Mutu 6

1Komatu [monga] antchito amzanu, tikupemphaninso kuti musalandire chisomo cha 1Mulungu pachabe: 2(pakuti Iye anena, Ndinamvera iwe mu nthawi yovomerezeka, ndipo ndakuthandiza iwe mu tsiku la chipulumutso: taonani, tsopano ino ndi nthawi yovomerezeka; taonani, tsopano ino ndi nthawi ya chipulumutso:) 3osapereka chokhumudwitsa chilichonse mwanjira ina iliyonse, kuti utumiki usanyozeke; 4koma mu zonse kudzipereka tokha monga atumiki a 2Mulungu, m’kupilira kwakukulu, m’masautso, m’zosoweka, mzikakamizo, 5m’mikwingwirima, m’ndende, m’ziwawa, m’zivutiko, m’kudikira, m’kusala kudya, 6m’chiyero, m’chidziwitso, m’chipiliro, m’chifundo, mwa Mzimu Woyera, m’chikondi chosanyenga, 7m’mau a choonadi, mu mphamvu ya 3Mulungu; kudzera m’zopereka za chifundo za chilungamo ku lamanja ndi lamanzere, 8kudzera mu ulemelero ndi mu mnyozo, kudzera mu mbiri yoipa ndi mbiri yabwino: monga achinyengo, ndi owoona; 9monga osadziwika, ndi odziwika bwino; monga akufa, ndipo taonani, ife tikhala ndi moyo; monga olangidwa, ndipo osati ophedwa; 10monga akumva chisoni, koma nthawi zonse okondwera; monga osauka, koma olemeretsa ambiri; monga opanda kanthu, ndipo okhala nazo zinthu zonse.

11Kamwa lathu latsegukira inu, Akorinto, mtima wathu wakulitsidwa. 12Inuyo simunapsinjike mwa ife, koma mwapsinjika chifukwa cha zokhumba zanu; 13koma m’kuyankha kobwezera, (ndilankhula monga kwa ana,) Lolani mtima wanu ukulitsidwe wokha.

14Musakhale omangidwa m’goli pamodzi ndi osakhulupilira; pakuti pali ubale wanji pakati pa kulungama ndi kusalungama? Kapena pali chiyanjano chanji pakati pa kuwala ndi mdima? 15ndipo pali kulumikizana kotani pakati pa Khristu ndi Beliyali, kapena pali gawo lotani pakati pa wokhulupilira ndi wosakhulupilira? 16ndipo pali kumvana kwanji pakati pa kachisi wa 4Mulungu ndi wa mafano? pakuti inu ndinu kachisi wa moyo wa 5Mulungu; molingana ndi momwe 6Mulungu analankhulira, Ine ndidzakhala pakati pawo, ndipo ndidzayenda pakati pawo; ndipo ndidzakhala 7Mulungu, wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga. 17Pamenepo chokani pakati pawo, ndipo zipatuleni, atero Ambuye, ndipo musakhudze chimene chili chodetsedwa, ndipo Ine ndidzakulandirani inu; 18ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndipo inu mudzakhala kwa Ine ana amuna ndi ana akazi, atero Ambuye Wamphamvuyonse.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu