Mutu-2

1Abale anga, musakhale nacho chikhulupiliro cha Ambuye wathu Yesu Khristu, [Ambuye] wa ulemelero, ndi ulemu wa anthu: 2pakuti ngati abwera m’sunagoge mwanu munthu wokhala ndi mphete ya golide ndi zovala zokongola, ndi munthunso wosauka abwera mu zovala zoyipa, 3ndipo inu muyang’anira pa iye amene wavala zovala zokongola, ndi kunena, Khalani pano pabwino, ndi kunena kwa wosaukayo, Inu imani apo, kapena khalani pansi pa mpando wa mapazi anga: 4kodi simunasiyanitse pakati panu, ndi kukhala oweruza okhala nawo malingaliro oipa? 5Tamverani, abale anga okondedwa: Kodi Mulungu1 sanasankhe osauka monga kwa dziko lapansi, kulemera m’chikhulupiliro, ndi olowa mnyumba a ufumu, umene iye analonjeza kwa iwo amene amkonda iye? 6Koma inu mwanyoza munthu wosauka. Kodi achuma samakuponderezani inu, ndipo samakutengerani ku mabwalo a milandu? 7Ndipo sachitira mwano dzina labwino limene muyitanidwa nalo? 8Ngatidi musunga lamulo la chifumu monga mwa lemba, Uzikonda mzako monga uzikonda wekha, muchita bwino. 9Koma ngati muchitira ulemu munthu, mukuchimwa, mutsutsidwa ndi lamulo monga olakwa. 10Pakuti amene asunga lamulo lonse nakhumudwa pa limodzi, iye wapezeka wolakwa kuti waphwanya onse. 11Pakuti iye amene anena, Usachite chigololo, anenanso, Usaphe. Tsopano ngati inu simuchita chigololo, koma mumapha, mwakhala wolakwira lamulo. 12Chomwecho lankhulani inu, ndi kuchitanso, monga iwo amene adzaweruzidwa ndi lamulo la ufulu; 13pakuti chiweruzo chidzakhala chopanda chifundo kwa iye amene sanaonetse chifundo. Chifundo chimapambana chiweruzo.

14Phindu lake ndi chiyani, abale anga, ngati wina anena kuti ali ndi chikhulupiliro, koma alibe kuonetsa ntchito? Kodi chikhulupiliro chikhoza kumpulumutsa? 15Tsopano ngati m’bale kapena mlongo ali wamaliseche nasowa chakudya cha tsiku limenelo, 16ndipo wina pakati panu nanena kwa iwo, Pitani mu mtendere, kadzifunditseni ndi kukhuta; koma osawapatsa iwo zinthu zofunika za thupi, phindu lake ndi chiyani? 17Momwemonso chikhulupiliro, ngati sichionetsa ntchito, ndi chakufa pa chokha. 18Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiliro ndipo ine ndili nazo ntchito. Ndionetseni chikhulupiliro chanu chopanda ntchito, ndipo ine ku ntchito zanga ndikuonetserani chikhulupiliro changa. 19Inu mumakhulupilira kuti Mulungu2 ndi m’modzi. Mumachita bwino. Ziwanda zimakhulupiliranso, ndi kunjenjemera. 20Koma ufuna kudziwa kodi, iwe munthu wopanda pake, kuti chikhulupiliro chopanda ntchito ndi chakufa? 21Kodi atate wathu Abrahamu sanalungamitsidwe ndi ntchito pamene anapereka nsembe Isake mwana wake pa guwa? 22Uwona kuti chikhulupiliro chinachita pamodzi ndi ntchito zake, ndi kuti mwa ntchito chikhulupiliro chidakhala changwiro. 23Ndipo lemba linakwaniritsidwa limene limati, Abrahamu anakhulupilira Mulungu3, ndipo chinatengedwa kwa iye monga chilungamo, ndipo iye anatchedwa Bwenzi la Mulungu4. 24Upenya kuti munthu amalungamitsidwa pa mfundo ya ntchito, ndipo osati pa mfundo ya chikhulupiliro chokha. 25Koma sikunali chimodzimodzinso ndi Rahabe mkazi wa dama analungamitsidwa pa mfundo ya ntchito, pamene iye analandira amthenga nawaturutsa kudutsa njira ina? 26 Pakuti monga thupi lopanda mzimu ndi lakufa, chomwechonso chikhulupiliro chopanda ntchito ndi chakufa.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu