Mutu 8

1Koma chidziwike ichi kwa inu, abale, chisomo cha 1Mulungu chapatsidwa m’mipingo yaku Makedoniya; 2kuti yesero lalikulu la zowawa kuchuluka kwa chimwemwe chawo ndi umphawi wao waukulu zachulukira ku kulemera kwa ufulu wa mtima wao. 3Pakuti molingana ndi mphamvu yawo, ndichitira umbonI, ndipo taonani mphamvu yawo, anafunitsitsa kuchita iwo mwa kuthekera kwao, 4kutipempha ife ndi kutidandaulira kwambiri kusamalira chisomo ndi chiyanjano cha utumiki chimene chinaperekedwa kwa oyera mtima. 5Ndipo osati monga mwa chiyembekezo chathu, koma anadzipereka koyamba kwa Ambuye, ndi kwa ife mwa chifuniro cha 2Ambuye. 6Kotero kuti tinampempha Tito kuti, molingana anayamba kale, kuti akamalizenso kwa inu monga mwa chisomonso ichi; 7koma ngakhale munachulukira mbali zonse, m’chikhulupiliro, ndi m’mau, ndi m’chidziwitso, ndi m’khama lonse, ndi m’chikondi chanu kwa ife, kuti mukachulukirenso m’chisomo ichi. 8Sindikulankhula monga kulamulira, koma kudzera mu khama la anthu ena, ndi kusonyeza choonadi cha chikondi chanu. 9Pakuti inu mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti chifukwa cha inu Iye, pokhala wolemera, anakhala wosauka, cholinga kuti inu mwa kusauka kwake mukalemere. 810Ndipo ine ndipereka malingaliro anga mu chimenechi, pakuti ichi ndi chopindulitsa kwa inu amene munayamba kale, osati kuchita chabe, komanso kufunitsitsa, kuyambira chaka chapitachi. 11Koma tsopano malizitsaninso kuchita ichi; kuti monga kunali kukonzekera kufunitsitsa, koteronso mukamalidzitse chimene muli nacho. 12Pakuti ngati kuyembekezera kuli pamenepo, munthu avomerezedwa molingana ndi chimene ali nacho, osati pa chimene alibe. 13Pakuti sikoyenera kuti ena akhale omasuka pa ena, ndipo inu musautsidwe, 14koma [pa mfundo] yokhala ofanana; mu nyengo yatsopano ya zochuluka zanu pa kusowa kwao, kuti zochuluka zao zikakwanire zosowa zanu, cholinga kuti pakakhale kufanana pakati panu. 15Molingana ndi zolembedwa, Iye amene asonkhanitsa zambiri sizinamtsalire, ndipo iye wosonkhanitsa pang’ono sichinamsowa.

16Koma alemekezeke 3Mulungu, amene amapereka khama lomwelo pa inu mumtima wa Tito. 17Pakuti analandiradi kudandaulira kwathu, koma, chifukwa chodzala ndi khama, anatuluka mwa iye yekha kupita kwa inu; 18koma tatumiza pamodzi ndi iye m’bale amene kuyamika kwake mu uthenga wabwino kuli m’mipingo yonse; 19ndipo osati ichi chokha, koma wasankhidwanso ndi mipingo monga woyenda naye pamodzi mu chisomo chimenechi, chotumikiridwa ndi ife ku ulemelero wa Ambuye mwini, ndi [mboni] ya chivomerezo chathu; 20popewa ichi, kuti aliyense akatidzudzula ife m’zochuluka zimenezi zotumikiridwa ndi ife; 21pakuti ife tipereka zinthu moona mtima, osati pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu. 22Ndipo tawatumizira iwo m’bale wathu amene ife tatsimikiza kuti ndi wamachawi mu zinthu zambiri, ndipo tsopano machawi akulu ndi kudzikhulupilira kwakukulu ali nako pa inu. 23Kaya zokhudzana ndi Tito, iyeyu ndi mzanga komanso wotumikira naye m’malo mwanu; kapena abale athu, ali atumiki a mipingo, ku ulemelero wa Khristu. 24Pamenepo awonetseni iwo, pamaso pa mipingo, umboni wa chikondi chanu, ndiponso kukutamandirani kwathu za inu.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu