Mutu 17

1Ndipo patapita masiku asanu ndi limodzi Yesu anadzitengera [Iye] Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane m’bale wake, ndipo anapita nawo pambali pa phiri lalitali. 2Ndipo iye anasandulika pamaso pawo. Ndipo nkhope yake inawala ngati dzuwa, ndipo zovala zake zinakhala zoyera mbuu ngati kuwala; 3ndipo taonani, Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo akuyankhula naye. 4Ndipo Petro pakuyankha anati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tikhale pano. Ngati mufuna, tiyeni timange misasa itatu: umodzi wa inu, ndi wina wa Mose ndi wina wa Eliya. 5Pamene iye anali chiyankhulire, taonani, mtambo wowala unawazinga iwo, ndipo tonani, mau ochokera mu mtambo, anati, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera: mverani Iye. 6Ndipo ophunzira pakumva mauwa anagwa nkhope zawo pansi, ndipo anagwidwa mantha akulu. 7Ndipo Yesu pakubwera kwa [iwo] anawakhudza, ndipo anati, Dzukani, ndipo musachite mantha. 8Ndipo pakukweza maso awo, iwo sanaonenso munthu wina koma Yesu yekha.

9Ndipo pamene anali kutsika pa phiri, Yesu anawalangiza iwo, nanena, Musauze wina aliyense masomphenyawa, kufikira Mwana wa munthu akadzauka pakati [pa] akufa. 10Ndipo ophunzira [ake] anamfunsa Iye nanena, Chifukwa chiyani alembi amanena kuti Eliya ndiye atsogole kubwera? 11Ndipo Iye pakuyankha anati kwa iwo, Eliya adzatsogoladi kubwera ndipo adzabwenzeretsa zinthu zonse. 12Koma ndinena kwa inu kuti Eliya wabwera kale, ndipo iwo sanamzindikire iye, komatu anachita kwa iye chilikonse chimene iwo anafuna. Chomwechonso Mwana wa munthu watsala pang’ono kuzunzidwa ndi iwo. 13Kenako ophunzira anamvetsetsa kuti Iye amalankhula kwa iwo zokhudza Yohane m’batizi.

14Ndipo pamene iwo anabwera ku khamu la anthu, munthu wina anabwera kwa Iye, atagwada pa maondo ake, ndipo anati, 15Ambuye, chitirani chifundo mwana wanga, pakuti iye ali wa khunyu, ndipo akuzunzika kwambiri; pakuti kawirikawiri amagwera pamoto komanso kawirikawiri m’madzi. 16Ndipo ndinamubweretsa iye kwa ophunzira anu, ndipo sanakwanitse kumuchiritsa iye. 17Ndipo Yesu pakuyankha anati, Ha! m’badwo wosakhulipilira ndi wamphulupulu, ndidzakhala ndi inu kufikira liti? Ndidzapilira nanu kufikira liti? M’bweretseni iye kwa Ine. 18Ndipo Yesu anamdzudzula iye, ndipo chiwanda chinatuluka mwa iye, ndipo mnyamatayo anachiritsidwa kuyambira nthawi yomweyo.

19Pamenepo ophunzira, pakubwera kwa Yesu pambali, anati [kwa Iye], Chifukwa chiyani ife sitinakwanitse kumtulutsa iye? 20Ndipo anati kwa iwo, Chifukwa cha kusakhulupirira kwanu; pakuti zoonadi ndinena kwa inu, Mukanakhala ndi chikhulupiriro ngati [mbeu] ya mpiru, mukananena kwa phiri ili, Samuka pano nupite uko, ndipo likanasamuka lokha; ndipo palibe chimene chikanakukanikani inu. 21Komatu cha mtundu uwu sichimatuluka wamba komatu mwa pemphero ndi kusala kudya.

22Ndipo pamene amapita ku Galileya, Yesu anati kwa iwo, Mwana wa munthu watsala pang’ono kuperekedwa m’manja mwa anthu, 23ndipo iwo adzamupha Iye; ndipo tsiku lachitatu adzauka. Ndipo iwo anali ndi chisoni chachikulu.

24Ndipo pamene iwo anafika ku Karpenao, iwo amene amalandira ndalama za ku kachisi anabwera kwa Petro ndipo anati, Kodi mphunzitsi wanu samapereka ndalama ya ku kachisi? 25Iye anati, Inde. Ndipo pamene analowa m’nyumba, anayamba kuyankhula naye, Kodi ukuganiza bwanji, Simoni? Mafumu a dziko lapansi, amalandira kwa ndani msonkho ndi choyamika? Amalandira kuchokera kwa ana awo kapena alendo? 26Petro anati kwa Iye, Amalandira kwa alendo. Yesu anati kwa Iye, Kotero anawo ndi mfulu. 27Komano kuti tisakhale chipsinjo kwa iwo, pita ku nyanja ndipo ukaponye mbedza, ndipo ukatenge nsomba yoyamba kukodwa, ndipo ukakanule kukamwa kwake ndipo upezamo kobiri; ulitenge ndipo uwapatse iwo kuti chimenecho ndi chopereka changa komanso chanu.