Mutu 4

1Okondedwa, musakhulupilire mzimu uliwonse, koma muyese mizimu, ngati ndi ya Mulungu1; chifukwa aneneri ambiri onyenga anatuluka m’dziko lapansi. 2M’menemo inu mudziwa Mzimu wa Mulungu2: mzimu uliwonse umene uvomereza Yesu Khristu anadza mthupi ndi wa Mulungu3; 3ndipo mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu Khristu anadza mthupi suli wa Mulungu4: ndipo imeneyi ndi [mphamvu] ya wokana Khristu, amene inu munamva kuti akubwera, ndipo tsopano wafika kale m’dziko lapansi. 4Inu muli ana a Mulungu5, ndipo mwawalaka iwo, chifukwa wamkulu ali iye amene ali mwa inu kuposa amene ali m’dziko lapansi. 5Iwo ali a dziko lapansi; pachifukwa chimenechi amalankhula ngati adziko lapansi, ndipo dziko lapansi limawamvera iwo. 6Ife tili a Mulungu6; iye amene adziwa Mulungu7 atimvera ife; iye amene sali wa Mulungu8 satimvera ife. Kuchokera m’menemu ife tidziwa mzimu wa choonadi ndi mzimu wosocheretsa.

7Okondedwa, tiyeni tikondane wina ndi mzake; chifukwa chikondi ndi Mulungu9, ndipo aliyense wokonda anabadwa mwa Mulungu10, ndipo amdziwa Mulungu11. 8Iye amene sakonda sanamdziwe Mulungu12; pakuti Mulungu13 ndi chikondi. 9Umo monga kwa ife chaonekera chikondi cha Mulungu14, kuti Mulungu15 anatumiza Mwana wake wokondedwa m’dziko lapansi, kuti tikakhale mwa iye. 10umo pali chikondi, osati kuti ife tinamkonda Mulungu16, koma kuti iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake nsembe ya chitetezo pa machimo athu.

11Okondeka, ngati Mulungu17 watikonda ife kotero, tikuyeneranso kukondana wina ndi mzake. 12Palibe munthu amene anaona Mulungu18 nthawi ina iliyonse: ngati tikondana wina ndi mzake, Mulungu19 akhala mwa ife, ndipo chikondi chake chatheka mwa ife. 13M’menemo ife tidziwa kuti tikhala mwa iye ndi iye mwa ife, kuti anatipatsako Mzimu wake. 14Ndipo ife taona, ndi kuchitira umboni, kuti Atate watumiza Mwana [monga] Mpulumutsi wadziko lapansi.

15Aliyense amene avomereza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu20, Mulungu21 akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu22. 16Ndipo ife tadziwa ndi kukhulupilira chikondi chimene Mulungu23 ali nacho kwa ife. Mulungu24 ndi chikondi, ndipo amene akhala m’chikondi akhala mwa Mulungu25, ndi Mulungu26 akhala mwa iye. 17M’menemo chikondi chake chatheka ndi ife kuti tikhale nako kulimbika m’tsiku la chiweruzo, monga iye ali, ifenso tili m’dziko lapansili. 18Palibe mantha m’chikondi, koma chikondi changwiro chimachotsa mantha; pakuti mantha amazunza, ndipo iye amene achita mantha sanakhale wangwiro m’chikondi. 19Ife timakonda chifukwa iye anatikonda poyamba.

20Ngati aliyense anena, Ndikonda Mulungu27, ndipo adana naye m’bale wake, ndi wabodza: pakuti iye amene sakonda m’bale wake amene amuona, adzakonda bwanji Mulungu28 amene sanamuone? 21Ndipo lamulo ili tili nalo kuchokera kwa iye, Kuti iye amene akonda Mulungu29 akondanso m’bale wake.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu12Elohimu13Elohimu14Elohimu15Elohimu16Elohimu17Elohimu18Elohimu19Elohimu20Elohimu21Elohimu22Elohimu23Elohimu24Elohimu25Elohimu26Elohimu27Elohimu28Elohimu29Elohimu