Mutu 7
1Ndipo pamene Iye anatsiriza mau ake onse akumvedwa ndi anthu, analowa mu Karpenao. 2Ndipo kapolo wina wa kenturiyo amene anali wokondedwa kwa iye anadwala pafupi kufa; 3ndipo atamva za Yesu, anatumiza kwa Iye akulu a Ayuda, namuchonderera kuti adze ndi kupulumutsa kapolo wake. 4Koma iwo, pakudza kwa Yesu, anampempha Iye mokakamiza, nanena, Iye ali woyenera kuti mumchitire ichi, 5pakuti iyeyu amakonda fuko lathuli, ndipo iye yekha anatimangira ife sunagoge. 6Ndipo Yesu anapita nawo. Koma atafika kale, pamene anali kuwandikira nyumbayo, kenturiyo anamtumira Iye amzake, nanena kwa Iye, Ambuye, musazivutitse nokha, pakuti sindili woyenera kuti mukhoza kulowa pansi pa tsindwi langa. 7Pameneponso ine sindidziwerengera ndekha woyenera kubwera kwa inu. Komatu mungolankhula mau ndipo kapolo wanga adzachiritsidwa. 8Pakuti Inenso ndi munthu amene ndili ndi ulamuliro, amene ndili ndi asilikali pansi panga, ndipo ndimalankhula ndi [uyu], Pita, ndipo amapitadi; ndi kwa wina, Bwera, ndipo amabweradi; ndi kwa kapolo wanga, Chita ichi, ndipo iye amachitadi [ichi]. 9Ndipo Yesu pakumva ichi anadabwa naye, ndipo potembenukira ku khamu lomutsatiralo anati, Ine ndinena kwa inu, Ngakhale mu Israyeli sindinapeze chikhulupiriro chachikulu chotere. 10Ndipo iwo amene anatumidwa pobwerera kunyumba anakapeza kapolo, amene amadwala, atachira.
11Ndipo kunachitika kuti zitatha izi anapita ku mzinda wotchedwa Nayini, ndipo ambiri mwa ophunzira ake pamodzi ndi khamu lalikulu anapita naye pamodzi. 12Ndipo akuwandikira pa chipata cha mzindawo, taonani, munthu wakufa ananyamulidwa, mwana wa mwamuna m’modzi yekhayo kwa mayi wake, ndipo iyeyu anali mkazi wa masiye, ndipo anthu ambiri mu mzindamo anali naye. 13Ndipo Ambuye, pakumuona, anagwidwa naye chifundo, nati kwa iye, Usalire; 14ndipo pakudza Iye anakhudza chithatha, ndipo akum’nyamulawo anayima. Ndipo Iye anati, Mnyamatawe, ndinena kwa iwe, Tauka. 15Ndipo wakufayo anakhala tsonga nayamba kulankhula; ndipo anampereka iye kwa mayi wake. 16Ndipo mantha anagwira onse, ndipo iwo analemekeza Mulungu1, nanena, Mneneri wamkulu wauka pakati pathu; ndipo Mulungu2 wayendera anthu ake. 17Ndipo mbiri yokhudza Iye inabuka mu Yudeya yense, ndi maiko onse ozungulira.
18Ndipo ophunzira a Yohane anabweretsa mau kwa iye okhudza zinthu zonsezi: 19ndipo Yohane, atayitana awiri a ophunzira ake, anawatuma kwa Yesu, nanena, Kodi ndinu amene ali nkudza, kapena tidikire wina? 20Koma anthuwo pofika kwa Iye anati, Yohane m’batizi watituma ife kwa inu, kunena kuti, Kodi ndinu amene ali nkudza, kapena tidikire wina? 21Mu ola limenelo Iye anachiritsa ambiri ku nthenda zawo ndi milili ndi mizimu yoipa, ndipo kwa ambiri osapenya anawapenyetsa. 22Ndipo Yesu poyankha anati kwa iwo, Pitani, kabwenzeni mau kwa Yohane pa zimene mwaona ndi kumva: kuti akhungu akupenya, opuwala akuyenda, akhate akuchiritsidwa, osamva akumva, akufa akuukitsidwa, osauka akulalikidwa uthenga; 23ndipo wodala amene sakhumudwa mwa Ine.
