Mutu 15

1Komatu ndikudziwitsani inu, abale, uthenga wabwino umene ndinakulalikirani, umenenso inu munaulandira, umenenso inu muyimapo, 2umenenso munapulumutsidwa nawo, (ngati mudzagwiritsitsa mau amene ine ndinakulalikirani monga uthenga wabwino,) pokhapokha ngati munakhulupilira pachabe. 3Pakuti ndinapereka kwa inu, poyambilira chimenenso ine ndinalandira, kuti Khristu anafa chifukwa cha machimo athu, molingana ndi malemba; 4ndipo kuti anayikidwa m’manda; ndipo kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, molingana ndi malemba; 5ndipo kuti anaonekera kwa Kefa, kenako kwa khumi ndi awiriwo. 6Kenako Iye anaonekera kwa abale oposa mazana asanu nthawi imodzi, amene ambiri a iwo adakalipo kufikira tsopano, koma ena anagona tulo. 7Kenako anaonekera kwa Yakobo; kenako kwa atumwi onse; 8ndipo kumapeto kwa onse, monga mtayo, anaonekeranso kwa ine. 9Pakuti ndine wamng’ono mwa atumwi, amene sindili woyenera kutchedwa mtumwi, chifukwa ine ndinazunzako mpingo wa Mulungu1. 10Koma mwa chisomo cha Mulungu2 ndine amene ndili; ndipo chisomo chake, chimene chinali pa ine, sichinakhale chabe; koma ine ndagwira ntchito kwambiri kuposa onsewa, komatu osati ine, koma chisomo cha Mulungu3 chimene chinali ndi ine. 11Pamenepo kaya ndi ine kapena iwowo, talalikira ndipo inu mwalandira uthengawo. 12Tsopano ngati Khristu alalikidwa kuti anaukitsidwa kwa akufa, nanga bwanji pakati panu ena anena kuti kulibe kuuka kwa akufa? 13Koma ngati kulibe kuuka kwa akufa, ndiye kuti Khristu sanauke: 14koma ngati Khristu sanauke, pamenepo, ndiye kuti kulalikira kwathu kuli chabe, ndipo chikhulupiliro chanunso chili chabe. 15Ndipo tipezekanso kuti ndife mboni zabodza za Mulungu4; pakuti ife tachitira umboni zokhudza kuti Mulungu5 anamuukitsa Khristu, amene Iye sanamuukitsa ngatidi iwo akufa saukitsidwa kwa akufa. 16Pakuti ngati [iwo amene] anafa saukitsidwa, ndiye kuti Khristu sanaukitsidwe; 17Koma ngati Khristu sanaukitsidwe, chikhulupiliro chanu chili chabe; inu mudakali mu uchimo wanu. 18Pamenepo indedi iwonso amene anagona mwa Khristu anaonongeka. 19Ngati tili nacho chiyembekezo mwa Khristu m’moyo uno okha, ndife anthu omvetsa chisoni kwambiri pa anthu onse.

20(Koma tsopano Khristu waukitsidwa pakati pa akufa, zipatso zoyamba za iwo akugona. 21Pakuti monga ndi munthu imfa inadza, ndi munthunso kuuka kwa akufa kunadza. 22Pakuti monga mwa Adamu tonse tinafa, chomwechonso mwa Khristu tonse tidzakhala ndi moyo. 23Koma aliyense mwa ndondomeko yake: Chipatso choyambilira, Khristu; kenako iwo amene ali a Khristu pa kubwera kwake. 24Kenako pamapeto, pamene adzapereka ufumu kwa Iye [amene ali] Mulungu6 ndi Atate; pamene adzathetsa ufumu onse, ulamuliro onse ndi mphamvu yonse. 25Pakuti Iye akuyenera kulamulira kufikira atayika adani onse pansi pa mapazi ake. 26Mdani wotsiriza amene adzagonjetsedwa ndi imfa. 27Pakuti wayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake. Koma pamene Iye anena kuti zinthu zonse zayikidwa pansi pa ulamuliro wake, ndi umboni wakuti akuchotserapo Iye amene anayika zinthu zonse pansi pa ulamuliro kwa Iye. 28Koma pamene zinthu zonse zidzabweretsedwa pansi pa ulamuliro kwa Iye, pamenepo Mwananso mwiniyekha adzayikidwa pansi pa ulamuliro kwa Iye amene amayika zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, kuti Mulungu7 akhale zonse m’zonse.)

