Mutu 3
1Koma panali munthu pakati pa Afarisi, dzina lake Nikodemo, mkulu wa Ayuda; 2anabwera kwa Iye usiku, nati, Rabi, tidziwa kuti munabwera monga mphunzitsi kuchokera kwa Mulungu1, pakuti palibe amene akhoza kuchita zizindikiro zimene mumachita pokhapokha ngati Mulungu2 ali naye. 3Yesu anayankha nati kwa iye, Zoonadi, zoonadi, Ine ndinena kwa iwe, Pokhapokha ngati munthu sabadwa mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu3. 4Nikodemo anati kwa Iye, Kodi munthu akhoza kubadwa bwanji atakula? Kodi akhoza kulowanso m’mimba mwa mayi wake ndi kubadwanso? 5Yesu anayankha, Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa iwe, Pokhapokha ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sangathe kulowa mu ufumu wa Mulungu4. 6Chimene chimabadwa mwa thupi chikhala thupi; ndipo chimene chimabadwa mwa Mzimu chikhala mzimu. 7Usadabwe pakuti ndanena kwa iwe, ndi kofunikira kuti iwe ubadwe mwatsopano. 8Mphepo imaomba kumene ifuna, ndipo mumaimva mau ake, koma simudziwa kumene ikuchokera ndi kumene ikupita: choteronso aliyense wobadwa mwa Mzimu. 9Nikodemo anayankha nati kwa Iye, Kodi zinthu zimenezi zingatheke bwanji? 10Yesu anayankha nati kwa iye, Ndiwe mphunzitsi wa Israyeli ndipo sudziwa zinthu zimenezi! 11Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa iwe, Ife timalankhula chimene tichidziwa, ndipo timachitira umboni za chimene taona, koma simulandira umboni wathu. 12Ngati ndanena zinthu za pansi pano kwa iwe, ndipo sukukhulupilira, nanga bwanji, ngati ndikanena kwa iwe zinthu zakumwamba, udzakhulupilira kodi? 13Ndipo palibe amene anapitako kumwamba, kupatula Iye yekhayo anatsika kuchokera kumwamba, Mwana wa munthu amene ali kumwamba. 14Ndipo monga Mose anakweza njoka m’chipululu, momwemonso Mwana wa munthu adzakwezedwa, 15kuti aliyense wokhulupilira Iye [asatayike, koma] akhale nawo moyo wosatha. 16Pakuti Mulungu5 anakonda dziko lapansi, kotero Iye anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilira pa Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha. 17Pakuti Mulungu6 sanatume Mwana wake m’dziko lapansi kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe mwa Iye. 18Wokhulupilira mwa Iye saweruzidwa: koma iye wosakhulupilira waweruzidwa kale, chifukwa sanakhulupilire pa dzina la Mwana wake wobadwa yekha wa Mulungu7. 19Ndipo chimenechi ndi chiweruzo, kuti kuunika kunabwera m’dziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima kusiyana ndi kuunika; pakuti ntchito zawo zinali zoipa. 20Pakuti aliyense wochita zoipa adana ndi kuunika, ndipo sabwera ku kuunika, kuti ntchito zake zisakaonetsedwe monga iwo alili; 21koma iye amene achita choonadi abwera ku kuunika, kuti ntchito zake zikawonetsedwe kuti zichitidwa mwa Mulungu8.
22Zitapita izi anabwera Yesu ndi ophunzira ake m’dziko la Yudeya; ndipo kumeneko anakhala nawo pamodzi ndi kubatiza. 23Ndipo Yohane amabatiza m’Ainoni, pafupi ndi Salimu; chifukwa panali madzi ochuluka pamenepo; ndipo iwo anabwera kwa [iye] nabatizidwa: 24pakuti Yohane anali asanaponyedwe m’ndende. 25Panali pamenepo kufunsana pa ophunzira a Yohane ndi Myuda za mayeretsedwe. 26Ndipo iwo anadza kwa Yohane nati kwa iye, Rabi, uyo amene anali ndi inu kutsidya la Yordano, amene munachitira umboni za Iye, taonani, akubatiza, ndipo onse akubwera kwa Iye. 27Yohane anayankha nati, Munthu sangalandire kanthu pokhapokha katapatsidwa kwa iye kuchokera kumwamba. 28Inu nokha mundichitira umboni kuti ndinati, Sindine Khristu, koma, kuti ndatumidwa patsogolo pake. 29Iye amene ali naye mkwatibwi ndi mkwati; koma mzake wa mkwati, amene ayima ndi kumva iye, akondwera mu mtima mwake chifukwa cha mau a mkwati: chimwemwe changa ichi chakwaniridwa. 30Iye akule, koma ine ndichepe. 31Iye wakudza kuchokera kumwamba aposa onse, 32[ndipo] zimene waona ndi kumva, zimenezi achitira umboni; ndipo palibe amene alandira umboni wake. 33Iye amene walandira umboni wake anaikapo chitsindikizo kuti Mulungu9 ndi woona; 34pakuti iye amene Mulungu10 wamtuma amalankhula mau a Mulungu11, pakuti Mulungu12 sapereka Mzimu mwa muyeso. 35Atate akonda Mwana, ndipo wapereka zinthu zonse [kukhala] m’manja mwake. 36Iye amene akhulupilira pa Mwana ali nawo moyo wosatha, ndipo amene sakhala pansi pa ulamuliro wa Mwana sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu13 ukhala pa iye.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu12Elohimu13Elohimu