Mutu 21

1Ndipo ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; pakuti kumwamba koyamba ndi dziko lapansi loyamba zinachoka, ndipo nyanja sinapezekenso.

2Ndipo ndinaona mzinda woyera, Yerusalemu watsopano, akutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu1, wokonzedwa monga mkwatibwi kukonzedwera mwamuna wake. 3Ndipo ndinamva mau ofuula kuchokera kumwamba, nanena, Taona, chihema cha Mulungu2 [chili] ndi anthu, ndipo iye adzakhaliramo ndi iwo, ndipo iwo adzakhala anthu ake, ndipo Mulungu3 mwini adzakhala ndi iwo, Mulungu4 wao. 4Ndipo adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwao; ndipo imfa sidzapezekanso, kapena chisoni, kapena kulira, kapena mavuto sadzapezekanso, pakuti zoyambazo zapita. 5Ndipo iye wakukhala pa mpando wa chifumu anati, Taonani, ndipanga zinthu zonse kukhala zatsopano. Ndipo anati [kwa ine], pakuti mau amenewa ndi oona ndi okhulupirika. 6Ndipo iye anati, Zatheka. Ndine Alefa ndi Omega, chiyambi ndi chitsiriziro. Ndidzapereka kwa iye wakumva Iudzu kasupe wa madzi a moyo kwaulere. 7Iye wakugonjetsa adzalandira zinthu zimenezi, ndipo ndidzakhala kwa iye Mulungu5, ndipo iye adzakhala kwa ine mwana. 8Koma kwa amantha ndi osakhulupilira, [ndi ochimwa], ndi iwo akuziipsa okha, ndi akupha, ndi achigololo, ndi amatsenga, ndi opembedza mafano, ndi onse abodza, gawo lawo [lili] m’nyanja yoyaka ndi moto ndi sulfure; imene ili imfa yachiwiri.

9Ndipo anabwera m’modzi wa angelo asanu ndi awiri aja amene anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri zodzadza ndi milili isanu ndi iwiri yotsiriza, ndipo analankhula ndi ine, nanena, Bwera kuno, ndikuonetsa mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa. 10Ndipo ananditenga ine mu Mzimu, [ndipo anandikhazika] paphiri lalikulu ndi lalitali, ndipo anandionetsa mzinda woyera, Yerusalemu, wakutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu6, 11wokhala nawo ulemelero wa Mulungu7. Kuwala kwake [kunali] ngati mwala wamtengo wapatali zedi, wonyezimira ngati mwala wa yasipi; 12wokhala nacho chipupa chachikulu ndi chachitali; wokhala ndi zipata khumi ndi ziwiri, ndipo pa zipatapo panali angelo khumi ndi awiri, ndi maina olembedwapo, amene ndi a iwo a mafuko khumi ndi awiri a mtundu wa ana a Israeli. 13Chakuvuma zipata zitatu; ndipo cha kumpoto zipata zitatu; ndipo cha kumwera zipata zitatu; ndipo cha kuzambwe zipata zitatu. 14Ndipo chipupa cha mzindawo chinali ndi maziko makumi ndi awiri, ndipo pamenepo maina khumi ndi awiri analembedwa maina a atumwi khumi ndi awiri a Mwanawankhosa.

15Ndipo iye wakulankhula ndi ine anali nalo bango la golide [monga] muyeso, kuti ayese mzindawo, ndi zipata zake, ndi chipupa chake. 16Ndipo mzindawo unali wotalika mofanana mbali zonse zinayi, ndipo mulitali mwake mofanana ndi mulifupi. Ndipo iye analinga mzindawo ndi bango — mastadiya zikwi khumi ndi awiri: mulitali ndi mulifupi ndi kutalika kwake zofanana. 17Ndipo anayesa chipupa chake, mikono zana mphambu makumi anayi kudza zinayi, muyeso wa munthu, ndiye, mngelo.

18Ndipo mamangidwe a chipupa chake [anali] yasipa; ndi mzinda wa golide, monga mandala oyera: 19maziko a chipupa cha mzindawo [anali] okongoletsedwa ndi miyala yonse ya mtengo wapatali: maziko woyamba, yasipa; achiwiri, safiro; achitatu, kalikedo, achinayi, smaragido; 20achisanu, sardonu; achisanu ndi chimodzi, sardiyo; achisanu ndi chiwiri, krusolito; achisanu ndi chitatu, berulo; achisanu ndi chinayi, topaziyo; akhumi, krusoprazo; akhumi ndi chimodzi, huakinto; akhumi ndi chiwiri, ametusto. 21Ndipo zitseko khumi ndi ziwiri, ngale khumi ndi ziwiri; chitseko chilichonse, pachokha, chinali cha ngale imodzi; ndipo msewu wa mzindawo unali ndi golide woyengeka, ndipo owonekera ngati mandala. 22Ndipo sindinaonemo kachisi m’menemo; pakuti Ambuye Mulungu8 Wamphamvuyonse ndiye kachisi wake, ndi Mwanawankhosa. 23Ndipo mzindawo sunasowekere dzuwa kapena mwezi, kuti ziwalire m’menemo; pakuti ulemelero wa Mulungu9 wawalitsa mzindawo, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa. 24Ndipo mafuko adzayenda mwa kuunika kwake; ndipo mafumu adziko lapansi adzapereka ulemelero wao pa mzindawo. 25Ndipo zipata zake sizizatsekedwa konse masana, pakuti usiku suzakhalako kumeneko. 26Ndipo iwo adzapereka ulemelero ndi ulemu wa amitundu kwa mzindawo. 27 Ndipo kanthu wamba, kapena kakuchita chonyansa ndi bodza, sikadzalowa m’menemo; komatu okhawo amene alembedwa m’buku la moyo la Mwanawankhosa.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu