Mutu 13

1Ndipo pamene Iye amatuluka m’kachisi, m’modzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, Mphunzitsi taonani miyala yotere ndi nyumba yotere! 2Ndipo Yesu poyankha anati kwa iye, Kodi waona nyumba zazikulu izi? Suzasiyidwa mwala wina pa umzake, umene sudzagwetsedwa. 3Ndipo pamene anakhala paphiri la Azitona moyang’anana ndi kachisi, Petro ndi Yakobo ndi Yohane ndi Andreya anamfunsa Iye mseri, 4Tatiuzeni ife, kodi zimenezi zizachitika liti, ndipo chizindikiro chake ndi chiyani pamene zonse izi zizakwaniritsidwa? 5Ndipo Yesu powayankha iwo anayamba kunena, Ziyang’anireni kuti wina asakusokeretseni. 6Pakuti ambiri adzabwera m’dzina langa, nadzanena, Ine ndine Iye, ndipo adzasocheretsa ambiri. 7Komatu pamene mudzamva za nkhondo ndi mphekesera za nkhondo, musamadere nkhawa, pakuti [chimenechi] chikuyenera kuchitika, komatu chitsiriziro sichinafike. 8Pakuti mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala zivomezi m’malo [osiyanasiyana], ndipo kudzakhala chilala ndi mavuto: zinthu zimenezi [ndizo] chiyambi cha zowawa. 9Koma inuyo, ziyang’anireni nokha, pakuti adzakuperekani kwa akulu a milandu ndi ku masunagoge: inutu mudzakwapulidwa ndi kuperekedwa pamaso pa oweruza ndi mafumu chifukwa cha Ine, kukhale umboni kwa iwo; 10ndipo uthenga ulalikidwe koyamba kwa mitundu yonse. 11Komatu pamene iwo adzakuperekani, musadandaule kuti mudzalankhula chiyani, [kapena kukonzekera chimene mudzalankhula]: komatu chilichonse chimene chidzapatsidwa kwa inu mu nthawi imeneyo, lankhulani chimenecho; pakuti inuyo siwolankhulayo, koma Mzimu Woyera. 12Koma m’bale adzapereka m’bale wake ku imfa. 13Ndipo adzakudani anthu onse chifukwa cha dzina langa; komatu iye wakupilira kufika kumapeto, adzapulumuka.

14Koma mudzaona choipa chopululutsa chikuyima pamene sichikuyenera kuyima, (iye amene amawerenga alingalire [ichi],) pamenepo iwo amene ali mu Yudea athawire ku mapiri; 15ndipo iye amene ali pamwamba pa nyumba asatsikire m’nyumba, kapena kulowa [mkati mwake] ndi kutulutsa kalikonse m’nyumba mwakemo; 16ndipo iye amene ali kumunda asabwerere kukatenga malaya ake. 17Komatu tsoka kwa iwo akukhala ndi ana ndi iwo amene akuyamwitsa masiku amenewo! 18Ndipo mupemphere kuti isadzakhale nyengo yozizira; 19pakuti masiku amenewo kudzakhala chisautso chimene sichinaonekepo chiyambire cha chilengedwe chimene Mulungu1 anachilenga, kufikira tsopano, ndipo sichidzangalakonso chotere; 20ndipo ngati Ambuye akanapanda kufupikitsa masiku amenewo, palibe thupi limene likanapulumuka; komatu chifukwa cha osankhikawo amene Iye anawasankha, anawafupikitsa masiku amenewo. 21Ndipo pamenepo ngati wina anena kwa inu, Onani, pano [pali] Khristu, kapena onani uko, musakhulupilire [ichi]. 22Pakuti a Khristu abodza ndi aneneri abodza adzauka, ndipo adzaonetsa zizindikiro ndi zodabwitsa kunyenga anthu, ngati nkutheka, ngakhale iwo osankhikawo. 23Komatu inu ziyang’anireni: Taonani, ndakuuziranitu zinthu izi zisanachitike. 24Koma m’masiku amenewo, pakutha pa chisautso, dzuwa lidzadetsedwa ndipo mwezi suzapereka kuwala kwake; 25ndipo nyenyezi za kumwamba zidzagwa pansi, ndipo mphamvu zimene zili m’miyamba zidzagwedezeka; 26ndipo pamenepo iwo adzaona Mwana wa munthu akubwera m’mitambo ndi mphamvu yaikulu ndi ulemelero; 27ndipo pamenepo Iye adzatuma angelo ake ndipo adzasonkhanitsa pamodzi osankhika ake ku mphepo zinayi, kuchokera ku malekezero a dziko lapansi kufikira kumalekezero a kumwamba.

28Koma phunzirani ku mtengo wa mkuyu: pamene nthambi yake ikhala ya nthete ndi kutulutsa masamba, mumadziwa kuti dzinja lawandikira. 29Chomwechonso inu, pamene muona zinthu zimenezi zikuchitika, dziwani kuti tsikuli lawandikira, lili pa makomo. 30Ndithudi ndinena kwa inu, m’badwo uwu sudzapita, kufikira zonse izi zitachitika. 31Kumwamba ndi dziko lapansi zidzapita, koma mau anga sadzapita. 32Komatu za ola limeneli palibe amene amadziwa, ngakhale angelo amene ali kumwamba, kapena Mwana, koma Atate. 33Yang’anirani, ndi kupemphera, pakuti simudziwa nthawi yake: 34 [zili ngati] munthu amene watuluka m’dziko lake, nasiya nyumba yake napereka ulamuliro kwa akapolo ake, ndipo kwa wina aliyense ntchito yake, ndi kulamulira wa pakhomo kuti ayang’anire. 35Chomwecho yang’anirani, pakuti simudziwa pamene mbuye wa nyumba afika: madzulo, kapena pakati pa usiku kapena m’bandakucha pakulira kwa tambala, kapena m’mamawa; 36kuti pakubwera mwadzidzidzi angadzakupezeni inu mukugona. 37Koma chimene ndinena kwa inu, ndinenanso kwa onse, Yang’anirani.

1Elohimu