Mutu 15

1Ndipo onse okhometsa msonkho ndi ochimwa anali kubwera pafupi naye kuti adzamvere Iye; 2ndipo Afarisi ndi alembi anang’ung’uza nati, [Munthu] uyu akulandira anthu ochimwa ndi kudya nawo. 3Ndipo Iye analankhula nawo fanizo ili, nati, 4Ndani wa inu pakukhala nazo nkhosa zana limodzi, ndipo pakutayika imodzi mwa izo, samasiya zinazo makumi asanu ndi anayi kudza mphambu zisanu ndi zinayi m’chipululu napita ndi kuyang’ana yotayikayo, kufikira atayipeza? 5ndipo atayipeza, ayinyamula pa mapewa pake, nasangalala; 6ndipo pakufika kunyumba, ayitana pamodzi abwenzi ake ndi anansi, nanena kwa iwo, Sangalalani ndi ine, pakuti ndayipeza nkhosa yanga yosocherayo. 7Ine ndinena kwa inu, kuti kudzakhala chimwemwe kumwamba kwa wochimwa m’modzi wolapa, [kuposera] makumi asanu ndi anayi kudza mphambu asanu ndi anayi olungama amene sasoweka kutembenuka mtima.

8Kapena, mkazi wanji amene ali nazo ndalama za siliva khumi, ngati ataya imodzi, samayatsa nyali yake ndi kusesa mnyumba nayifunafuna mosamala kufikira atayipeza? 9ndipo atayipeza ayitana pamodzi abwezi ndi anansi, nanena, Sangalalani ndi ine, pakuti ndayipeza ndalama imene inanditayikayo. 10Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chisangalalo pamaso pa angelo a Mulungu1 chifukwa cha wochimwa m’modzi.

11Ndipo Iye anati, Munthu wina anali ndi ana amuna awiri; 12ndipo wamng’onoyo anati kwa atate wake, Atate, ndipatseni gawo la chuma limene likugwa [kwa ine]. Ndipo Iye anawagawira zimene iye anali nazo. 13Ndipo pakupita masiku ochepa wamng’onoyo anasonkhetsa pamodzi zonse napita kudziko lakutali, ndipo kumeneko anasakaza chuma chake, nakhala moyo wachitayiko. 14Koma pamene anawononga zonse kumeneko kunabuka njala yaikulu m’dziko lonselo, ndipo anayamba kusowa. 15Ndipo iye anapita nadziphatika kwa imodzi mwa mzika ya dziko limenelo, ndipo anamutumiza iye kubusa kukaweta nkhumba. 16Ndipo iye anafunitsitsa kukhutitsa mimba yake ndi madeya amene nkhumba zimadya; ndipo palibe amene anampatsa iye kanthu. 17Ndipo pokumbukira mwa iye yekha, anati, Ndi angati antchito olembedwa a atate wanga amene ali nawo mkate wochuluka, ndipo ine ndikuvutika kuno ndi njala. 18Ine ndidzanyamuka ndi kupita kwa atate wanga, ndipo ndikati kwa iwo, Atate, ndachimwira kumwamba ndi pamaso panu; 19Ineyo sindiyeneranso kutchedwa mwana wanu: munditenge ngati m’modzi wa antchito anu olembedwa. 20Ndipo iye ananyamuka napita kwa atate wake. Koma ali patali, atate wake anamuona iye, ndipo anagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira mkhosi mwake, ndipo anampsopsonetsa. 21Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate, nadachimwira kumwamba ndi pamaso panu; Ine sindilinso woyenera kutchedwa mwana wanu. 22Koma atatewo anati kwa akapolo ake, Tulutsani mwinjiro wabwino ndi kumveka iye, ndipo muyike mphete pa dzanja lake ndi nsapato kumapazi kwake; 23ndipo mubweretse ng’ombe yonenepa ndi kuyipha, ndipo tiyeni tidye ndi kusangalala: 24pakuti mwana wanga uyu anali wakufa ndipo wakhalanso ndi moyo, anali wotayika ndipo wapezeka. Ndipo iwo anayamba kusangalala. 25Ndipo mwana wake wamkulu anali kumunda; ndipo pamene amabwera, anawandikira kunyumba kuja, iye anamva kuyimba ndi kuvina. 26Ndipo pamene anayitana m’modzi wa anyamata, anafunsa kuti chimene chimachitika ndi chiyani. 27Ndipo anati kwa iye, M’bale wako wabwera, ndipo atate wako amuphera ng’ombe yonenepa chifukwa amulandira iye wabwino ndi wamoyo. 28Koma iye anapsa mtima ndipo sanalowe mkati. Ndipo atate wake anatuluka panja namdandaulira iye. 29Koma iye poyankha anati kwa atate wake, Taonani, kwa zaka zambiri ndakutumikirani inu, ndipo sindinapandukirepo lamulo lanu; ndipo ine simunandipatseko mwana wa ng’ombe kuti ndisangalale ndi abwezi anga: 30koma pamene mwana wanu uyu, amene wawononga chuma chanu ndi mahule, wabwera, mwamuphera iye ng’ombe yonenepa. 31Koma atatewo anati kwa iye, Mwana wanga, iwe wakhala uli ndi ine nthawi zonse, ndipo zonse zimene zili zanga ndi zako. 32Komatu kunali koyenera kusangalala ndi kukondwera, chifukwa m’bale wako uyu anali wakufa koma wakhalanso ndi moyo, anatayika ndipo wapezeka.

1Elohimu