29Ngati sikutero kodi adzatani obatizidwa pa akufa ngati iwo amene anafa sadzaukanso konse? Nanga chifukwa chiyani akubatizidwa pa iwo? 30Chifukwa chiyani tiyika moyo wathu pa chiopsezo ola lililonse? 31Ndimafa tsiku ndi tsiku, pa kudzitamandira kwanu kumene ndili nako mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. 32Ngati, [ndilankhula] monga mwa munthu, ndalimbana nazo zilombo mu Efeso, nanga pali phindu lanji kwa ine ngati [iwo amene] anafa sadzaukanso? Tiyeni tidye ndi kumwa; pakuti mawa tifa ndithu. 33Musanyengeke: maubwenzi oyipa amaononga makhalidwe abwino, 34Ganizirani moyenera, ndipo musachimwe; pakuti ena ndi mbuli pa za Mulungu8: ndikuIankhula izi kuti muchite manyazi.

35Koma wina adzati, Kodi akufa adzaukitsidwa bwanji? Ndipo adzaukitsidwa ndi thupi lotani? 36Wopusa iwe; chimene umadzala sichikhala ndi moyo pokhapokha chitafa. 37Ndipo chimene umafetsa, sumafetsa thupi limene lidzakhala, koma mbewu yokha: ikhoza kukhala ya tirigu, kapena ya mtundu wina: 38ndipo Mulungu9 amayipatsa iyo thupi monga afunira, ndipo kwa mbewu iliyonse thupi lakelake. 39Mnofu uliwonse suli chimodzimodzi, pakuti wina ndi wa anthu, wina wa zirombo, ndi wina wa mbalame, ndi wina wa nsomba. 40Ndipo palinso matupi akumwamba, ndi matupi a dziko lapansi: koma kusiyana ndi kwakuti ulemelero wa kumwamba, ndi wina wa dziko lapansiso ndi winanso: 41wina uli ulemelero wa dzuwa, ndi wina ulemelero wa mwezi, ndi wina ulemelero wa nyenyezi; pakuti ulemelero wa nyenyezi yina umasiyana ndi yina. 42Chimodzimodzinso kuuka kwa akufa. Lifetsedwa m’chivundi, ndipo lidzaukitsidwa m’chivundi. 43Lifetsedwa m’chitodzo, liwukitsidwa mu ulemelero. Lifetsedwa m’chifowoko, liwukitsidwa mu mphamvu. 44Lifetsedwa monga thupi la nyama, liwukitsidwa thupi la uzimu: ngati pali thupi la nyama, kulinso thupi la uzimu. 45Koteronso kwalembedwa, Munthu woyamba Adamu anakhala mzimu wamoyo; Adamu wotsiriza wopereka mzimu. 46Koma chimene chili cha uzimu sichinali choyamba, komatu chimene chili cha thupi, kenako chimene chili cha uzimu: 47munthu woyamba wochokera mu nthaka, wopangidwa ku dothi; munthu wachiwiri, kuchokera kumwamba. 48Monga anapangidwa kuchoka ku dothi, ateronso wa dothi, ndipo monga akumwamba, ateronso wa m’mwamba. 49Ndipo monga ife tinavala chifanizo cha iye wopangidwa ku dothi, tidzavalanso chifanizo cha wam’mwambayo. 50Koma ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingalowe ufumu wa Mulungu10, kapena chovunda kulowa m’chosavunda.

51Taonani, ndikuuzani chinsinsi: sitidzagona tulo tonse, koma tonse tidzasandulika, 52Mu kamphindi, m’kuthwanima kwa diso, ku lipenga lomalidza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa m’chosavunda, ndipo ife tidzasandulika. 53Pakuti chovunda ichi chikuyenera kuvala chosavunda, ndi chakufa kuvala chosafa. 54Koma pamene chovunda chivala chosavunda, ndi chakufa kuvala chosafa, pamenepo adzakwaniritsidwa mau olembedwa: Imfa yamezedwa m’chipambano. 55Ili kuti mbola yako imfa iwe? Chili kuti chipambano chako, imfa iwe? 56Tsopano mbola ya imfa ndi tchimo, ndipo mphamvu ya tchimo ndi lamulo; 57koma alemekezeke Mulungu11, amene amatipatsa ife chipambano mwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 58Tsopano pamenepo, abale anga okondeka, chilimikani, musatekeseke, kukhazikikabe nthawi zonse mu ntchito ya Ambuye, podziwa kuti kugwiritsa ntchito kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu