Mutu 16

1Koma ine ndikumpereka Febe, mlongo wathu, amene ali mtumiki mu mpingo umene uli mu Kenkreya; 2kuti mumlandire iye mwa Ambuye moyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize iye mu chinthu chilichonse chosoweka chimene angafune kwa inu; pakutinso iye wakhala thandizo kwa anthu ambiri, komanso kwa ine ndemwe. 3Mupereke malonje kwa Prisila ndi Akwila, amene ndi atumiki amzanga mwa Khristu Yesu, 4(amene chifukwa cha moyo wanga anapereka khosi lawo; kwa iwowa sindikungoyamika ine ndekha, komanso mipingo yonse ya kwa amitundu,) 5ndi mpingo wa mnyumba mwao. Mupereke malonje kwa Epeneto, wokondedwa wanga, amene ndi zipatso zoyambilira za ku Asiya za Khristu. 6Malonje kwa Mariya, amene anakugwilirani inu ntchito zambiri. 7Malonje kwa Androniko ndi Yuniya, abale anga, komanso andende amzanga, amene ali odziwika pakati pa atumwi; amene analinso mwa Khristu ine ndisanakhale. 8Malonje kwa Ampliato, wokondedwa wanga mwa Ambuye. 9Malonje kwa Urbano, mtumiki mzathu mwa Khristu, ndi Staku, wokondedwa wanga. 10Malonje kwa Apele, wovomerezeka mwa Khristu. Malonje kwa iwo a m’banja la Aristobulo. 11Malonje kwa Herodiona, m’bale wanga. Muwapatse malonje iwo amene akupezeka m’banja la Narkiso, amene ali mwa Ambuye. 12Malonje kwa Trufena ndi Trufosa, amene anagwiritsa ntchito mwa Ambuye. Malonje kwa Persida, wokondedwayo, amene anagwiritsa ntchito kwambiri mwa Ambuye. 13Malonje kwa Rufo, wosankhika mwa Ambuye; ndi kwa mayi wake amenenso ali mayi wanga. 14Malonje kwa Asunkrito, Felego, Herme, Patroba, Herma, ndi abale amene ali pamodzi ndi iwo. 15Malonje kwa Filologo, ndi Yuliya, Nereya, ndi mlongo wake, ndi Olimpa, ndi oyera mtima onse amene ali ndi iwo. 16Mupatsane malonje wina ndi mzake ndi chipsopsono choyera. Mipingo yonse ya Khristu ikukulonjerani. 17Koma ndikukupemphani, abale, musamale ndi iwo obweretsa magawano ndi zopunthwitsa, zosemphana ndi chiphunzitso chimene inu mwaphunzira, ndipo muwapewe iwo. 18Pakuti otere satumikira Ambuye Khristu, koma mimba zawo, ndipo ndi mau okoma ndi oshashalika amapusitsa mitima ya anthu osalakwa. 19Pakuti kumvera kwanu kunafikira onse. Pamenepo ine ndimasangalala chifukwa cha inu; koma ndikufunisitsa kuti inu mukhale a nzeru ku chimene chili chabwino, ndi wosatengeka ku choipa. 20Koma Mulungu1 wa mtendere adzamphwanya Satana pansi pa mapazi anu posachedwapa. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu.

21Timoteyo, mtumiki mzanga, ndi Lusiyo, ndi Yasoni, ndi Sosipatro, abale anga, akukulonjerani.

22Ineyo Tertiyo, amene ndalemba kalatayi, ndikulonjerani inu mwa Ambuye. 23Gayo, amene wandisunga ine mnyumba mwake pamodzi ndi mpingo onse, akukulonjerani. Erasto, woyang’anira mzindawu, akukulonjerani, pamodzi ndi m’bale Kwarto. 24Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. Amen.

25Tsopano kwa Iye amene ali ndi kuthekera kokukhazikitsani inu, molingana ndi uthenga wanga wabwino ndi kulalikira kwa Yesu Khristu, molingana ndi vumbulutso la chinsinsi, monga chinasungidwa chinsinsi kwa nthawi yaitali, 26koma tsopano chavumbulutsidwa, ndi malemba a uneneri, molingana ndi lamulo la Mulungu2 wamuyaya, zadziwitsidwa pa chikhulupiliro cha kumvera kwa mitundu yonse — 27Mulungu3 yekhayo wa nzeru, mwa Yesu Khristu, kwa Iye ukhale ulemelero nthawi zonse. Amen.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu