Mutu 2

1Kwa mngelo wa mpingo waku Efeso lemba: Anena zinthu izi iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri kudzanja lake lamanja, amene amayenda pakati pa nyali za golide zisanu ndi ziwiri:

2Ine ndidziwa ntchito zako ndi kulimbika kwako, ndi kupilira kwako, ndi kuti sukhoza kulola [anthu] oipa; ndipo unawayesa iwo akunena okha kuti ali atumwi ndipo sali choncho, ndipo unawapeza iwo kukhala abodza; 3ndipo wapilira, ndi chipiliro chifukwa cha dzina langa, ndipo sunaleme: 4koma ndili nako kotsutsana nawe, kuti wataya chikondi chako choyamba. 5Pamenepo kumbukira pamene wagwera, ndi kulapa, ndipo uchite ntchito zako zoyamba: koma ngati sichoncho, ndibwera kwa iwe, ndipo ndidzachotsa nyali yako pa choikapo chake, pokhapokha utalapa. 6Koma ichi uli nacho, kuti udana nazo ntchito za Anikolayi, zimenenso ine ndidana nazo.

7Iye amene ali nalo khutu, amve chimene Mzimu anena kwa mipingo. Kwa iye amene agonjetsa, ndidzampatsa kudya za mu mtengo wamoyo umene uIi m’paradiso wa Mulungu1.

8Ndipo kwa mngelo wa mpingo m’Smurna lemba: Zinthu izi anena woyamba ndi wotsiriza, amene anafa, nakhala ndi moyo:

9Ine ndidziwa chisautso chako ndi umphawi wako; komatu ndiwe wolemera; ndi chipongwe cha iwo amene amazitchula okha kuti ali Ayuda, ndipo sali Ayuda, koma a sunagoge wa Satana. 10Usaope za zimene uzamva kuwawa. Taona, mdierekezi afuna kukuponya iwe m’ndende, kuti ukayesedwe; ndipo udzakhala pa chisautso kwa masiku khumi. Khala okhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.

11Iye amene ali nalo khutu, amve zimene Mzimu anena ku mipingo. Iye wakugonjetsa sadzaonongeka mwanjira ina iliyonse ndi imfa yachiwiri.

12Ndipo kwa mngelo wa mpingo waku Pergamo lemba: Zinthu izi anena iye amene ali ndi lupanga lakuthwa konsekonse:

13Ndidziwa kumene iwe umakhaIa, kumene mpando wachifumu wa Satana [uli]; ndipo iwe wagwiritsitsa dzina langa, ndipo sunakane chikhulupiliro changa, ngakhale m’masiku amene Antipa mboni yanga yokhulupirika [anali], amene anaphedwa pakati panu, kuja kumene amakhala Satana. 14Koma ndili nazo zinthu zochepa zotsutsana nawe: kuti muli nawo kumeneko amene asunga chiphunzitso cha Balamu, amene anaphunzitsa Balaki kutcherera msampha ana a Israeli, kudya [za] nsembe ya mafano ndi kuchita chigololo. 15Chomwechonso uli nawo iwo akusunga chiphunzitso cha Anikolayi mofanana. 16Ulape pamenepo: koma ngati sutero, ndidza msanga kwa iwe, ndipo ndidzachita nawo nkhondo ndi lupanga la pakamwa panga.

17Iye amene ali nalo khutu, amve chimene Mzimu anena ku mipingo. Kwa iye amene agonjetsa, kwa iye ndidzampatsa mana obisika; ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndipo pa mwalawu padzalembedwa dzina latsopano, limene wina aliyense salidziwa koma iye yekha amene waulandira.

18Ndipo kwa mngelo wa mpingo wa m’Tiyatira lemba: Zinthu izi anena Mwana wa Mulungu2, iye amene ali ndi maso ngati lawi la moto, ndipo mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira:

19Ndidziwa ntchito zako, ndi chikondi, ndi chikhulupiliro, ndi utumiki wako, ndi kupilira kwako, ndi kuti ntchito zako zomaliza [zikhala] zoposa zoyambazo. 20Koma ndili nako kokutsutsa iwe kuti unamulola mkazi Yezebeli, amene anadzitcha yekha mneneri wamkazi, ndipo akuphunzitsa ndi kusocheretsa akapolo anga kuchita chigololo ndi kudya zoperekedwa ku nsembe ya mafano. 21Ndipo ndinamupatsa nthawi kuti alape, ndipo iye sakulapa za chigololo chake. 22Taona, ndimponya iye pakama, ndipo iwo amene achita naye chigololo adzakhala naye m’chisautso chachikulu, pokhapokha atalapa ku ntchito zake, 23ndipo ana ake ndidzawakantha ndi imfa; ndipo mipingo yonse idzadziwa kuti ndine amene ndimasanthula impso ndi mitima; ndipo ndidzakupatsani aliyense wa inu molingana ndi ntchito zanu. 24Koma kwa inu ndinena, nonse amene muli m’Tiyatira, nonse amene mulibe chiphunzitso ichi, amene simunadziwe kuzama kwake kwa Satana, monga iwo anena, sindikuyikizani mtolo wina ulionse pa inu; 25koma chimene inu mwachigwiritsitsa kufikira ine nditabwera. 26Ndipo iye amene agonjetsa, ndipo iye wakusunga ntchito zanga kufikira mapeto, kwa iye ndidzampatsa ulamuliro pa mafuko onse, 27ndipo iye adzawaweta iwo ndi ndodo ya chitsulo; monga mbale za dothi za woumba zisweka, monganso ndalandira kuchokera kwa Atate anga; 28ndipo ndidzampatsa iye nyenyezi ya nthanda.

292 Iye amene ali ndi khutu, amve zimene Mzimu anena ku mipingo.

1Elohimu2Elohimu