Mutu 1
1Paulo, mtumwi wa Yesu Khristu, molingana ndi lamulo la Mulungu1 Mpulumutsi wathu, ndi la Khristu Yesu chiyembekezo chathu, 2kwa Timoteyo, mwana wanga weniweni m’chikhulupiliro: chisomo, chifundo, mtendere, zochokera kwa Mulungu2 Atate wathu ndi Khristu Yesu Ambuye wathu. 3Monga ndinakupemphani inu kukhalabe m’Efeso, pamene ndimapita ku Makedoniya, kuti ukawalamulire ena kuti asaphunzitse ziphunzitso zina, 4kapena kutembenuzira malingaliro awo ku ziphunzitso zabodza ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, zimene zimabweretsa mafunso kusiyana ndi chikonzero cha Mulungu3, chimene chili m’chikhulupiliro. 5Koma chitsiriziro cha zimene zinalamulidwa ndicho chikondi chochokera mu mtima wangwiro ndi chikumbumtima chabwino ndi chikhulupiliro chenicheni; 6zinthu zimene ena anaziphonya, natembenukira zinthu zopanda pake, 7pofunitsitsa kukhala aphunzitsi a chilamulo, osamvetsetsa chimene iwo anena kapena zokhuza zimene azilimbikira. 8Tsopano ife tidziwa kuti lamulo ndi labwino ngati munthu aligwiritsa ntchito monga mwa lamulo, 9podziwa ichi, kuti lamulo siligwira ntchito kwa munthu wolungama, koma kwa wosaweruzika ndi wosamvera, amwano kwa Mulungu4 ndi ochimwa, osayera mtima ndi achipongwe, akumenya atate, ndi akumenya amayi; kufikira akupha, 10achigololo, ogonana amuna kapena akazi okhaokha, ogwira anthu mokakamiza, abodza, olumbira zonama; ndi kalikonse kotsutsana ndi chiphunzitso choonadi, 11molingana ndi uthenga wabwino wa ulemelero wa Mulungu5 wodalitsika,umene unaikizidwa mwa ine. 12Ndipo ndiyamika Khristu Yesu Ambuye wathu, amene anandipatsa ine mphamvu, kuti anandiwerengera ine kukhala wokhulupirika, wosankhidwa kumtumikira iye 13amene poyamba ndinali wamwano ndi wozunza, ndi munthu woyerekedwa: koma chifundo chinaonetsedwa kwa ine chifukwa ndinachita izi mosazindikira, mosakhulupilira. 14koma chisomo cha Ambuye wathu chidachulukira mopyola muyeso ndi chikhulupiliro ndi chikondi, chimene chili mwa Khristu Yesu. 15Okhulupirika ali mauwa, ndi oyenera mkulandiridwa konse, kuti Khristu Yesu anabwera m’dziko lapansi kudzapulumutsa ochimwa, amene ine ndili woyambilira. 16Koma pachifukwa chimenechi chifundo chinaonetsedwa kwa ine, kuti mwa ine, koyamba, Yesu Khristu akaonetsere kupilira konse, kukhala chitsanzo kwa iwo odzakhulupilira pa iye ku moyo wosatha. 17Tsopano kwa mfumu ya nthawi zonse, yosavunda, yosaoneka ndi maso, Mulungu6 yekhayo, ulemu ndi ulemelero ku nthawi za nthawi. Amen. 18Lamulo ili, mwana wanga Timoteyo, ndilipereka kwa iwe, molingana ndi mauneneri ananenedwa kwa iwe, cholinga kuti ulimbane nawo nkhondo yabwino, 19kusungabe chikhulupiliro ndi chikumbumtima chabwino; chimene ena otsala, anachikankha, nachiononga ngati ngalawa monga mwa chikhulupiliro; 20 amene mwa iwo Humenayo ndi Alesandro, amene ndinawapereka kwa Satana, kuti iwo akaphunzitsidwe mwambo kuti asalankhule mwano.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu