Mutu 1

1Mulungu1 atalankhula m’magawo ochuluka ndi mnjira zosiyanasiyana kalelo kwa makolo athu mwa aneneri, 2pamapeto a masiku amenewa analankhula kwa ife mwa [munthu] Mwana, amene anakhazikitsidwa wolowa mnyumba wa zinthu zonse, mwa amenenso analenga maiko; 3ameneyo pokhala chinyezimiro cha ulemelero wake ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, ndi kunyamula zinthu zonse mwa mau a mphamvu yake, nachita [mwa iye yekha] chiyeretso cha machimo, naziika yekha padzanja lamanja la ukulu m’mwamba, 4kutenga malo abwino kuposa angelo, pamene adalowa dzina labwino loposa kusiyana ndi iwo. 5Pakuti ndi kwa mngelo uti ananena nthawi zonse, Ndiwe Mwana wanga: lero ndakubereka iwe? Ndi kutinso, Ine ndidzakhala kwa iye atate, ndipo iye adzakhala kwa ine mwana? 6ndi kutinso, pamene iye abweretsa mwana wamwamuna woyamba kulowa naye mdziko lokhalamo, iye akuti, Ndipo angelo onse a Mulungu2 alambire iye. 7Ndipo monga kwa angelo iye anena, Iye amene ayesa angelo ake mizimu ndi atumiki ake lawi lamoto; 8koma monga kwa Mwana, mpando Wanu wa chifumu, Mulungu3, ufikira ku nthawi za nthawi zonse, ndipo ndodo ya chifumu yoongoka ndiyo ndodo ya chifumu ya ufumu wanu. 9Inu munakonda chilungamo ndipo munadana nacho choipa; pamenepo Mulungu4, Mulungu5 wanu, anakuzodzani ndi mafuta a chikondwerero pamwamba pa anzanu onse. 10Ndipo, inu pachiyambi, Ambuye, munalenga dziko lapansi, ndipo ntchito ya manja anu ndiyo miyamba. 11Iwo adzaonongeka, koma inu mudzakhalitsabe; ndipo iwo onse adzaguga monga chovala, 12ndipo monga chophimba mudzawapiringiza onse, ndipo iwo adzasinthika; koma inu muli chimodzimodzi, ndipo zaka zanu sizizatha. 13Koma ndani mwa angelo ananena nthawi zonse, Khala kudzanja langa lamanja kufikira ndidzaika adani ako kukhala chopondapo mapazi ako? 141kodi iwo sali mizimu yotumikira, kutumizidwa kukatumikira chifukwa cha iwo amene adzalowa chipulumutso?

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu