Mutu 10
1Koma ine mwini, Paulo, ndidandaulira inu mwakufatsa ndi kudzichepetsa kwa Khristu, ameneyo pakuoneka, [popezeka pakati panu] ndine wamng’ono, koma pamene ine palibepo ndine wolimba mtima kwa inu; 2koma ndipempha kuti pamene ndipezeka pakati panu ndisakhale wolimba mtima ndi chilimbiko chimene ndiganiza kuti chikayikitsa ena amene aganiza kuti ife timayenda monga mwa thupi. 3Pakuti poyenda m’thupi, sitimenya nkhondo molingana ndi thupi. 4Pakuti zida za nkhondo yathu sizathupi, koma za mphamvu molingana kwa 1Mulungu kuphwasula zimphamvu; 5kuphwasula malingaliro ndi maukulu onse amene amazikweza okha motsutsana ndi chidziwitso cha 2Mulungu, ndi kutsogolera lingaliro lililonse ku kumvera Khristu; 6ndi kukhala nako kukonzekera kubwezera kusamvera konse pamene kumvera kwanu kunayenera kukwaniritsidwa. 7Kodi mumayang’anira zimene zimakhudza maonekedwe? Ngati wina ali nako kulimbika kwa iye yekha kuti ali wa Khristu, aganizenso kawiri mwa iye yekha, kuti ngakhale ali wa Khristu, ifenso tili chimodzimodzi. 8Pakuti ngakhale ndizitamandira mu kenakake mochulukira ulamuliro wathu, umene Ambuye anapereka [kwa ife] kuti umangilire osati kuphwasula, sindizachititsidwa manyazi; 9kuti ndisaoneke ngati ndimakuopsezani m’makalata: 10chifukwa makalata ake, iye anena, [ndi] olemelera ndi amphamvu, koma kupezeka kwake mthupi ndi kofooka, ndi kulankhula kwake kwachabe. 11Wotereyu aganize motere, kuti pamene tili nawo mau mwa kalata pamene sitili pakati panu, moteronso pamene tipezeka pakati panu mu ntchito. 12Pakuti ife sitifuna kudzikweza tokha kapena kuzifanizira tokha ndi ena amene amazikweza okha; koma amenewa, amaziyesa okha mwa iwo okha, ndipo amazifanizira okha mwa iwo okha, sali anzeru. 13Tsopano ife sitizitamandira tokha mopitilira muyeso, koma molingana ndi mlingo wa ulamuliro umene 3Mulungu wa mlingo anatipatsa ife, kukufikiraninso inu. 14Pakuti ife sitifikira kwa inu monyanyamphira, (pakuti tabweranso kwa inu mu uthenga wabwino wa Khristu;) 15osati kuzitamandira mopyoza mu ntchito ya anthu ena, koma pokhala nacho chiyembekezo, chikhulupiliro chanu chichulukira, kukwezedwa pakati panu, kolingana ndi lamulo lathu, komabe mochulukira kwambiri 16kulalikira uthenga wabwino umene uli patsogolo panu, osati kuzitamandira m’kulamulira kwa zinthu za ena zokonzeka kale. 17Koma iye amene akuzitamandira, azitamandire mwa Ambuye. 18Pakuti iye amene azikweza yekha savomerezeka, koma iye yekhayo amene Ambuye amuvomereza.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu