Mutu 10

1Pakuti lamulo, pokhala nacho chithunzithunzi cha kubwera kwa zinthu zabwino, osati chifanizo cha zinthuzo, silinakhoza, mwa nsembe yomweyo imene amapereka mowirikiza chaka ndi chaka, kuwalungamitsa iwo akuwandikira. 2Chifukwa, iwo akanalekadi kudzipereka, m’malo mwa olambira sakanakhala nacho chikumbumtima chilichonse cha machimo? 3Koma mu zimenezi pali chikumbutso cha machimo chaka ndi chaka. 4Pakuti mwazi wa ng’ombe za mphongo ndi mbuzi sungakwanitse kuchotsa machimo. 5Pamenepo pobwera m’dziko lapansi anati, Nsembe ndi chopereka simunazifune ayi; koma inu mwandikonzera ine thupi. 6Inu simukondwera mu nsembe zopsereza ndi nsembe ya uchimo. 7Pamenepo ndinati, Taonani ndafika monga kwalembedwa za ine m’pukutu wa buku) kuchita, chifuniro chanu, inde Mulungu1. 8Pamwamba, kunena za Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza ndi nsembe za uchimo inu simufuna zimenezo, kapena kukondweramo (zimene zaperekedwa molingana ndi lamulo); 9kenako anati, Taonani, ndabwera kudzachita chifuniro chanu. Iye anachotsa loyambalo kuti akakhazikitse lachiwiri; 10pa limenelo ife tikayeretsedwe kudzera muchopereka cha thupi la Yesu Khristu kamodzi kokha kwatha. 11Ndipo wansembe aliyense amayima tsiku ndi tsiku kutumikira, ndi kupereka kawirikawiri nsembe zomwezomwezo, zimene sizingachotse machimo. 12Koma iye, pamene anapereka nsembe imodzi pa machimo, nakhala pansi kwamuyaya kudzanja lamanja la Mulungu2, 13kudikira kuyambira tsopano kufikira adani ake akhazikitsidwe kukhala chopondapo mapazi ake. 14Pakuti ndi chopereka chimodzi anakwaniritsa kosatha iwo oyeretsedwa. 15Ndipo Mzimu Woyera amatichitiranso umboni [wa ichi]; pakuti zitatha zonenedwazo: 16Limeneli ndi pangano limene ndidzakhazikitsa kwa iwo atapita masiku amenewo, atero Ambuye: Kupereka malamulo anga m’mitima mwao, ndiwalembanso m’kumvetsetsa kwao; 17ndipo machimo awo ndi kusamvera kwao sindidzakumbukiranso. 18Koma pamene pali chikhululukiro cha izi, palibeponso nsembe ya uchimo.

19Chomwecho pokhala nako, abale, kulimbika mtima polowa m’malo oyeretsetsa mwa mwazi wa Yesu, 20njira yatsopano ndi yamoyo imene wayikhazikitsa kwa ife kudzera mu chotchinga, chimene chili, thupi lake, 21ndipo [pokhala naye] wansembe wamkulu woyang’anira nyumba ya Mulungu3, 22tiyeni tiwandikire ndi mtima woonadi, m’chitsimikizo chonse cha chikhulupiriro, chowazidwa ku mitima yathu kuchokera ku chikumbumtima choipa, ndi kusambitsidwa kwa thupi lathu ndi madzi oyera. 23Tiyeni tigwiritsitse chivomerezo cha chiyembekezo chosasunthika, (pakuti iye [ali] wokhulupirika amene anatilonjeza;) 24ndipo tiyeni tiganizirane wina ndi mzake pakutakasana m’chikondi ndi ntchito zabwino; 25osasiya kusonkhana kwathu pamodzi, monga ena achitira; koma kulimbikitsana wina ndi mzake, ndipo monga muona kuti tsiku likuyandikira. 26Pakuti pamene tichimwa mwakufuna pamene talandira chidziwitso cha choonadi, sipatsalanso nsembe iliyonse ya machimo, 27koma kudikira kwina koopsa kwa chiweruzo, ndi kutentha kwa moto umene udzaononga adaniwo. 28Aliyense amene adzanyozera lamulo la Mose adzafa wopanda kuchitidwa chifundo pakati pa mboni ziwiri kapena zitatu: 29nanga koposa kotani adzalandira chilango, muganiza inu, naweruzidwa koyenera iye amene anapondereza pansi pa mapazi a Mwana wa Mulungu4, ndi mwazi wolemekezeka wa pangano, umene iye wayeretsedwa nawo, nauyesa wamba, ndipo nanyazitsa Mzimu wa chisomo? 30Pakuti ife timdziwa amene anati, Kwa ine [kuli] kubwenzera; ndidzabwezera, atero Ambuye: nditeronso, Ambuye adzaweruza anthu ake. 31Ndi chinthu choopsa kugwa m’dzanja la Mulungu5 wa moyo.

32Koma lingalirani masiku anu oyambilira amene, powunikiridwa, inu munapilira kwambiri chitsutsano chachikulu cha zowawa; 33mbali inayi, pamene inu munapangidwa kukhala chionetsero m’zonyoza ndi m’sautso; ndiponso mbali inayi, pamene munakhala otenga nawo gawo pamodzi ndi iwo amene akudutsa mzoterezi. 34Pakuti inu munawamvera chisoni andende ndipo munavomereza ndi chimwemwe kulandidwa kwa katundu wanu, podziwa kuti muli nazo zinthu zoposa, zokhazikika. 35Pamenepo musataye chidaliro chanu, chimene chili nawo malipiro akulu. 36Pakuti mwasowekera chipiliro cholinga kuti, pochita chifuniro cha Mulungu6, mukalandire lonjezano. 37Pakutibe kwatsala kanthawi pang’ono pamene iye wakudzayo adzabwera, ndipo sadzachedwa. 38Koma wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiliro; ndipo, ngati abwerera, moyo wanga sungakondwere mwa iye. 390 Koma sindife wobwerera m’mbuyo ku chiwonongeko, koma a chikhulupiliro kukapulumutsa moyo.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu