Mutu 8
1Tsopano kuomba mkota pa zinthu zimene ife tikulankhula [ndiko], Tili naye wamkulu wansembe amene wakhala pansi kudzanja lamanja la mpando wachifumu waukulu m’miyamba; 2mtumiki wa malo opatulika ndi wa chihema choonadi, chimene Ambuye anachimanga [ndipo] osati munthu.
3Pakuti mkulu wa ansembe anayikidwa kupereka mphatso ndi nsembe; pamenepo nkofunika kuti ameneyunso akhale nacho china chake choti apereke. 4Ngatidi pamenepo iye akanakhala padziko lapansi, sakanakhala wansembe, pokhala iwo amene apereka mphatso molingana ndi lamulo, 5(amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zinthu zakumwamba, kolingana monga Mose anachenjezedwa [pamene] anafuna kumanga chihema; pakuti taona, atero Iye, kuti munapanga zinthu zonse molingana ndi ndondomeko imene inasonyezedwa kwa iwe m’phiri.) 6koma tsopano iye ali nawo utumiki wina woposa, mwa kutero monga iye ali mkhalapakati wa pangano labwino, limene lakhazikitsidwa pansi pa malonjezano oposa. 7Pakuti ngati loyambalo likanakhala lopanda polakwika, malo sakanapezeka a lachiwiliro. 8Popeza linapezeka lolakwika, iye anati kwa iwo, Taonani, masiku akubwera, atero Ambuye, ndipo ine ndizamalidzitsa pangano latsopano monga mwa nyumba ya Israeli, ndi monga mwa nyumba ya Yuda; 9osati monga mwa pangano limene ndinalipanga kwa makolo awo mu tsiku lija ndinawagwira padzanja kuwatsogolera kutuluka m’dziko la Aigupto; chifukwa iwo sanapitilize mu pangano langa, ndipo ine sindinawasamale iwo, atero Ambuye. 10Chifukwa limeneli [ndi] pangano limene ndidzapangana kunyumba ya Israeli atapita masiku amenewo, atero Ambuye: Kupereka malamulo m’malingaliro awo, ndiwalembanso pa mitima pawo; ndipo ndikhala kwa iwo Mulungu1, ndipo iwo adzakhala kwa ine anthu. 11Ndipo sadzaphunzitsana wina ndi mzake monga mzika, ndi wina m’bale wake, nanena, Mdziwe Ambuye; chifukwa onse adzandidziwa ine mwa wio okha, kuyambira wamng’ono [pakati pawo] kufikira wamkulu pakati pawo. 12Chifukwa ndidzachitira chifundo kusalungama kwao, ndi machimo awo ndi kusamvera kwao sindidzakumbukiranso. 13 M’menemo iye anena Latsopano, iye analipanga loyamba kukhala lakale; koma chimene chikuguga ndi kukalamba chikuyandikira kusowa.
1Elohimu