Mutu 23
1Ndipo Paulo, popenyetsetsa maso ake pa akulu a bwalo, anati, Abale, Ine ndayenda m’chikumbumtima chonse chabwino ndi Mulungu1 kufikira lero. 2Koma mkulu wa ansembe Hananiya analamulira iwo amene anayimilira pafupi naye kuti am’menye pakamwa pake. 3Pamenepo Paulo anati kwa iye, Mulungu2 adzakukantha, chipupa choyeretsedwa iwe. Ndipo iwe, ukhala wakundiweruza ine molingana ndi lamulo, ndipo pophwanya lamulo ulamulira kuti ine ndimenyedwe? 4Ndipo iwo akuyimilira pamenepo anati, Kodi ukulalatira mkulu wa ansembe wa Mulungu3? 5Ndipo Paulo anati, Sindinadziwe, abale, kuti anali mkulu wa ansembe; pakuti kunalembedwa, Usalankhule koipa za olamulira a anthu ako. 6Koma Paulo, podziwa kuti ena [mwa iwo] anali a Asaduki ndi ena a Afarisi, anafuula m’bwalomo, Abale inu, ana a Afarisi: Ine ndikuweruzidwa zokhudza chiyembekezo ndi kuuka kwa akufa. 7Ndipo pamene iye analankhula izi, panali kutsutsana pakati pa Afarisi ndi Asaduki, ndipo khamulo linagawanika. 8Pakuti Asaduki amati palibe kuuka kwa akufa, kapena angelo, kapena mzimu; koma Afarisi amakhulupilira izi zonse. 9Ndipo pamenepo panabuka chipolowe chachikulu, ndipo alembi ena a kwa Afarisi anayimilira nati, Sitikupeza cholakwika pa munthu uyu; ndipo ngati mzimu walankhula kwa iye, kapena mngelo walankhula naye? 10Ndipo chipolowe chachikulu chinabuka, kapitao wamkulu, poopa kuti Paulo akhoza kukhadzulidwa ndi iwo, analamulira asilikali atsike kudzamtenga mokakamiza pakati pawo, ndipo anam’bweretsa [iye] m’linga. 11Koma usiku wotsatirawo Ambuye anayima pambali pake, ndipo anati, Limba mtima; pakuti monga wachitira umboni zinthu zokhudza Ine ku Yerusalemu, chomwecho uchitirenso umboni ku Roma. 12Ndipo pamene kunacha, Ayuda, atakumana pamodzi, anadziyika okha pansi pa lumbilo, nanena kuti siadya kapena kumwa kufikira atamupha Paulo. 13Ndipo iwo analipo anthu oposa makumi anayi amene anagwirizana pamodzi mu lumbiro limeneli; 14ndipo iwo anapita kwa akulu ansembe ndi akulu, ndipo anati, Tadziyika tokha mu lumbiro la themberero kuti sitilawa kanthu kufikira titamupha Paulo. 15Tsopano pamenepo inu pamodzi ndi abwalo mudziwitse kapitao wamkulu kuti amubweretse kwa inu, monga kuti mufuna kufufuza bwino zokhudza iye, ndipo ife, pamene iye adzawandikira, tidzakhala okonzeka kumupha. 16Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo, pamene anamva za chiwembu ichi, anabwera nalowa m’linga ndi kumuuza Paulo. 17Ndipo Paulo anayitana m’modzi wa a kenturiyo, nanena, Tamutengere mnyamata uyu kwa kapitao wamkulu, pakuti ali ndi kanthu kakuti am’dziwitse iye. 18Pamenepo iye anamutengera kwa kapitao wamkuluyo, ndipo anati, Wandende Paulo anandiyitana ndipo anandipempha kuti ndim’bweretse mnyamata uyu kwa inu, amene ali ndi kena kake kakuti akuuzeni. 19Ndipo kapitao wamkulu pamene anam’gwira padzanja, anapita pambali pa awiri, namfunsa, Kodi ndi chiyani chimene ukufuna kundiuza? 20Ndipo iye anati, Ayuda agwirizana kuti akupempheni, kuti mum’bweretse Paulo m’mawa pamaso pa bwalo, monga kufuna kukamufunsa bwino zokhudza iyeyo. 21Musakopeke nawo, pakuti amlalira iye amuna oposa makumi anayi, amene aziyika okha pansi pa lumbiro la themberero kuti siadya kapena kumwa kufikira atamupha iye; ndipo tsopano iwo akudikilira lonjezanoli kuchokera kwa inu. 22Kapitao wamkulu anamlola mnyamatayo apite, namlamulira [iye, asauze wina aliyense kuti wamuuza iye zinthu izi. 23Ndipo pamene anayitanitsa awiri mwa akenturiyo, anati, Konzekeretsani asilikali mazana awiri kuti apite mpaka ku Kaisareya, komanso okwera ngamira makumi asanu ndi awiri, ndi oyenda pansi okhala ndi zida zopepuka mazana awiri, anyamuke ola lachitatu la usiku. 24Ndipo [iye anawalamulira iwo] apereke nyama zonyamula katundu, kuti Paulo akwerepo ndi kum’nyamula [iye] motetezeka kupita kwa Filipo kazembeyo, 25anamlembera kalata, yotere: 26Klaudiyo Lusiya kwa kazembe wolemekezeka Felike, ndikulonjerani. 27Munthu uyu, pamene anatengedwa ndi Ayuda, ndipo atatsala pang’ono kumupha, ine ndinadza pamodzi ndi asilikali ndipo tinamlanditsa [m’manja mwao], ndipo tinazindikira kuti ndi m’Roma. 28Ndipo tinafunitsitsa kudziwa mlandu umene akumutsutsa nawo, ndinam’bweretsa iye ku bwalo lawo; 29pamenepo ndinapeza kuti amatsutsidwa pa nkhani yokhudza chilamulo, koma sanapezeke ndi mlandu woti aphedwe kapena kumangidwa. 30Koma pamene ndalandira uthenga wa chiwembu kuti munthu ameneyu aphedwe [ndi Ayuda], ine ndamtumiza mwachangu kwa inu, ndawalamuliranso omneneza mlandu kuti anene kanthu kwa inu zinthu zimene akum’nenezazo. [Zabwino zonse.] 31Pamenepo asilikali, molingana ndi zimene analamulidwa, anamtenga Paulo nam’bweretsa kwa Antipatri usiku, 32ndipo m’mawa mwake, anawasiya a pakavalo kuti apite naye, nabwerera ku linga. 33Ndipo awa, pamene analowa m’Kaisareya, ndi kupereka kalatayo kwa kazembe, anamperekanso Paulo kwa iye. 34Ndipo atawerenga [kalatayo], ndi kumufunsa dziko limene iye amachokera, ndipo anadziwa kuti ndi waku Kilikiya, 35anati, Ndidzakumva iwe kwathunthu akabwera amene akukutsutsa mlandu. Ndipo iye analamulira kuti asungidwe mnyumba ya milandu ya Herode.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu