Mutu 7

1Ndipo Afarisi ndi ena mwa alembi, pochokera ku Yerusalemu anasonkhanira pamodzi kwa Iye, 2ndipo poona ena mwa ophunzira ake akudya mkate mwa umve, ndiko kuti, osasamba m’manja, 3(pakuti Afarisi ndi Ayuda onse, pokhapokha ngati asamba m’manja bwino lomwe, samayenera kudya kanthu, kusamalira chimene chinaperekedwa ndi makolo; 4ndipo [pobwera] kuchokera ku msika, pokhapokha ngati asamba mthupi, iwo sakuyenera kudya; ndipo pali zinthu zina zambiri zimene iwo anazilandira kuzigwiritsitsa, matsukidwe a zikho ndi mitsuko, ndi ziwiya komanso zotengera za mkuwa), 5pamenepo Afarisi ndi alembi anamfunsa Iye, Chifukwa chiyani ophunzira anu samayenda kolingana ndi zimene zinaperekedwa ndi makolo kale, koma amadya mkate ndi m’manja mwakuda? 6Koma Iye poyankha anati kwa iwo, Mneneri Yesaya analosera molondola zokhudza inu achinyengo, monga kunalembedwa, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo ili kutali ndi Ine. 7Komatu mwachabe iwo andipembedza ine, kuphunzitsa [monga] aphunzitsa malamulo a anthu. 8 [Pakuti], pakusiya malamulo a Mulungu1, mugwiritsitsa chimene chaperekedwa ndi anthu [kuchisunga] — kuchapa ziwiya ndi zikho, ndi zinthu zina zambiri monga zimene muchita. 9Ndipo Iye anati kwa iwo, Bwino lomwe musiya kumbali lamulo la Mulungu2, kuti mukasamale zimene zaperekedwa ndi inu eni [kukazisunga]. 10Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo, iye amene alankhula zoipa za atate wake kapena amake, ameneyo aphedwe ndithu. 11Koma inu munena, Ngati munthu anena kwa atate wake kapena amake, [kunena kuti] Korban (ndiko kutanthauza kuti, mphatso), chilichonse chimene uzapindula nacho kuchokera kwa ine mwa ... 12Ndipo simulolanso kumchitira kanthu iye kakuchitira atate wake ndi amake; 13kunyalapsa mau a Mulungu3 mwa chiphunzitso cha mwambo wanu chimene munachipereka; ndi zinthu zina zotere zimene muzichita. 14Ndipo pakuitananso khamu, Iye anati kwa iwo, Mverani Ine [inu nonse], ndipo zindikirani: 15Palibe chinthu chakuchokera kunja ndi kulowa mwa munthu chimene chingamudetse; koma zinthu zimene zituluka mwa iye, zimenezo ndi zomwe zimadetsa munthu. 16Ngati wina ali nawo makutu akumva, amve.

17Ndipo pamene Iye analowa mnyumba kusiyana ndi khamulo, ophunzira ake anamufunsa zokhudza fanizolo. 18Ndipo Iye anati kwa iwo, Kodi inunso ndinu opanda nzeru? Kodi inu simudziwa kuti zonse zochokera kunja ndi kulowa mwa munthu sizikhoza kumudetsa iye, 19chifukwa kuti sizilowa mumtima mwake koma m’mimba mwake, ndipo zimapita kuthengo, kutulutsa nyama yonse? 20Ndipo Iye anati, Chimene chimatuluka mwa munthu, chimenecho chimamudetsa munthu. 21Pakuti kuchokera mkati, kutuluka mumtima mwa munthu, mutuluka malingaliro oipa, za chigololo, za chiwerewere, za kupha, 22za kuba, masiliro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, malankhulidwe oipa, kudzikuza, kupusa; 23zinthu zonse zoipa izi zimatuluka mkati ndi kumudetsa munthu.

24Ndipo Iye anauka ndi kupita ku malire a Turo ndi Sidoni; ndipo atalowa m’nyumba sanafune wina aliyense adziwe za [ichi], ndipo Iye sanathe kubisala. 25Koma pomwepo mkazi, amene mwana wake anali ndi mzimu woipa, pakumva za Iye, anabwera nagwa pamazi ake 26(ndipo mkaziyu anali Mhelene, wa mtundu wa chi Surofonika), ndipo anamupempha kuti atulutse chiwanda mwa mwana wake. 27Koma [Yesu] anati kwa iye, Balola kuti ana akhute kaye; pakuti sikwabwino kuti titenge mkate wa ana ndi kuponyera kwa agalu. 28Ndipo anayankha nati kwa Iye, Inde, Ambuye; ngakhale agalu pansi pa gome amadya nyenyeswa za ana. 29Ndipo anati kwa iye, Chifukwa cha mawu awa, pita panjira yako, chiwanda chatuluka mwa mwana wako wamkazi. 30Ndipo atapita panjira yake kunyumba kwake iye anapeza chiwanda chitatuluka, ndipo mwana wake wa mkazi wakukhala pa kama.

31Ndipo atachokanso kumalire a Turo ndi Sidoni, Iye anafika kunyanja ya Galileya, kupyola mkatikati mwa magombe aku Dekapoli. 32Ndipo iwo anabweretsa kwa Iye [munthu] wogontha amenenso anali wachibwibwi, ndipo iwo anampempha kuti ayike dzanja lake pa iye. 33Ndipo atamuchotsa iye pakati pa khamulo, anayika dzala zake m’makutu mwake; ndipo atalavula, Iye anakhudza lilime lake; 34ndipo pakuyang’ana kumwamba anausa moyo, nanena naye, Efata, kutanthauza kuti, Tseguka. 35Ndipo pomwepo makutu ake anatseguka, ndipo chomangira lilime lake chinamasuka ndipo analankhula bwino lomwe. 36Ndipo anawalamulira iwo kuti asauze wina aliyense [za ichi]. Koma pamene Iye anawalamulitsa iwo, pomweponso iwo analankhulirabe za ichi; 37ndipo iwo anali ozizwa koposa muyeso, nanena, Iyeyu amapanga zinthu zonse bwino lomwe; amapangitsa osamva kumva, ndi osalankhula kulankhula.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu