zimene zili zake zomwe; pakuti iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza: 45ndipo chifukwa ndilankhula choonadi, simundikhulupilira Ine. 46Ndani mwa inu anganditsutse Ine za tchimo? Ngati ndilankhula chilungamo, chifukwa chiyani simukundikhulupilira? 47Iye amene ali wa Mulungu5 amamva mau a Mulungu6: chomwecho inu simuwamva, chifukwa simuli a Mulungu7. 48Ayuda anayankha nati kwa Iye, Sitinanene ife bwino lomwe kuti ndinu Msamaliya ndipo muli ndi chiwanda? 49Yesu anayankha, Ine ndilibe chiwanda; koma Ine ndimalemekeza Atate wanga, ndipo inu simundilemekeza Ine. 50Koma Ine sindifuna ulemelero wa Ine ndekha: alipo Iye wakuutsata ndi wakuweruza. 51Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, Ngati wina adzasunga mau anga, sadzaona konse imfa. 52Pamenepo Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tadziwa kuti muli ndi chiwanda. Abrahamu anamwalira, ndiponso aneneri, ndiye inu mukuti, Ngati wina adzasunga mau anga, sadzalawa imfa. 53Kodi ndinu wamkulu kuposa atate wathu Abrahamu, amene anamwalira? Ndi aneneri anamwalira: mukudziyesa kuti ndinu ndani? 54Yesu anayankha, Ngati ndizilemekeza ndekha, ulemelero wanga uli chabe: ndi Atate wanga amene amandilemekeza Ine, amene inu munena, Iye ndi Mulungu8 wathu. 55Ndipo inu simumdziwa Iye; koma Ine ndimdziwa Iye; ndipo ngati Ine ndinena, Sindimdziwa, ndifanana ndi inu, wabodza. Koma ndimdziwa Iye, ndipo ndimasunga mau ake. 56Atate wanu Abrahamu anakondwera kuti akaone tsiku langa, ndipo anaona nasangalala. 57Pamenepo Ayuda anati kwa Iye, Simunakwanitse ndi zaka makumi asanu zomwe, ndiye munaona Abrahamu kodi? 58Yesu anati kwa iwo, Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, Abrahamu asanakhaleko, Ine ndinaliko. 598Iwo anatenga miyala yawo kuti amugende [nayo] Iye; koma Yesu anazibisa yekha natuluka m’kachisi, [nadutsa pakati pawo, napitilira.]

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu