Mutu 20
1Ndipo chipwirikiticho chitatha, Paulo anaziitanira ophunzira kwa [iye] ndipo anawachenjeza [iwo], napita ku Makedoniya. 2Ndipo pamene anadutsa mbali zina, ndipo atawalimbikitsa iwo ndi chiphunzitso chambiri, anafika ku Helene. 3Ndipo anakhala [kumeneko] kwa miyezi itatu, chiwembu chachikulu chinakonzedwera iye ndi Ayuda, pamene amakonzekera kupita ku Suriya pa ngalawa, chiganizo chinachitika chobwerera kudutsa ku Makedoniya. 4Ndipo kumeneko anaperekezedwa iye kufika mpaka ku Asiya, Suprato [mwana] wa Puro, m’Bereya; ndi wa Atesalonika, Aristarko ndi Sekundo, ndi Gayo ndi Timoteo waku Derbe, ndi waku Asiya, Tukino ndi Trofimo. 5Amenewa potsogola anatidikira ife m’Trowa; 6koma ife tinakwera ngalawa kuchoka ku Filipo atapita masiku a mkate wopanda chotupitsa, ndipo ife tinafika kwa iwo ku Trowa kwa masiku asanu, ndipo tinakhalako kwa masiku asanu ndi awiri. 7Ndipo tsiku loyamba la sabata, pokhala kuti tinasonkhana pamodzi kunyema mkate, Paulo anawaphunzitsa iwo, asananyamuke m’mawa mwake. Ndipo iye anatalikitsa chiphunzitso chake kufika pakati pa usiku. 8Ndipo munali nyali zambiri m’chipinda chapamwamba chimene tinasonkhana. 9Ndipo mnyamata wina, dzina lake Utiko, anakhala pazenera lotsegula, ndipo atagwidwa nato tulo tatikulu, anagwa kuchoka pa chipinda chosanjikana chachitatu kugwera pansi, ndipo anatoledwa atafa kale. 10Koma Paulo potsika anagwera pa iye, ndipo anamkupatira [m’manja mwake], nanena, Musadandaule pakuti moyo udakalimo mwa iyeyu. 11Ndipo atakwera m’mwamba, ananyema mkate, ndipo anadya, ndipo analankhula nthawi yaitali kufikira m’mawa mwake, kotero iye anachokako. 12Ndipo iwo anam’bweretsa mnyamatayo ali wamoyo ndipo anatonthozedwa osati pang’ono. 13Ndipo ife, pamene tinakwera ngalawa, tinapita ku Aso, tinapita kukamutenga Paulo kumeneko; pakuti iye anafotokozera, kuti adzayenda yekha ulendo wa pansi. 14Ndipo pamene anakumana nafe ku Aso, tinamutenga ndipo tinafika ku Mileto; 15ndipo tinakwera ngalawa kuchoka kumeneko, ndipo mawa mwake tinafika moyang’anana ndi Kiyo, ndipo tsiku lotsatilalo tinakhala ku Samo; ndipo titakhala ku Trogeliya, tsiku linalo tinafika ku Mileto: 16pakuti Paulo anaona chofunikira kupita ku Efeso, cholinga kuti asakhale ndi nthawi yokhala m’Asiya; pakuti iye anachita changu, ngati kunali kotheka kwa iye, kupezeka ku Yerusalemu patsiku la Pentekoste. 17Koma kuchokera ku Mileto potumizidwa ku Efeso, anadziitanira [kwa iye] akulu a mpingo. 18Ndipo pamene iwo anafika kwa iye, anati kwa iwo, Inu mukudziwa m’mene ndinalili ndi inu nthawi zonse kuyambira tsiku loyamba limene ndinafika m’Asiya, 19kutumikira Ambuye ndi kudzichepetsa konse, ndi misozi, ndi mayesero, zimene zinachitika kwa ine kudzera m’maupandu a Ayuda; 20m’mene sindinakubisireni kalikonse kamene kali kopindulitsa, kukulalikirani izi kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu poyera komanso mnyumba iliyonse, 21kuchitira umboni Ayuda ndi Ahelene omwe kulapa kupita kwa Mulungu1, ndi chikhulupiliro kupita kwa Ambuye Yesu Khristu. 22Ndipo tsopano, taonani, womangidwa mu mzimu wanga ndibwerera ku Yerusalemu, osadziwa zinthu zimene zikandichitikira ine kumeneko; 23kungoti Mzimu Woyera akandichitire umboni ine mzinda wina ulionse, kunena kuti nsinga ndi zisautso zikundidikira ine. 24Komatu sindiyesa moyo [wanga] kukhala wofunika kwa ine ndekha, kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi iwo amene ndakhala ndikuwalalikira ufumu [wa Mulungu2], simudzayionanso nkhope yanga. 25Ndipo tsopano, taonani, ndikudziwa kuti inu nonse, amene ndinapita pakati panu kulalikira uthenga [wa Mulungu3], simudzayionanso nkhope yanga. 26Pamenepo ndikuchitirani umboni kufikira lero, kuti ndili woyera ku mwazi wa onse, 27pakuti sindinakubisirani inu kulalikira uphungu onse wa Mulungu4. 28Pamenepo tadzichenjerani inu nokha, ndi kwa nkhosa zonse, zimene Mzimu Woyera anakuikani inu kukhala odziyang’anira, kusamalira mpingo wa Mulungu5, umene anaugula ndi mwazi wa Iye mwini. 29[Pakuti] ine ndidziwa [ichi], kuti idzabwera pakati panu ine nditachoka mimbulu yoopsa, imene idzaononga gulu la nkhosa; 30ndipo pakati panu adzauka amuna olankhula zinthu zokhotakhota kuwapatutsa ophunzira kuti awatsatire iwo. 31Chomwecho yang’anirani, pokumbukira kuti zaka zitatu, usiku ndi usana, sindinaleke kukuchenjezani aliyense [wa inu] ndi misozi. 32Ndipo tsopano ndikuperekani inu kwa Mulungu6, ndi ku mau a chisomo chake, amene ali akutha kukumangilirani [inu] ndi kukupatsani [inu] cholowa pakati pa onse oyeretsedwa. 22Ine sindinasilire siliva kapena golide kapena chovala cha wina aliyense. 34Inu nokha mukudziwa kuti manja anga awa atumikira ku zosoweka zanga, ndi iwo amene anali ndi ine. 35Ndakuonetsani inu zinthu zonse, kuti pogwira ntchito [ife] tikuyenera kuthandizira ofooka, ndi kukumbukira mau a Ambuye Yesu, kuti Iye mwini anati, Kupereka kutidalitsa koposa kulandira.
36Ndipo pamene ananena zinthu izi, anagwada pansi napemphera ndi iwo onse. 37Ndipo iwo onse analira kwambiri; ndipo iwo anagwira pakhosi pa Paulo nampsopsona iye, 38makamaka anapwetekedwa ndi mau amene iye analankhula, kuti iwo sadzaionanso nkhope yake. Ndipo iwo anapita naye pamodzi ku ngalawa.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu