Mutu 1
1Vumbulutso la Yesu Khristu, limene Mulungu1 analipereka kwa iye, kuonetsera kwa akapolo ake zimene zikuyenera kuchitika posachedwapa; ndipo iye anatanthauzira zimenezi, potumiza kudzera mwa mngelo wake, kupita kwa kapolo wake Yohane, 2amene anachitira umboni mau a Mulungu2, ndi umboni wa Yesu Khristu, zinthu zonse zimene iye anaziona. 3Wodala [ali] iye amene awerenga, ndi iwo amene amva mau a uneneri, ndi kusunga zinthu zolembedwa m’menemo; pakuti nthawi yawandikira.
4Yohane kwa mipingo isanu ndi iwiri imene ili m’Asiya: Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa [iye] amene ali, adali, ndi amene ali mkudza; ndi kwa Mizimu isanu ndi iwiri yokhala pa mpando wa chifumu wake; 5ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, woyamba kubadwa pakati pa akufa, ndi kalonga wa mafumu a dziko lapansi. Kwa iye amene atikonda ife, ndipo watisambitsa kuchoka ku machimo athu m’mwazi wake, 6natipanga ife ufumu, ansembe kwa Mulungu3 wake ndi Atate: kwa iye [kukhale] ulemelero ndi mphamvu ku nthawi za nthawi. Amen.
7Taonani, iye adza ndi mitambo, ndipo diso lililonse lidzamuona iye, ndi iwo amene anam’baya, ndi mafuko onse a padziko adzalira chifukwa cha iye. Indedi. Amen.
8Ndine Alefa ndi Omega, atero Ambuye Mulungu4, iye amene ali, ndipo anali, ndi iye amene ali nkudza, Wamphamvu yonse.
9Ine Yohane, m’bale wanu ndi woyanjana nanu m’chisautso ndi ufumu ndi chipiliro, mwa Yesu, ndinali m’chisumbu chotchedwa Patmo, chifukwa cha mau a Mulungu5, ndi chifukwa cha umboni wa Yesu. 10Ndinali mu Mzimu patsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau akulu monga a lipenga, 11nanena, Zimene waona ulembe m’buku, ndipo utumize ku mipingo isanu ndi iwiri: ku Efeso, ndi ku Smurna, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiyatira, ndi ku Sarde, ndi ku Filadelfiya, ndi ku Laodikaya.
12Ndipo ndinatembenuka kuti ndione wakunena mau amene analankhulidwa ndi ine; ndipo nditatembenuka, ndinaona nyali za golide zisanu ndi ziwiri, 13ndipo pakati pa nyali zisanu ndi ziwirizo ndinaona wina onga Mwana wa munthu, wovala chovala chofikira kumapazi, namangira lamba wa golide pa chifuwa pake: 14mutu wake wokhala ndi tsitsi loyera ngati ubweya woyera, monga chipale chofewa; ndi maso ake ngati lawi la moto; 15ndipo mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira, monga woyengeka mng’anjo; ndi mau ake ngati mkokomo wa madzi ochuluka; 16ndipo mdzanja lake lamanja muli nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndipo mkamwa mwake munatuluka lupanga lakuthwa konsekonse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake.
17Ndipo pamene ndinamuona ndinagwa pamapazi pake ngati wakufa; ndipo anayika dzanja lake lamanja pa ine, nanena, Usaope; Ndine woyamba ndi wotsiriza, 18ndi wamoyoyo: ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndili nawo moyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndili nazo zifungulo za imfa ndi hade. 19Lemba pamenepo zimene waona, ndi zinthu zimene zili, ndi zinthu zimene zikuyenera kukhalapo mtsogolo zitapita izi. 20Chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene waona kudzanja langa lamanja, ndi nyali zisanu ndi ziwiri za golide. — Nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndiwo angelo a mipingo isanu ndi iwiri; ndipo nyali zisanu ndi ziwiri ndiyo mipingo isanu ndi iwiri.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu