Mutu 8

1Ndipo pamene anamasula chizindikiro cha chisanu ndi chiwiri, munali chete m’mwamba kwa ola ndi theka. 2Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri amene anaima pamaso pa Mulungu1, ndipo malipenga asanu ndi awiri anaperekedwa kwa iwo. 3Ndipo mngelo wina anadza nayima pa guwa, atanyamula chofukiza cha golide; ndipo zofukiza zambiri zinaperekedwa kwa iye, kuti akapereke [mphamvu] ku mapemphero a oyera mtima onse pa guwa la golide limene linali pa mpando wachifumu. 4Ndipo utsi wa chofukiza unakwera pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima, kuchoka mdzanja la mngelo pamaso pa Mulungu2. 5Ndipo mngelo anatenga chofukiza, nachizaza pa moto wa paguwa, ndipo anachiwaza padziko lapansi: ndipo panali mau, ndi mabingu ndi mphenzi, ndi chivomezi.

6Ndipo angelo asanu ndi awiri amene anali ndi malipenga asanu ndi awiri anazikonzekeretsa okha kuti akaombe malipenga awo.

7Ndipo woyamba anaomba lipenga [lake]: ndipo panali matalala ndi moto, zosakanikirana ndi mwazi, ndipo zinaponyedwa padziko lapansi; ndipo gawo lachitatu la dziko lapansi linatenthedwa, ndipo gawo lachitatu la mitengo linatenthedwa, ndipo udzu onse obiriwira unatenthedwa.

8Ndipo mngelo wachiwiri anaomba lipenga [lake]: ndipo monga phiri lalikulu loyaka moto linaponyedwa mnyanja, ndipo gawo lachitatu la nyanja linasanduka mwazi; 9ndipo gawo lachitatu la zolengedwa limene linali mnyanja limene linali ndi moyo linafa; ndipo gawo lachitatu la zombo linaonongeka.

10Ndipo mngelo wachitatu anaomba lipenga [lake]: ndipo inagwa kuchoka kumwamba nyenyezi yayikulu, yoyaka ngati muuni, ndipo inagwera pa gawo lachitatu la mitsinje, ndi pa akasupe a madzi. 11Ndipo dzina la nyenyeziyo ndilo Chitsamba chowawa; ndipo gawo lachitatu la madzi linasanduka chitsamba chowawa, ndipo anthu ochuluka anafa ndi madziwo chifukwa anasanduka owawa.

12Ndipo mngelo wachinayi anaomba lipenga [lake]: ndipo gawo lachitatu la dzuwa linaphwanyidwa, ndi gawo lachitatu la mwezi, ndi gawo lachitatu la nyenyezi; cholinga kuti gawo lawo lachitatu likadetsedwe, ndi kuti tsikulo lisawale pa gawo lake lachitatu, ndiponso chimodzimodzi usiku.

13 Ndipo ndinaona, ndikumva nkhwazi ikuwuluka mlengelenga, ikulankhula ndi mau okweza, Tsoka, tsoka, tsoka, kwa iwo okhala padziko lapansi, pa mau otsalira a lipenga la angelo atatu limene lifuna kuombedwa.

1Elohimu2Elohimu