24Ndipo amithenga a Yohane atachoka, Iye anayamba kulankhula kwa makamu zokhudza Yohane: Kodi munapita mu chipululu kukaona chiyani? Bango likugwedezeka ndi mphepo? 25Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zofewa kodi? Taonani, iwo ovala zovala zapamwamba ndi kukhala moyo wofewa ali m’makuka a mafumu. 26Koma inu munatuluka kukaona chiyani? Mneneri kodi? Indetu, Ine ndinena kwa inu, chimene chili cholemekezeka kwambiri kuposa mneneri. 27Izi ndi zimene zinalembedwa zokhudza iye, Taonani, Ine ndidzatuma wamthenga patsogolo pako, amene adzakonza njira yako pamaso pako; 28pakuti ndinena kwa inu, pakati pa iwo obadwa mwa mkazi palibe [mneneri] wamkulu woposa Yohane [m’batizi]; komatu amene ali wamng’ono mu ufumu wa Mulungu3 ali wamkulu kuposa iye. 29(Ndipo anthu onse amene anamva [ichi], pamodzi ndi okhometsa msonkho omwe, anavomereza Mulungu4, pobatizidwa ndi ubatizo wa Yohane; 30komatu Afarisi ndi achilamulo anakanitsitsa kwa iwo okha uphungu wa Mulungu5, posabatizidwa ndi iye.) 31Kodi ndidzafanizira chiyani anthu a m’badwo uno, ndipo iwo ali ngati ndani? 32Iwo ali ngati ana akukhala mu msika, naitanana wina ndi mzake ndi kuti, Ife takuyimbirani chitoliro, koma inu simunavine; ife tinabuma maliro kwa inu, koma inu simunalire. 33Pakuti Yohane m’batizi wabwera wosadya mkate kapena kumwa vinyo, ndipo inu munena, Ali ndi chiwanda. 34Mwana wa munthu wabwera wakudya ndi kumwa, ndipo inu munena, Taonani munthu wosusuka ndi womwaimwa vinyo, bwenzi la okhometsa msonkho ndi ochimwa; 35ndipo nzeru inalungamitsidwa mwa ana ake onse.
36Koma m’modzi wa Afarisi anamupempha Iye kuti akadye naye pamodzi. Ndipo polowa m’nyumba ya Mfarisiyo anakhala pansi kuseyama pa gome; 37ndipo taonani, mkazi wa mumzindamo, amene anali wochimwa, podziwa kuti Iye anakhala pansi kuseyama nyama m’nyumba ya Mfarisi, anatenga nsupa ya alabastero ya mafuta a mule, 38ndipo poyimilira pamapazi ake kumbuyo kwake akulira, anayamba kusambitsa mapazi ake ndi misozi; ndipo anapukuta mapaziwo ndi tsitsi la m’mutu mwake, napsopsona mapazi akewo, nawadzodza ndi mule. 39Ndipo Mfarisi amene anamuyitana Iye, powona ichi, analankhula mwa iye yekha nati, [Munthu] uyu akanakhala mneneri akadadziwa za mkazi amene akumukhudzayu, pakuti ndi wochimwa ndithu. 40Ndipo Yesu poyankha anati kwa iye, Simoni, ndili ndi kanthu kakuti ndikuuze iwe. Ndipo iye anati, Mphunzitsi, tanenani. 41Panali anthu awiri amene anangongola ndalama kwa wongongoletsa ndalama: wina anangongola marupiya mazana asanu ndi wina makumi asanu; 42koma pamene anasowa kanthu kobweza, iye anawakhululukira onse awiri [ngongole zawo]: [tandiuze,] ndani mwa awiriwa adzamkonda iye koposa? 43Ndipo Simoni poyankha anati, Ndiganiza uyo amene amkhululukira zambiriyo. Ndipo Iye anati, waweruza bwino. 44Ndipo potembenukira kwa mkaziyo Iye anati kwa Simoni, Wamuona mkazi uyu? Ine ndalowa mnyumba mwako muno; sunandipatse madzi kusambitsa mapazi anga, koma iye wasambitsa mapazi anga ndi misozi, ndi kupukuta ndi tsitsi lake. 45Iwe sunandipsopsoneko, koma iye nthawi imene ndalowa muno sanasiye kupsopsona mapazi anga. 46Mutu wanga sunandidzodze ndi mafuta, koma iye wadzodza mapazi anga ndi mule. 47Pachifukwa ichi ndinena kwa iwe, Machimo ake ambiri akhululukidwa; pakutinso wakonda kwambiri; koma kwa iye amene wakhululukidwa zochepa amakondanso pang’ono. 48Ndipo anati kwa iye, Machimo ako akhululukidwa. 49Ndipo iwo amene anali [nawo] pa gome anayamba kulankhula mwa iwo okha, Ndani uyu kuti akhoza kukhululukira machimo? 50Ndipo anati kwa mkaziyo, Chikhulupiliro chako chakupulumutsa iwe; pita mu mtendere.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu