Mutu 16
1Ndipo Iye anatinso kwa ophunzira [ake], Panali munthu wina wolemera amene anali ndi kapitawo wake, ndipo iye ananenezedwa kuti amaononga katundu wa mbuye wake. 2Ndipo atamuyitana, anati kwa iye, Chiyani [ichi] chimene ndikumva cha iwe? Uziwerengere za ukapitawo wako, pakuti sukuyeneranso kukhala kapitawo. 3Ndipo kapitawo anati mwa iye yekha, Ndidzatani; pakuti mbuye wanga akuchotsa ukapitawo wanga? Ine sindingakwanitse kulima; ndili ndi manyazi kupemphapempha. 4Ine ndadziwa chimene ndidzachita, kuti pamene ndidzachotsedwa ukapitawo wanga ndikalandiridwe mnyumba zawo. 5Ndipo anaziyitanira kwa iye yekha aliyense amene anali ndi ngongole ndi mbuye wake, nati kwa woyambayo, kodi uli ndi ngongole yochuluka bwanji ndi mbuye wanga? 6Ndipo iye anati, mitsuko zana limodzi ya mafuta. Ndipo anati kwa iye, Tenga cholembera chako ndi kukhala pansi mwachangu ndipo ulembe makumi asanu. 7Pamenepo anati kwa wina, Nanga iwe, uli ndi ngongole yochuluka bwanji? Ndipo iye anati, Mitanga zana limodzi ya tirigu. Ndipo anati kwa iye, Tenga cholembera chako ndipo ulembe makumi asanu ndi atatu. 8Ndipo mbuyeyo anamuyamikira kapitawo wosalungamayo kuti anachita mwa nzeru. Pakuti ana a pansi pano mwa m’badwo wawo ali ochenjera kuposa ana a kuwala. 9Ndipo ndinena kwa inu, Zipangireni nokha abwenzi ndi chuma chosalungama, kuti pamene zikakuvutani inu akakulandireni m’mahema amuyaya. 10Iye amene akhulupirika pa zinthu zochepa alinso wokhulupirika pa zinthu zambiri. 11Ngati sunakhale wokhulupirika mu chuma chosalungama, ndani amene adzakhulupilira iwe mu choonadi? 12ndipo ngati sunakhulupirike mu cha wina, ndani amene adzakupatsa iwe chako chako? 13Palibe kapolo amene adzatumikira ambuye awiri, pakuti mwina azada wina ndi kukonda winayo, kapena mwina azakangamira kwa wina ndi kunyazitsa winayo. Simungathe kutumikira Mulungu1 ndi chuma.
14Ndipo Afarisinso, amene anali okonda chuma, anamva zinthu zonse izi, ndipo anam’nyodola Iye. 15Ndipo Iye anati kwa iwo, Ndinu amene mumazilungamitsa nokha pamaso pa anthu, koma Mulungu2 amadziwa mitima yanu; pakuti chimene chimaganizidwa kwambiri pakati pa anthu ndi choipa pamaso pa Mulungu3. 16Chilamulo ndi aneneri zinalipo kuyambira nthawi ya Yohane: kuyambira nthawi imeneyo uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu4 unalalikidwa, ndipo aliyense anazikakamiza m’menemo. 17Komatu ndi kosavuta kuti kumwamba ndi dziko lapansi zipite koposa limodzi la kalembo kachilamulo kalephere. 18Aliyense amene achotsa mkazi wake ndi kukwatira wina achita chigololo; ndipo aliyense amene akwatira iye wochotsedwa ndi mwamunayo achitanso chigololo.
19Tsopano panali munthu wolemera amene amavala chibakuwa ndi nsalu ya bafuta, amadya ndi kusangalala tsiku ndi tsiku. 20Ndipo [panali] munthu wosauka, dzina lake Lazaro, [amene] anayikidwa pa chipata chake wodzala ndi zilonda, 21ndipo analakalaka kukhuta ndi nyenyetswa zakugwa pa gome la munthu wolemera; koma agalunso anabwera kuzanyambita zilonda zake. 22Ndipo kunachitika kuti munthu wosauka uja anamwalira, ndipo ananyamulidwa ndi angelo kupita m’chifuwa cha Abrahamu. Ndipo munthu wolemeranso anamwalira ndipo anayikidwa m’manda. 23Ndipo mu hade pokweza maso ake, pozunzika, anaona Abrahamu patali, ndi Lazaro m’chifuwa chake. 24Ndipo iye pofuula anati, Atate Abrahamu, ndimvereni chifundo ine, ndipo tumizani Lazaro kuti aviike nsonga ya chala chake m’madzi ndi kuziziritsa lilime langa, pakuti ndikuzunzika mu lawi la moto ili. 25Koma Abrahamu anati, Mwana wanga, kumbukira kuti iwe unalandiliratu zinthu zabwino m’moyo mwako, ndi chimodzimodzinso Lazalo zinthu zoipa. Komatu tsopano akutonthozedwa kuno, ndipo iwe ukuzunzika. 26Ndipo pambali pa zonsezi, pakati pa ife ndi iwe pali phompho loyikika, kotero kuti iwo ofuna kudutsa kupita kwa iwe sangakwanitse, kapena iwo [ofuna kuwoloka] kuchoka kumeneko kubwera kwa ife. 27Ndipo iye anati, Ndikupemphani, Atate, kuti mumutumize kunyumba kwa atate wanga, 28pakuti ndili nawo abale anga asanu, kuti iye akawachitire umboni iwo, kuti asabwere kumalo ano a mazunzo. 29Koma Abrahamu anati kwa iye, Iwo ali naye Mose ndi aneneri: alekeni awamvere iwo. 30Koma iye anati, Iyayi, atate Abrahamu, koma ngati wina wa akufa apita kwa iwo, azatembenuka mtima. 31Ndipo anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, ngakhale atadzuka munthu kwa akufa sadzakopeka mtima.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu